Psalms 138 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.” 2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyerandipo ndidzayamika dzina lanuchifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anukupambana zinthu zonse. 3 Pamene ndinayitana, munandiyankha;munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima. 4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,pamene amva mawu a pakamwa panu. 5 Iwo ayimbe za njira za Yehova,pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu. 6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,koma anthu onyada amawadziwira chapatali. 7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,mumasunga moyo wanga;mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja. 8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosathamusasiye ntchito ya manja anu.