1 Kings 5 (BOGWICC)

1 Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse. 2 Solomoni anabweza mawu awa kwa Hiramu: 3 “Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo. 4 Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse. 5 Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’ 6 “Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.” 7 Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.” 8 Tsono Hiramu anabweza mawu awa kwa Solomoni:“Ndalandira uthenga umene mwanditumizira ndipo ine ndidzachita zonse zimene mukufuna pokupatsani mitengo ya mkungudza ndi payini. 9 Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.” 10 Motero Hiramu anapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi payini imene ankayifuna, 11 ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka. 12 Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano. 13 Mfumu Solomoni inasonkhanitsa anthu ogwira ntchito ya thangata mʼdziko lonse la Israeli ndipo anthu athangatawo analipo 30,000. 14 Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo. 15 Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri, 16 ndi akapitawo 33,000 amene ankayangʼanira ntchitoyi ndiponso anthu ogwira ntchito zina. 17 Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu. 18 Amisiri a Solomoni ndi a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala anasema miyala ndi kukonza matabwa ndi miyala yomangira Nyumba ya Mulungu.

In Other Versions

1 Kings 5 in the ANGEFD

1 Kings 5 in the ANTPNG2D

1 Kings 5 in the AS21

1 Kings 5 in the BAGH

1 Kings 5 in the BBPNG

1 Kings 5 in the BBT1E

1 Kings 5 in the BDS

1 Kings 5 in the BEV

1 Kings 5 in the BHAD

1 Kings 5 in the BIB

1 Kings 5 in the BLPT

1 Kings 5 in the BNT

1 Kings 5 in the BNTABOOT

1 Kings 5 in the BNTLV

1 Kings 5 in the BOATCB

1 Kings 5 in the BOATCB2

1 Kings 5 in the BOBCV

1 Kings 5 in the BOCNT

1 Kings 5 in the BOECS

1 Kings 5 in the BOHCB

1 Kings 5 in the BOHCV

1 Kings 5 in the BOHLNT

1 Kings 5 in the BOHNTLTAL

1 Kings 5 in the BOICB

1 Kings 5 in the BOILNTAP

1 Kings 5 in the BOITCV

1 Kings 5 in the BOKCV

1 Kings 5 in the BOKCV2

1 Kings 5 in the BOKHWOG

1 Kings 5 in the BOKSSV

1 Kings 5 in the BOLCB

1 Kings 5 in the BOLCB2

1 Kings 5 in the BOMCV

1 Kings 5 in the BONAV

1 Kings 5 in the BONCB

1 Kings 5 in the BONLT

1 Kings 5 in the BONUT2

1 Kings 5 in the BOPLNT

1 Kings 5 in the BOSCB

1 Kings 5 in the BOSNC

1 Kings 5 in the BOTLNT

1 Kings 5 in the BOVCB

1 Kings 5 in the BOYCB

1 Kings 5 in the BPBB

1 Kings 5 in the BPH

1 Kings 5 in the BSB

1 Kings 5 in the CCB

1 Kings 5 in the CUV

1 Kings 5 in the CUVS

1 Kings 5 in the DBT

1 Kings 5 in the DGDNT

1 Kings 5 in the DHNT

1 Kings 5 in the DNT

1 Kings 5 in the ELBE

1 Kings 5 in the EMTV

1 Kings 5 in the ESV

1 Kings 5 in the FBV

1 Kings 5 in the FEB

1 Kings 5 in the GGMNT

1 Kings 5 in the GNT

1 Kings 5 in the HARY

1 Kings 5 in the HNT

1 Kings 5 in the IRVA

1 Kings 5 in the IRVB

1 Kings 5 in the IRVG

1 Kings 5 in the IRVH

1 Kings 5 in the IRVK

1 Kings 5 in the IRVM

1 Kings 5 in the IRVM2

1 Kings 5 in the IRVO

1 Kings 5 in the IRVP

1 Kings 5 in the IRVT

1 Kings 5 in the IRVT2

1 Kings 5 in the IRVU

1 Kings 5 in the ISVN

1 Kings 5 in the JSNT

1 Kings 5 in the KAPI

1 Kings 5 in the KBT1ETNIK

1 Kings 5 in the KBV

1 Kings 5 in the KJV

1 Kings 5 in the KNFD

1 Kings 5 in the LBA

1 Kings 5 in the LBLA

1 Kings 5 in the LNT

1 Kings 5 in the LSV

1 Kings 5 in the MAAL

1 Kings 5 in the MBV

1 Kings 5 in the MBV2

1 Kings 5 in the MHNT

1 Kings 5 in the MKNFD

1 Kings 5 in the MNG

1 Kings 5 in the MNT

1 Kings 5 in the MNT2

1 Kings 5 in the MRS1T

1 Kings 5 in the NAA

1 Kings 5 in the NASB

1 Kings 5 in the NBLA

1 Kings 5 in the NBS

1 Kings 5 in the NBVTP

1 Kings 5 in the NET2

1 Kings 5 in the NIV11

1 Kings 5 in the NNT

1 Kings 5 in the NNT2

1 Kings 5 in the NNT3

1 Kings 5 in the PDDPT

1 Kings 5 in the PFNT

1 Kings 5 in the RMNT

1 Kings 5 in the SBIAS

1 Kings 5 in the SBIBS

1 Kings 5 in the SBIBS2

1 Kings 5 in the SBICS

1 Kings 5 in the SBIDS

1 Kings 5 in the SBIGS

1 Kings 5 in the SBIHS

1 Kings 5 in the SBIIS

1 Kings 5 in the SBIIS2

1 Kings 5 in the SBIIS3

1 Kings 5 in the SBIKS

1 Kings 5 in the SBIKS2

1 Kings 5 in the SBIMS

1 Kings 5 in the SBIOS

1 Kings 5 in the SBIPS

1 Kings 5 in the SBISS

1 Kings 5 in the SBITS

1 Kings 5 in the SBITS2

1 Kings 5 in the SBITS3

1 Kings 5 in the SBITS4

1 Kings 5 in the SBIUS

1 Kings 5 in the SBIVS

1 Kings 5 in the SBT

1 Kings 5 in the SBT1E

1 Kings 5 in the SCHL

1 Kings 5 in the SNT

1 Kings 5 in the SUSU

1 Kings 5 in the SUSU2

1 Kings 5 in the SYNO

1 Kings 5 in the TBIAOTANT

1 Kings 5 in the TBT1E

1 Kings 5 in the TBT1E2

1 Kings 5 in the TFTIP

1 Kings 5 in the TFTU

1 Kings 5 in the TGNTATF3T

1 Kings 5 in the THAI

1 Kings 5 in the TNFD

1 Kings 5 in the TNT

1 Kings 5 in the TNTIK

1 Kings 5 in the TNTIL

1 Kings 5 in the TNTIN

1 Kings 5 in the TNTIP

1 Kings 5 in the TNTIZ

1 Kings 5 in the TOMA

1 Kings 5 in the TTENT

1 Kings 5 in the UBG

1 Kings 5 in the UGV

1 Kings 5 in the UGV2

1 Kings 5 in the UGV3

1 Kings 5 in the VBL

1 Kings 5 in the VDCC

1 Kings 5 in the YALU

1 Kings 5 in the YAPE

1 Kings 5 in the YBVTP

1 Kings 5 in the ZBP