Psalms 29 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu. 2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake. 3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;Mulungu waulemerero abangula,Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu. 4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;liwu la Yehova ndi laulemerero. 5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni. 6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,Siriyoni ngati mwana wa njati: 7 Liwu la Yehova limakanthangati kungʼanima kwa mphenzi. 8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi. 9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawandi kuyeretsa nkhalango.Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!” 10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,Yehova ndiye mfumu kwamuyaya. 11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.