Zechariah 1 (BOGWICC)
1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti: 2 “Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. 3 Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 4 Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova. 5 Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? 6 Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu?“Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ” 7 Tsiku la 24 la mwezi wa 11, mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido. 8 Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera. 9 Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?”Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.” 10 Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.” 11 Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.” 12 Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?” 13 Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane. 14 Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, “Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni, 15 koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.’ 16 “Choncho, Yehova akuti, ‘Ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo, nyumba yanga adzayimanganso kumeneko. Ndipo adzatenganso chingwe choyezera kuti amange Yerusalemu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 17 “Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ” 18 Kenaka ndinayangʼananso, ndipo patsogolo panga panali nyanga zinayi. 19 Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?”Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.” 20 Kenaka Yehova anandionetsa amisiri azitsulo anayi. 21 Ndinafunsa kuti, “Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?”Iye anayankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake.”
In Other Versions
Zechariah 1 in the ANGEFD
Zechariah 1 in the ANTPNG2D
Zechariah 1 in the AS21
Zechariah 1 in the BAGH
Zechariah 1 in the BBPNG
Zechariah 1 in the BBT1E
Zechariah 1 in the BDS
Zechariah 1 in the BEV
Zechariah 1 in the BHAD
Zechariah 1 in the BIB
Zechariah 1 in the BLPT
Zechariah 1 in the BNT
Zechariah 1 in the BNTABOOT
Zechariah 1 in the BNTLV
Zechariah 1 in the BOATCB
Zechariah 1 in the BOATCB2
Zechariah 1 in the BOBCV
Zechariah 1 in the BOCNT
Zechariah 1 in the BOECS
Zechariah 1 in the BOHCB
Zechariah 1 in the BOHCV
Zechariah 1 in the BOHLNT
Zechariah 1 in the BOHNTLTAL
Zechariah 1 in the BOICB
Zechariah 1 in the BOILNTAP
Zechariah 1 in the BOITCV
Zechariah 1 in the BOKCV
Zechariah 1 in the BOKCV2
Zechariah 1 in the BOKHWOG
Zechariah 1 in the BOKSSV
Zechariah 1 in the BOLCB
Zechariah 1 in the BOLCB2
Zechariah 1 in the BOMCV
Zechariah 1 in the BONAV
Zechariah 1 in the BONCB
Zechariah 1 in the BONLT
Zechariah 1 in the BONUT2
Zechariah 1 in the BOPLNT
Zechariah 1 in the BOSCB
Zechariah 1 in the BOSNC
Zechariah 1 in the BOTLNT
Zechariah 1 in the BOVCB
Zechariah 1 in the BOYCB
Zechariah 1 in the BPBB
Zechariah 1 in the BPH
Zechariah 1 in the BSB
Zechariah 1 in the CCB
Zechariah 1 in the CUV
Zechariah 1 in the CUVS
Zechariah 1 in the DBT
Zechariah 1 in the DGDNT
Zechariah 1 in the DHNT
Zechariah 1 in the DNT
Zechariah 1 in the ELBE
Zechariah 1 in the EMTV
Zechariah 1 in the ESV
Zechariah 1 in the FBV
Zechariah 1 in the FEB
Zechariah 1 in the GGMNT
Zechariah 1 in the GNT
Zechariah 1 in the HARY
Zechariah 1 in the HNT
Zechariah 1 in the IRVA
Zechariah 1 in the IRVB
Zechariah 1 in the IRVG
Zechariah 1 in the IRVH
Zechariah 1 in the IRVK
Zechariah 1 in the IRVM
Zechariah 1 in the IRVM2
Zechariah 1 in the IRVO
Zechariah 1 in the IRVP
Zechariah 1 in the IRVT
Zechariah 1 in the IRVT2
Zechariah 1 in the IRVU
Zechariah 1 in the ISVN
Zechariah 1 in the JSNT
Zechariah 1 in the KAPI
Zechariah 1 in the KBT1ETNIK
Zechariah 1 in the KBV
Zechariah 1 in the KJV
Zechariah 1 in the KNFD
Zechariah 1 in the LBA
Zechariah 1 in the LBLA
Zechariah 1 in the LNT
Zechariah 1 in the LSV
Zechariah 1 in the MAAL
Zechariah 1 in the MBV
Zechariah 1 in the MBV2
Zechariah 1 in the MHNT
Zechariah 1 in the MKNFD
Zechariah 1 in the MNG
Zechariah 1 in the MNT
Zechariah 1 in the MNT2
Zechariah 1 in the MRS1T
Zechariah 1 in the NAA
Zechariah 1 in the NASB
Zechariah 1 in the NBLA
Zechariah 1 in the NBS
Zechariah 1 in the NBVTP
Zechariah 1 in the NET2
Zechariah 1 in the NIV11
Zechariah 1 in the NNT
Zechariah 1 in the NNT2
Zechariah 1 in the NNT3
Zechariah 1 in the PDDPT
Zechariah 1 in the PFNT
Zechariah 1 in the RMNT
Zechariah 1 in the SBIAS
Zechariah 1 in the SBIBS
Zechariah 1 in the SBIBS2
Zechariah 1 in the SBICS
Zechariah 1 in the SBIDS
Zechariah 1 in the SBIGS
Zechariah 1 in the SBIHS
Zechariah 1 in the SBIIS
Zechariah 1 in the SBIIS2
Zechariah 1 in the SBIIS3
Zechariah 1 in the SBIKS
Zechariah 1 in the SBIKS2
Zechariah 1 in the SBIMS
Zechariah 1 in the SBIOS
Zechariah 1 in the SBIPS
Zechariah 1 in the SBISS
Zechariah 1 in the SBITS
Zechariah 1 in the SBITS2
Zechariah 1 in the SBITS3
Zechariah 1 in the SBITS4
Zechariah 1 in the SBIUS
Zechariah 1 in the SBIVS
Zechariah 1 in the SBT
Zechariah 1 in the SBT1E
Zechariah 1 in the SCHL
Zechariah 1 in the SNT
Zechariah 1 in the SUSU
Zechariah 1 in the SUSU2
Zechariah 1 in the SYNO
Zechariah 1 in the TBIAOTANT
Zechariah 1 in the TBT1E
Zechariah 1 in the TBT1E2
Zechariah 1 in the TFTIP
Zechariah 1 in the TFTU
Zechariah 1 in the TGNTATF3T
Zechariah 1 in the THAI
Zechariah 1 in the TNFD
Zechariah 1 in the TNT
Zechariah 1 in the TNTIK
Zechariah 1 in the TNTIL
Zechariah 1 in the TNTIN
Zechariah 1 in the TNTIP
Zechariah 1 in the TNTIZ
Zechariah 1 in the TOMA
Zechariah 1 in the TTENT
Zechariah 1 in the UBG
Zechariah 1 in the UGV
Zechariah 1 in the UGV2
Zechariah 1 in the UGV3
Zechariah 1 in the VBL
Zechariah 1 in the VDCC
Zechariah 1 in the YALU
Zechariah 1 in the YAPE
Zechariah 1 in the YBVTP
Zechariah 1 in the ZBP