1 Corinthians 2 (BOGWICC)
1 Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu. 2 Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo. 3 Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri. 4 Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu, 5 kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu. 6 Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. 7 Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. 8 Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. 9 Komabe monga zalembedwa kuti,“Palibe diso linaona,palibe khutu linamva,palibe amene anaganizira,zimene Mulungu anakonzera amene amukonda” 10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe. 11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. 12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. 13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. 14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. 15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. 16 Pakuti“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,kuti akhoza kumulangiza Iye.”Koma tili nawo mtima wa Khristu.
In Other Versions
1 Corinthians 2 in the ANGEFD
1 Corinthians 2 in the ANTPNG2D
1 Corinthians 2 in the AS21
1 Corinthians 2 in the BAGH
1 Corinthians 2 in the BBPNG
1 Corinthians 2 in the BBT1E
1 Corinthians 2 in the BDS
1 Corinthians 2 in the BEV
1 Corinthians 2 in the BHAD
1 Corinthians 2 in the BIB
1 Corinthians 2 in the BLPT
1 Corinthians 2 in the BNT
1 Corinthians 2 in the BNTABOOT
1 Corinthians 2 in the BNTLV
1 Corinthians 2 in the BOATCB
1 Corinthians 2 in the BOATCB2
1 Corinthians 2 in the BOBCV
1 Corinthians 2 in the BOCNT
1 Corinthians 2 in the BOECS
1 Corinthians 2 in the BOHCB
1 Corinthians 2 in the BOHCV
1 Corinthians 2 in the BOHLNT
1 Corinthians 2 in the BOHNTLTAL
1 Corinthians 2 in the BOICB
1 Corinthians 2 in the BOILNTAP
1 Corinthians 2 in the BOITCV
1 Corinthians 2 in the BOKCV
1 Corinthians 2 in the BOKCV2
1 Corinthians 2 in the BOKHWOG
1 Corinthians 2 in the BOKSSV
1 Corinthians 2 in the BOLCB
1 Corinthians 2 in the BOLCB2
1 Corinthians 2 in the BOMCV
1 Corinthians 2 in the BONAV
1 Corinthians 2 in the BONCB
1 Corinthians 2 in the BONLT
1 Corinthians 2 in the BONUT2
1 Corinthians 2 in the BOPLNT
1 Corinthians 2 in the BOSCB
1 Corinthians 2 in the BOSNC
1 Corinthians 2 in the BOTLNT
1 Corinthians 2 in the BOVCB
1 Corinthians 2 in the BOYCB
1 Corinthians 2 in the BPBB
1 Corinthians 2 in the BPH
1 Corinthians 2 in the BSB
1 Corinthians 2 in the CCB
1 Corinthians 2 in the CUV
1 Corinthians 2 in the CUVS
1 Corinthians 2 in the DBT
1 Corinthians 2 in the DGDNT
1 Corinthians 2 in the DHNT
1 Corinthians 2 in the DNT
1 Corinthians 2 in the ELBE
1 Corinthians 2 in the EMTV
1 Corinthians 2 in the ESV
1 Corinthians 2 in the FBV
1 Corinthians 2 in the FEB
1 Corinthians 2 in the GGMNT
1 Corinthians 2 in the GNT
1 Corinthians 2 in the HARY
1 Corinthians 2 in the HNT
1 Corinthians 2 in the IRVA
1 Corinthians 2 in the IRVB
1 Corinthians 2 in the IRVG
1 Corinthians 2 in the IRVH
1 Corinthians 2 in the IRVK
1 Corinthians 2 in the IRVM
1 Corinthians 2 in the IRVM2
1 Corinthians 2 in the IRVO
1 Corinthians 2 in the IRVP
1 Corinthians 2 in the IRVT
1 Corinthians 2 in the IRVT2
1 Corinthians 2 in the IRVU
1 Corinthians 2 in the ISVN
1 Corinthians 2 in the JSNT
1 Corinthians 2 in the KAPI
1 Corinthians 2 in the KBT1ETNIK
1 Corinthians 2 in the KBV
1 Corinthians 2 in the KJV
1 Corinthians 2 in the KNFD
1 Corinthians 2 in the LBA
1 Corinthians 2 in the LBLA
1 Corinthians 2 in the LNT
1 Corinthians 2 in the LSV
1 Corinthians 2 in the MAAL
1 Corinthians 2 in the MBV
1 Corinthians 2 in the MBV2
1 Corinthians 2 in the MHNT
1 Corinthians 2 in the MKNFD
1 Corinthians 2 in the MNG
1 Corinthians 2 in the MNT
1 Corinthians 2 in the MNT2
1 Corinthians 2 in the MRS1T
1 Corinthians 2 in the NAA
1 Corinthians 2 in the NASB
1 Corinthians 2 in the NBLA
1 Corinthians 2 in the NBS
1 Corinthians 2 in the NBVTP
1 Corinthians 2 in the NET2
1 Corinthians 2 in the NIV11
1 Corinthians 2 in the NNT
1 Corinthians 2 in the NNT2
1 Corinthians 2 in the NNT3
1 Corinthians 2 in the PDDPT
1 Corinthians 2 in the PFNT
1 Corinthians 2 in the RMNT
1 Corinthians 2 in the SBIAS
1 Corinthians 2 in the SBIBS
1 Corinthians 2 in the SBIBS2
1 Corinthians 2 in the SBICS
1 Corinthians 2 in the SBIDS
1 Corinthians 2 in the SBIGS
1 Corinthians 2 in the SBIHS
1 Corinthians 2 in the SBIIS
1 Corinthians 2 in the SBIIS2
1 Corinthians 2 in the SBIIS3
1 Corinthians 2 in the SBIKS
1 Corinthians 2 in the SBIKS2
1 Corinthians 2 in the SBIMS
1 Corinthians 2 in the SBIOS
1 Corinthians 2 in the SBIPS
1 Corinthians 2 in the SBISS
1 Corinthians 2 in the SBITS
1 Corinthians 2 in the SBITS2
1 Corinthians 2 in the SBITS3
1 Corinthians 2 in the SBITS4
1 Corinthians 2 in the SBIUS
1 Corinthians 2 in the SBIVS
1 Corinthians 2 in the SBT
1 Corinthians 2 in the SBT1E
1 Corinthians 2 in the SCHL
1 Corinthians 2 in the SNT
1 Corinthians 2 in the SUSU
1 Corinthians 2 in the SUSU2
1 Corinthians 2 in the SYNO
1 Corinthians 2 in the TBIAOTANT
1 Corinthians 2 in the TBT1E
1 Corinthians 2 in the TBT1E2
1 Corinthians 2 in the TFTIP
1 Corinthians 2 in the TFTU
1 Corinthians 2 in the TGNTATF3T
1 Corinthians 2 in the THAI
1 Corinthians 2 in the TNFD
1 Corinthians 2 in the TNT
1 Corinthians 2 in the TNTIK
1 Corinthians 2 in the TNTIL
1 Corinthians 2 in the TNTIN
1 Corinthians 2 in the TNTIP
1 Corinthians 2 in the TNTIZ
1 Corinthians 2 in the TOMA
1 Corinthians 2 in the TTENT
1 Corinthians 2 in the UBG
1 Corinthians 2 in the UGV
1 Corinthians 2 in the UGV2
1 Corinthians 2 in the UGV3
1 Corinthians 2 in the VBL
1 Corinthians 2 in the VDCC
1 Corinthians 2 in the YALU
1 Corinthians 2 in the YAPE
1 Corinthians 2 in the YBVTP
1 Corinthians 2 in the ZBP