Psalms 61 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. 1 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;mvetserani pemphero langa. 2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inundimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo. 3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,nsanja yolimba polimbana ndi adani anga. 4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyayandi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu. 5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu. 6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,zaka zake kwa mibado yochuluka. 7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze. 8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanundi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.