Psalms 70 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho. 1 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;Yehova bwerani msanga kudzandithandiza. 2 Iwo amene akufunafuna moyo wangaachititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;onse amene akukhumba chiwonongeko changaabwezedwe mopanda ulemu. 3 Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”abwerere chifukwa cha manyazi awo. 4 Koma onse amene akufunafuna Inuakondwere ndi kusangalala mwa Inu;iwo amene amakonda chipulumutso chanunthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!” 5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;Inu Yehova musachedwe.