Psalms 15 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? 2 Munthu wa makhalidwe abwino,amene amachita zolungama,woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake, 3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,amene sachitira choyipa mnansi wakekapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake, 4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,amene amakwaniritsa zomwe walonjezangakhale pamene zikumupweteka, 5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanjandipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezisadzagwedezeka konse.