1 Kings 17 (BOGWICC)

1 Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.” 2 Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, 3 “Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani. 4 Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.” 5 Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko. 6 Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo. 7 Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo. 8 Yehova anayankhula naye kuti, 9 “Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” 10 Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” 11 Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.” 12 Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.” 13 Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. 14 Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ” 15 Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. 16 Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya. 17 Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. 18 Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?” 19 Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. 20 Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” 21 Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!” 22 Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. 23 Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!” 24 Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”

In Other Versions

1 Kings 17 in the ANGEFD

1 Kings 17 in the ANTPNG2D

1 Kings 17 in the AS21

1 Kings 17 in the BAGH

1 Kings 17 in the BBPNG

1 Kings 17 in the BBT1E

1 Kings 17 in the BDS

1 Kings 17 in the BEV

1 Kings 17 in the BHAD

1 Kings 17 in the BIB

1 Kings 17 in the BLPT

1 Kings 17 in the BNT

1 Kings 17 in the BNTABOOT

1 Kings 17 in the BNTLV

1 Kings 17 in the BOATCB

1 Kings 17 in the BOATCB2

1 Kings 17 in the BOBCV

1 Kings 17 in the BOCNT

1 Kings 17 in the BOECS

1 Kings 17 in the BOHCB

1 Kings 17 in the BOHCV

1 Kings 17 in the BOHLNT

1 Kings 17 in the BOHNTLTAL

1 Kings 17 in the BOICB

1 Kings 17 in the BOILNTAP

1 Kings 17 in the BOITCV

1 Kings 17 in the BOKCV

1 Kings 17 in the BOKCV2

1 Kings 17 in the BOKHWOG

1 Kings 17 in the BOKSSV

1 Kings 17 in the BOLCB

1 Kings 17 in the BOLCB2

1 Kings 17 in the BOMCV

1 Kings 17 in the BONAV

1 Kings 17 in the BONCB

1 Kings 17 in the BONLT

1 Kings 17 in the BONUT2

1 Kings 17 in the BOPLNT

1 Kings 17 in the BOSCB

1 Kings 17 in the BOSNC

1 Kings 17 in the BOTLNT

1 Kings 17 in the BOVCB

1 Kings 17 in the BOYCB

1 Kings 17 in the BPBB

1 Kings 17 in the BPH

1 Kings 17 in the BSB

1 Kings 17 in the CCB

1 Kings 17 in the CUV

1 Kings 17 in the CUVS

1 Kings 17 in the DBT

1 Kings 17 in the DGDNT

1 Kings 17 in the DHNT

1 Kings 17 in the DNT

1 Kings 17 in the ELBE

1 Kings 17 in the EMTV

1 Kings 17 in the ESV

1 Kings 17 in the FBV

1 Kings 17 in the FEB

1 Kings 17 in the GGMNT

1 Kings 17 in the GNT

1 Kings 17 in the HARY

1 Kings 17 in the HNT

1 Kings 17 in the IRVA

1 Kings 17 in the IRVB

1 Kings 17 in the IRVG

1 Kings 17 in the IRVH

1 Kings 17 in the IRVK

1 Kings 17 in the IRVM

1 Kings 17 in the IRVM2

1 Kings 17 in the IRVO

1 Kings 17 in the IRVP

1 Kings 17 in the IRVT

1 Kings 17 in the IRVT2

1 Kings 17 in the IRVU

1 Kings 17 in the ISVN

1 Kings 17 in the JSNT

1 Kings 17 in the KAPI

1 Kings 17 in the KBT1ETNIK

1 Kings 17 in the KBV

1 Kings 17 in the KJV

1 Kings 17 in the KNFD

1 Kings 17 in the LBA

1 Kings 17 in the LBLA

1 Kings 17 in the LNT

1 Kings 17 in the LSV

1 Kings 17 in the MAAL

1 Kings 17 in the MBV

1 Kings 17 in the MBV2

1 Kings 17 in the MHNT

1 Kings 17 in the MKNFD

1 Kings 17 in the MNG

1 Kings 17 in the MNT

1 Kings 17 in the MNT2

1 Kings 17 in the MRS1T

1 Kings 17 in the NAA

1 Kings 17 in the NASB

1 Kings 17 in the NBLA

1 Kings 17 in the NBS

1 Kings 17 in the NBVTP

1 Kings 17 in the NET2

1 Kings 17 in the NIV11

1 Kings 17 in the NNT

1 Kings 17 in the NNT2

1 Kings 17 in the NNT3

1 Kings 17 in the PDDPT

1 Kings 17 in the PFNT

1 Kings 17 in the RMNT

1 Kings 17 in the SBIAS

1 Kings 17 in the SBIBS

1 Kings 17 in the SBIBS2

1 Kings 17 in the SBICS

1 Kings 17 in the SBIDS

1 Kings 17 in the SBIGS

1 Kings 17 in the SBIHS

1 Kings 17 in the SBIIS

1 Kings 17 in the SBIIS2

1 Kings 17 in the SBIIS3

1 Kings 17 in the SBIKS

1 Kings 17 in the SBIKS2

1 Kings 17 in the SBIMS

1 Kings 17 in the SBIOS

1 Kings 17 in the SBIPS

1 Kings 17 in the SBISS

1 Kings 17 in the SBITS

1 Kings 17 in the SBITS2

1 Kings 17 in the SBITS3

1 Kings 17 in the SBITS4

1 Kings 17 in the SBIUS

1 Kings 17 in the SBIVS

1 Kings 17 in the SBT

1 Kings 17 in the SBT1E

1 Kings 17 in the SCHL

1 Kings 17 in the SNT

1 Kings 17 in the SUSU

1 Kings 17 in the SUSU2

1 Kings 17 in the SYNO

1 Kings 17 in the TBIAOTANT

1 Kings 17 in the TBT1E

1 Kings 17 in the TBT1E2

1 Kings 17 in the TFTIP

1 Kings 17 in the TFTU

1 Kings 17 in the TGNTATF3T

1 Kings 17 in the THAI

1 Kings 17 in the TNFD

1 Kings 17 in the TNT

1 Kings 17 in the TNTIK

1 Kings 17 in the TNTIL

1 Kings 17 in the TNTIN

1 Kings 17 in the TNTIP

1 Kings 17 in the TNTIZ

1 Kings 17 in the TOMA

1 Kings 17 in the TTENT

1 Kings 17 in the UBG

1 Kings 17 in the UGV

1 Kings 17 in the UGV2

1 Kings 17 in the UGV3

1 Kings 17 in the VBL

1 Kings 17 in the VDCC

1 Kings 17 in the YALU

1 Kings 17 in the YAPE

1 Kings 17 in the YBVTP

1 Kings 17 in the ZBP