1 John 2 (BOGWICC)

1 Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo. 2 Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi. 3 Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. 4 Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. 5 Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. 6 Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala. 7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale. 8 Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala. 9 Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. 10 Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake. 12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberanipopeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu. 13 Inu abambo, ndikukulemberanipopeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.Inu anyamata, ndikukulemberanipopeza kuti munagonjetsa woyipayo. 14 Ana okondedwa, ndikukulemberanichifukwa mumawadziwa Atate.Abambo, ndikukulemberanichifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.Inu anyamata, ndikukulemberanichifukwa ndinu amphamvu.Mawu a Mulungu amakhala mwa inundipo mumamugonjetsa woyipayo. 15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. 16 Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya. 18 Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza. 19 Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu. 20 Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi. 21 Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi. 22 Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana. 23 Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate. 24 Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate. 25 Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha. 26 Ine ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuwuzeni za amene akufuna kukusocheretsani. 27 Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo. 28 Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera. 29 Popeza mukudziwa kuti Khristu ndi wolungama, choncho mukudziwanso kuti aliyense amene amachita chilungamo ndi mwana wa Mulungu.

In Other Versions

1 John 2 in the ANGEFD

1 John 2 in the ANTPNG2D

1 John 2 in the AS21

1 John 2 in the BAGH

1 John 2 in the BBPNG

1 John 2 in the BBT1E

1 John 2 in the BDS

1 John 2 in the BEV

1 John 2 in the BHAD

1 John 2 in the BIB

1 John 2 in the BLPT

1 John 2 in the BNT

1 John 2 in the BNTABOOT

1 John 2 in the BNTLV

1 John 2 in the BOATCB

1 John 2 in the BOATCB2

1 John 2 in the BOBCV

1 John 2 in the BOCNT

1 John 2 in the BOECS

1 John 2 in the BOHCB

1 John 2 in the BOHCV

1 John 2 in the BOHLNT

1 John 2 in the BOHNTLTAL

1 John 2 in the BOICB

1 John 2 in the BOILNTAP

1 John 2 in the BOITCV

1 John 2 in the BOKCV

1 John 2 in the BOKCV2

1 John 2 in the BOKHWOG

1 John 2 in the BOKSSV

1 John 2 in the BOLCB

1 John 2 in the BOLCB2

1 John 2 in the BOMCV

1 John 2 in the BONAV

1 John 2 in the BONCB

1 John 2 in the BONLT

1 John 2 in the BONUT2

1 John 2 in the BOPLNT

1 John 2 in the BOSCB

1 John 2 in the BOSNC

1 John 2 in the BOTLNT

1 John 2 in the BOVCB

1 John 2 in the BOYCB

1 John 2 in the BPBB

1 John 2 in the BPH

1 John 2 in the BSB

1 John 2 in the CCB

1 John 2 in the CUV

1 John 2 in the CUVS

1 John 2 in the DBT

1 John 2 in the DGDNT

1 John 2 in the DHNT

1 John 2 in the DNT

1 John 2 in the ELBE

1 John 2 in the EMTV

1 John 2 in the ESV

1 John 2 in the FBV

1 John 2 in the FEB

1 John 2 in the GGMNT

1 John 2 in the GNT

1 John 2 in the HARY

1 John 2 in the HNT

1 John 2 in the IRVA

1 John 2 in the IRVB

1 John 2 in the IRVG

1 John 2 in the IRVH

1 John 2 in the IRVK

1 John 2 in the IRVM

1 John 2 in the IRVM2

1 John 2 in the IRVO

1 John 2 in the IRVP

1 John 2 in the IRVT

1 John 2 in the IRVT2

1 John 2 in the IRVU

1 John 2 in the ISVN

1 John 2 in the JSNT

1 John 2 in the KAPI

1 John 2 in the KBT1ETNIK

1 John 2 in the KBV

1 John 2 in the KJV

1 John 2 in the KNFD

1 John 2 in the LBA

1 John 2 in the LBLA

1 John 2 in the LNT

1 John 2 in the LSV

1 John 2 in the MAAL

1 John 2 in the MBV

1 John 2 in the MBV2

1 John 2 in the MHNT

1 John 2 in the MKNFD

1 John 2 in the MNG

1 John 2 in the MNT

1 John 2 in the MNT2

1 John 2 in the MRS1T

1 John 2 in the NAA

1 John 2 in the NASB

1 John 2 in the NBLA

1 John 2 in the NBS

1 John 2 in the NBVTP

1 John 2 in the NET2

1 John 2 in the NIV11

1 John 2 in the NNT

1 John 2 in the NNT2

1 John 2 in the NNT3

1 John 2 in the PDDPT

1 John 2 in the PFNT

1 John 2 in the RMNT

1 John 2 in the SBIAS

1 John 2 in the SBIBS

1 John 2 in the SBIBS2

1 John 2 in the SBICS

1 John 2 in the SBIDS

1 John 2 in the SBIGS

1 John 2 in the SBIHS

1 John 2 in the SBIIS

1 John 2 in the SBIIS2

1 John 2 in the SBIIS3

1 John 2 in the SBIKS

1 John 2 in the SBIKS2

1 John 2 in the SBIMS

1 John 2 in the SBIOS

1 John 2 in the SBIPS

1 John 2 in the SBISS

1 John 2 in the SBITS

1 John 2 in the SBITS2

1 John 2 in the SBITS3

1 John 2 in the SBITS4

1 John 2 in the SBIUS

1 John 2 in the SBIVS

1 John 2 in the SBT

1 John 2 in the SBT1E

1 John 2 in the SCHL

1 John 2 in the SNT

1 John 2 in the SUSU

1 John 2 in the SUSU2

1 John 2 in the SYNO

1 John 2 in the TBIAOTANT

1 John 2 in the TBT1E

1 John 2 in the TBT1E2

1 John 2 in the TFTIP

1 John 2 in the TFTU

1 John 2 in the TGNTATF3T

1 John 2 in the THAI

1 John 2 in the TNFD

1 John 2 in the TNT

1 John 2 in the TNTIK

1 John 2 in the TNTIL

1 John 2 in the TNTIN

1 John 2 in the TNTIP

1 John 2 in the TNTIZ

1 John 2 in the TOMA

1 John 2 in the TTENT

1 John 2 in the UBG

1 John 2 in the UGV

1 John 2 in the UGV2

1 John 2 in the UGV3

1 John 2 in the VBL

1 John 2 in the VDCC

1 John 2 in the YALU

1 John 2 in the YAPE

1 John 2 in the YBVTP

1 John 2 in the ZBP