1 Chronicles 22 (BOGWICC)

1 Ndipo Davide anati, “Nyumba ya Yehova Mulungu idzakhala pano, ndiponso guwa lansembe zopsereza za Israeli.” 2 Choncho Davide analamula kuti asonkhanitse alendo onse amene amakhala mu Israeli ndipo kuchokera pakati pawo anasankha amisiri a miyala kuti aseme miyala yomangira nyumba ya Mulungu. 3 Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza. 4 Iye anaperekanso mitengo yambiri ya mkungudza, yosawerengeka, pakuti anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo anabweretsa yambiri kwa Davide. 5 Davide anati, “Mwana wanga Solomoni ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Koma nyumba yomwe timangire Yehova iyenera kukhala yaulemerero, yotchuka ndi yokongola pamaso pa anthu a mitundu yonse. Choncho ndikonzekeratu zambiri.” Motero Davide anayikonzekera kwambiri asanamwalire. 6 Tsono iye anayitana Solomoni mwana wake ndipo anamulamula kuti adzamangire nyumba Yehova Mulungu wa Israeli. 7 Davide anati kwa Solomoni, “Mwana wanga, ine ndinali ndi maganizo oti ndimangire nyumba Dzina la Yehova Mulungu wanga. 8 Koma Yehova anandiyankhula kuti, ‘Iwe wapha anthu ambiri ndiponso wachita nkhondo zambiri. Sumangira dzina langa nyumba chifukwa wapha anthu ambiri pa dziko lapansi pamaso panga. 9 Koma udzabala mwana wamwamuna amene adzakhala munthu wamtendere ndi wabata ndipo ndidzamupatsa mpumulo kuchokera kwa adani ake onse a mbali zonse. Dzina lake adzatchedwa Solomoni ndipo Ine ndidzapereka mtendere ndi bata kwa Israeli pa nthawi ya ulamuliro wake. 10 Iye ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu mʼdziko la Israeli mpaka muyaya.’ ” 11 “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo upambane ndi kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga momwe Iye ananenera kuti udzatero. 12 Yehova akupatse nzeru ndi kumvetsetsa pamene Iye adzakuyika kukhala wolamulira Israeli, kuti udzasunge malamulo a Yehova Mulungu wako. 13 Ndipo udzapambana ngati udzamvera mosamala malangizo ndi malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kudzera mwa Mose. Khala wamphamvu ndi wolimba mtima. Usachite mantha kapena kutaya mtima. 14 “Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi. 15 Iwe uli ndi antchito ambiri: osema miyala, amisiri a miyala, ndi amisiri a matabwa, komanso anthu ambiri aluso la ntchito zosiyanasiyana, 16 zagolide ndi zasiliva, zamkuwa, zazitsulo, amisiri osawerengeka. Tsopano yamba ntchito, ndipo Yehova akhale nawe.” 17 Tsono Davide analamula atsogoleri onse a Israeli kuti athandize Solomoni mwana wake. 18 Iye anawawuza kuti, “Kodi Yehova Mulungu, sali nanu? Ndipo Iye siwakupatsani mpumulo mbali zonse? Pakuti Iyeyo wapereka eni nthaka kwa inu ndipo dziko lili pa ulamuliro wa Yehova ndi anthu ake. 19 Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.”

In Other Versions

1 Chronicles 22 in the ANGEFD

1 Chronicles 22 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 22 in the AS21

1 Chronicles 22 in the BAGH

1 Chronicles 22 in the BBPNG

1 Chronicles 22 in the BBT1E

1 Chronicles 22 in the BDS

1 Chronicles 22 in the BEV

1 Chronicles 22 in the BHAD

1 Chronicles 22 in the BIB

1 Chronicles 22 in the BLPT

1 Chronicles 22 in the BNT

1 Chronicles 22 in the BNTABOOT

1 Chronicles 22 in the BNTLV

1 Chronicles 22 in the BOATCB

1 Chronicles 22 in the BOATCB2

1 Chronicles 22 in the BOBCV

1 Chronicles 22 in the BOCNT

1 Chronicles 22 in the BOECS

1 Chronicles 22 in the BOHCB

1 Chronicles 22 in the BOHCV

1 Chronicles 22 in the BOHLNT

1 Chronicles 22 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 22 in the BOICB

1 Chronicles 22 in the BOILNTAP

1 Chronicles 22 in the BOITCV

1 Chronicles 22 in the BOKCV

1 Chronicles 22 in the BOKCV2

1 Chronicles 22 in the BOKHWOG

1 Chronicles 22 in the BOKSSV

1 Chronicles 22 in the BOLCB

1 Chronicles 22 in the BOLCB2

1 Chronicles 22 in the BOMCV

1 Chronicles 22 in the BONAV

1 Chronicles 22 in the BONCB

1 Chronicles 22 in the BONLT

1 Chronicles 22 in the BONUT2

1 Chronicles 22 in the BOPLNT

1 Chronicles 22 in the BOSCB

1 Chronicles 22 in the BOSNC

1 Chronicles 22 in the BOTLNT

1 Chronicles 22 in the BOVCB

1 Chronicles 22 in the BOYCB

1 Chronicles 22 in the BPBB

1 Chronicles 22 in the BPH

1 Chronicles 22 in the BSB

1 Chronicles 22 in the CCB

1 Chronicles 22 in the CUV

1 Chronicles 22 in the CUVS

1 Chronicles 22 in the DBT

1 Chronicles 22 in the DGDNT

1 Chronicles 22 in the DHNT

1 Chronicles 22 in the DNT

1 Chronicles 22 in the ELBE

1 Chronicles 22 in the EMTV

1 Chronicles 22 in the ESV

1 Chronicles 22 in the FBV

1 Chronicles 22 in the FEB

1 Chronicles 22 in the GGMNT

1 Chronicles 22 in the GNT

1 Chronicles 22 in the HARY

1 Chronicles 22 in the HNT

1 Chronicles 22 in the IRVA

1 Chronicles 22 in the IRVB

1 Chronicles 22 in the IRVG

1 Chronicles 22 in the IRVH

1 Chronicles 22 in the IRVK

1 Chronicles 22 in the IRVM

1 Chronicles 22 in the IRVM2

1 Chronicles 22 in the IRVO

1 Chronicles 22 in the IRVP

1 Chronicles 22 in the IRVT

1 Chronicles 22 in the IRVT2

1 Chronicles 22 in the IRVU

1 Chronicles 22 in the ISVN

1 Chronicles 22 in the JSNT

1 Chronicles 22 in the KAPI

1 Chronicles 22 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 22 in the KBV

1 Chronicles 22 in the KJV

1 Chronicles 22 in the KNFD

1 Chronicles 22 in the LBA

1 Chronicles 22 in the LBLA

1 Chronicles 22 in the LNT

1 Chronicles 22 in the LSV

1 Chronicles 22 in the MAAL

1 Chronicles 22 in the MBV

1 Chronicles 22 in the MBV2

1 Chronicles 22 in the MHNT

1 Chronicles 22 in the MKNFD

1 Chronicles 22 in the MNG

1 Chronicles 22 in the MNT

1 Chronicles 22 in the MNT2

1 Chronicles 22 in the MRS1T

1 Chronicles 22 in the NAA

1 Chronicles 22 in the NASB

1 Chronicles 22 in the NBLA

1 Chronicles 22 in the NBS

1 Chronicles 22 in the NBVTP

1 Chronicles 22 in the NET2

1 Chronicles 22 in the NIV11

1 Chronicles 22 in the NNT

1 Chronicles 22 in the NNT2

1 Chronicles 22 in the NNT3

1 Chronicles 22 in the PDDPT

1 Chronicles 22 in the PFNT

1 Chronicles 22 in the RMNT

1 Chronicles 22 in the SBIAS

1 Chronicles 22 in the SBIBS

1 Chronicles 22 in the SBIBS2

1 Chronicles 22 in the SBICS

1 Chronicles 22 in the SBIDS

1 Chronicles 22 in the SBIGS

1 Chronicles 22 in the SBIHS

1 Chronicles 22 in the SBIIS

1 Chronicles 22 in the SBIIS2

1 Chronicles 22 in the SBIIS3

1 Chronicles 22 in the SBIKS

1 Chronicles 22 in the SBIKS2

1 Chronicles 22 in the SBIMS

1 Chronicles 22 in the SBIOS

1 Chronicles 22 in the SBIPS

1 Chronicles 22 in the SBISS

1 Chronicles 22 in the SBITS

1 Chronicles 22 in the SBITS2

1 Chronicles 22 in the SBITS3

1 Chronicles 22 in the SBITS4

1 Chronicles 22 in the SBIUS

1 Chronicles 22 in the SBIVS

1 Chronicles 22 in the SBT

1 Chronicles 22 in the SBT1E

1 Chronicles 22 in the SCHL

1 Chronicles 22 in the SNT

1 Chronicles 22 in the SUSU

1 Chronicles 22 in the SUSU2

1 Chronicles 22 in the SYNO

1 Chronicles 22 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 22 in the TBT1E

1 Chronicles 22 in the TBT1E2

1 Chronicles 22 in the TFTIP

1 Chronicles 22 in the TFTU

1 Chronicles 22 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 22 in the THAI

1 Chronicles 22 in the TNFD

1 Chronicles 22 in the TNT

1 Chronicles 22 in the TNTIK

1 Chronicles 22 in the TNTIL

1 Chronicles 22 in the TNTIN

1 Chronicles 22 in the TNTIP

1 Chronicles 22 in the TNTIZ

1 Chronicles 22 in the TOMA

1 Chronicles 22 in the TTENT

1 Chronicles 22 in the UBG

1 Chronicles 22 in the UGV

1 Chronicles 22 in the UGV2

1 Chronicles 22 in the UGV3

1 Chronicles 22 in the VBL

1 Chronicles 22 in the VDCC

1 Chronicles 22 in the YALU

1 Chronicles 22 in the YAPE

1 Chronicles 22 in the YBVTP

1 Chronicles 22 in the ZBP