Psalms 54 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.” 1 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu. 2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungumvetserani mawu a pakamwa panga. 3 Alendo akundithira nkhondo;anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,anthu amene salabadira za Mulungu. 4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine. 5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;mwa kukhulupirika kwanu awonongeni. 6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,pakuti ndi labwino. 7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.