1 Chronicles 5 (BOGWICC)
1 Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, 2 ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) 3 ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa:Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi. 4 Ana a Yoweli anali awa:Semaya, Gogi,Simei, 5 Mika,Reaya, Baala, 6 ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri. 7 Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa:Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, 8 ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. 9 Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi. 10 Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi. 11 Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka: 12 Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati. 13 Abale awo mwa mabanja awo anali awa:Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri. 14 Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi. 15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo. 16 Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera. 17 Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli. 18 Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. 19 Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. 20 Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. 21 Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, 22 enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo. 23 Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri. 24 Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. 25 Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. 26 Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.
In Other Versions
1 Chronicles 5 in the ANGEFD
1 Chronicles 5 in the ANTPNG2D
1 Chronicles 5 in the AS21
1 Chronicles 5 in the BAGH
1 Chronicles 5 in the BBPNG
1 Chronicles 5 in the BBT1E
1 Chronicles 5 in the BDS
1 Chronicles 5 in the BEV
1 Chronicles 5 in the BHAD
1 Chronicles 5 in the BIB
1 Chronicles 5 in the BLPT
1 Chronicles 5 in the BNT
1 Chronicles 5 in the BNTABOOT
1 Chronicles 5 in the BNTLV
1 Chronicles 5 in the BOATCB
1 Chronicles 5 in the BOATCB2
1 Chronicles 5 in the BOBCV
1 Chronicles 5 in the BOCNT
1 Chronicles 5 in the BOECS
1 Chronicles 5 in the BOHCB
1 Chronicles 5 in the BOHCV
1 Chronicles 5 in the BOHLNT
1 Chronicles 5 in the BOHNTLTAL
1 Chronicles 5 in the BOICB
1 Chronicles 5 in the BOILNTAP
1 Chronicles 5 in the BOITCV
1 Chronicles 5 in the BOKCV
1 Chronicles 5 in the BOKCV2
1 Chronicles 5 in the BOKHWOG
1 Chronicles 5 in the BOKSSV
1 Chronicles 5 in the BOLCB
1 Chronicles 5 in the BOLCB2
1 Chronicles 5 in the BOMCV
1 Chronicles 5 in the BONAV
1 Chronicles 5 in the BONCB
1 Chronicles 5 in the BONLT
1 Chronicles 5 in the BONUT2
1 Chronicles 5 in the BOPLNT
1 Chronicles 5 in the BOSCB
1 Chronicles 5 in the BOSNC
1 Chronicles 5 in the BOTLNT
1 Chronicles 5 in the BOVCB
1 Chronicles 5 in the BOYCB
1 Chronicles 5 in the BPBB
1 Chronicles 5 in the BPH
1 Chronicles 5 in the BSB
1 Chronicles 5 in the CCB
1 Chronicles 5 in the CUV
1 Chronicles 5 in the CUVS
1 Chronicles 5 in the DBT
1 Chronicles 5 in the DGDNT
1 Chronicles 5 in the DHNT
1 Chronicles 5 in the DNT
1 Chronicles 5 in the ELBE
1 Chronicles 5 in the EMTV
1 Chronicles 5 in the ESV
1 Chronicles 5 in the FBV
1 Chronicles 5 in the FEB
1 Chronicles 5 in the GGMNT
1 Chronicles 5 in the GNT
1 Chronicles 5 in the HARY
1 Chronicles 5 in the HNT
1 Chronicles 5 in the IRVA
1 Chronicles 5 in the IRVB
1 Chronicles 5 in the IRVG
1 Chronicles 5 in the IRVH
1 Chronicles 5 in the IRVK
1 Chronicles 5 in the IRVM
1 Chronicles 5 in the IRVM2
1 Chronicles 5 in the IRVO
1 Chronicles 5 in the IRVP
1 Chronicles 5 in the IRVT
1 Chronicles 5 in the IRVT2
1 Chronicles 5 in the IRVU
1 Chronicles 5 in the ISVN
1 Chronicles 5 in the JSNT
1 Chronicles 5 in the KAPI
1 Chronicles 5 in the KBT1ETNIK
1 Chronicles 5 in the KBV
1 Chronicles 5 in the KJV
1 Chronicles 5 in the KNFD
1 Chronicles 5 in the LBA
1 Chronicles 5 in the LBLA
1 Chronicles 5 in the LNT
1 Chronicles 5 in the LSV
1 Chronicles 5 in the MAAL
1 Chronicles 5 in the MBV
1 Chronicles 5 in the MBV2
1 Chronicles 5 in the MHNT
1 Chronicles 5 in the MKNFD
1 Chronicles 5 in the MNG
1 Chronicles 5 in the MNT
1 Chronicles 5 in the MNT2
1 Chronicles 5 in the MRS1T
1 Chronicles 5 in the NAA
1 Chronicles 5 in the NASB
1 Chronicles 5 in the NBLA
1 Chronicles 5 in the NBS
1 Chronicles 5 in the NBVTP
1 Chronicles 5 in the NET2
1 Chronicles 5 in the NIV11
1 Chronicles 5 in the NNT
1 Chronicles 5 in the NNT2
1 Chronicles 5 in the NNT3
1 Chronicles 5 in the PDDPT
1 Chronicles 5 in the PFNT
1 Chronicles 5 in the RMNT
1 Chronicles 5 in the SBIAS
1 Chronicles 5 in the SBIBS
1 Chronicles 5 in the SBIBS2
1 Chronicles 5 in the SBICS
1 Chronicles 5 in the SBIDS
1 Chronicles 5 in the SBIGS
1 Chronicles 5 in the SBIHS
1 Chronicles 5 in the SBIIS
1 Chronicles 5 in the SBIIS2
1 Chronicles 5 in the SBIIS3
1 Chronicles 5 in the SBIKS
1 Chronicles 5 in the SBIKS2
1 Chronicles 5 in the SBIMS
1 Chronicles 5 in the SBIOS
1 Chronicles 5 in the SBIPS
1 Chronicles 5 in the SBISS
1 Chronicles 5 in the SBITS
1 Chronicles 5 in the SBITS2
1 Chronicles 5 in the SBITS3
1 Chronicles 5 in the SBITS4
1 Chronicles 5 in the SBIUS
1 Chronicles 5 in the SBIVS
1 Chronicles 5 in the SBT
1 Chronicles 5 in the SBT1E
1 Chronicles 5 in the SCHL
1 Chronicles 5 in the SNT
1 Chronicles 5 in the SUSU
1 Chronicles 5 in the SUSU2
1 Chronicles 5 in the SYNO
1 Chronicles 5 in the TBIAOTANT
1 Chronicles 5 in the TBT1E
1 Chronicles 5 in the TBT1E2
1 Chronicles 5 in the TFTIP
1 Chronicles 5 in the TFTU
1 Chronicles 5 in the TGNTATF3T
1 Chronicles 5 in the THAI
1 Chronicles 5 in the TNFD
1 Chronicles 5 in the TNT
1 Chronicles 5 in the TNTIK
1 Chronicles 5 in the TNTIL
1 Chronicles 5 in the TNTIN
1 Chronicles 5 in the TNTIP
1 Chronicles 5 in the TNTIZ
1 Chronicles 5 in the TOMA
1 Chronicles 5 in the TTENT
1 Chronicles 5 in the UBG
1 Chronicles 5 in the UGV
1 Chronicles 5 in the UGV2
1 Chronicles 5 in the UGV3
1 Chronicles 5 in the VBL
1 Chronicles 5 in the VDCC
1 Chronicles 5 in the YALU
1 Chronicles 5 in the YAPE
1 Chronicles 5 in the YBVTP
1 Chronicles 5 in the ZBP