1 Samuel 18 (BOGWICC)

1 Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha. 2 Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake. 3 Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. 4 Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba. 5 Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli. 6 Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira. 7 Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati:“Sauli wapha 1,000,Koma Davide wapha miyandamiyanda.” 8 Koma Sauli anapsa mtima kwambiri ndipo mawu amenewa anamuyipira. Iye anati, “Iwo amuwerengera Davide miyandamiyanda, koma ine 1,000 okha. Nanga chatsalanso nʼchiyani kuti atenge? Si ufumu basi?” 9 Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide. 10 Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake. 11 Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse. 12 Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli. 13 Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa. 14 Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye. 15 Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri. 16 Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo. 17 Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!” 18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?” 19 Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire. 20 Koma Mikala mwana wamkazi wa Sauli anamukonda Davide ndipo Sauli atamva za zimenezi, anakondwera. 21 Sauli ankaganiza kuti, “Ndimupatse amukwatire kuti akhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo adzaphedwe ndi Afilisti.” Choncho Sauli anawuza Davide kachiwiri, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.” 22 Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” 23 Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.” 24 Nduna za Sauli zinamuwuza zonse zimene anayankha Davide. 25 Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’ ” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti. 26 Nduna za Saulizo zitamuwuza Davide zimenezi, anakondwera kuti akhale mpongozi wa mfumu. Koma nthawi imene anapatsidwa isanathe, 27 Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire. 28 Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide, 29 iye anapitirirabe kumuopa Davide ndi kumadana naye moyo wake wonse. 30 Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.

In Other Versions

1 Samuel 18 in the ANGEFD

1 Samuel 18 in the ANTPNG2D

1 Samuel 18 in the AS21

1 Samuel 18 in the BAGH

1 Samuel 18 in the BBPNG

1 Samuel 18 in the BBT1E

1 Samuel 18 in the BDS

1 Samuel 18 in the BEV

1 Samuel 18 in the BHAD

1 Samuel 18 in the BIB

1 Samuel 18 in the BLPT

1 Samuel 18 in the BNT

1 Samuel 18 in the BNTABOOT

1 Samuel 18 in the BNTLV

1 Samuel 18 in the BOATCB

1 Samuel 18 in the BOATCB2

1 Samuel 18 in the BOBCV

1 Samuel 18 in the BOCNT

1 Samuel 18 in the BOECS

1 Samuel 18 in the BOHCB

1 Samuel 18 in the BOHCV

1 Samuel 18 in the BOHLNT

1 Samuel 18 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 18 in the BOICB

1 Samuel 18 in the BOILNTAP

1 Samuel 18 in the BOITCV

1 Samuel 18 in the BOKCV

1 Samuel 18 in the BOKCV2

1 Samuel 18 in the BOKHWOG

1 Samuel 18 in the BOKSSV

1 Samuel 18 in the BOLCB

1 Samuel 18 in the BOLCB2

1 Samuel 18 in the BOMCV

1 Samuel 18 in the BONAV

1 Samuel 18 in the BONCB

1 Samuel 18 in the BONLT

1 Samuel 18 in the BONUT2

1 Samuel 18 in the BOPLNT

1 Samuel 18 in the BOSCB

1 Samuel 18 in the BOSNC

1 Samuel 18 in the BOTLNT

1 Samuel 18 in the BOVCB

1 Samuel 18 in the BOYCB

1 Samuel 18 in the BPBB

1 Samuel 18 in the BPH

1 Samuel 18 in the BSB

1 Samuel 18 in the CCB

1 Samuel 18 in the CUV

1 Samuel 18 in the CUVS

1 Samuel 18 in the DBT

1 Samuel 18 in the DGDNT

1 Samuel 18 in the DHNT

1 Samuel 18 in the DNT

1 Samuel 18 in the ELBE

1 Samuel 18 in the EMTV

1 Samuel 18 in the ESV

1 Samuel 18 in the FBV

1 Samuel 18 in the FEB

1 Samuel 18 in the GGMNT

1 Samuel 18 in the GNT

1 Samuel 18 in the HARY

1 Samuel 18 in the HNT

1 Samuel 18 in the IRVA

1 Samuel 18 in the IRVB

1 Samuel 18 in the IRVG

1 Samuel 18 in the IRVH

1 Samuel 18 in the IRVK

1 Samuel 18 in the IRVM

1 Samuel 18 in the IRVM2

1 Samuel 18 in the IRVO

1 Samuel 18 in the IRVP

1 Samuel 18 in the IRVT

1 Samuel 18 in the IRVT2

1 Samuel 18 in the IRVU

1 Samuel 18 in the ISVN

1 Samuel 18 in the JSNT

1 Samuel 18 in the KAPI

1 Samuel 18 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 18 in the KBV

1 Samuel 18 in the KJV

1 Samuel 18 in the KNFD

1 Samuel 18 in the LBA

1 Samuel 18 in the LBLA

1 Samuel 18 in the LNT

1 Samuel 18 in the LSV

1 Samuel 18 in the MAAL

1 Samuel 18 in the MBV

1 Samuel 18 in the MBV2

1 Samuel 18 in the MHNT

1 Samuel 18 in the MKNFD

1 Samuel 18 in the MNG

1 Samuel 18 in the MNT

1 Samuel 18 in the MNT2

1 Samuel 18 in the MRS1T

1 Samuel 18 in the NAA

1 Samuel 18 in the NASB

1 Samuel 18 in the NBLA

1 Samuel 18 in the NBS

1 Samuel 18 in the NBVTP

1 Samuel 18 in the NET2

1 Samuel 18 in the NIV11

1 Samuel 18 in the NNT

1 Samuel 18 in the NNT2

1 Samuel 18 in the NNT3

1 Samuel 18 in the PDDPT

1 Samuel 18 in the PFNT

1 Samuel 18 in the RMNT

1 Samuel 18 in the SBIAS

1 Samuel 18 in the SBIBS

1 Samuel 18 in the SBIBS2

1 Samuel 18 in the SBICS

1 Samuel 18 in the SBIDS

1 Samuel 18 in the SBIGS

1 Samuel 18 in the SBIHS

1 Samuel 18 in the SBIIS

1 Samuel 18 in the SBIIS2

1 Samuel 18 in the SBIIS3

1 Samuel 18 in the SBIKS

1 Samuel 18 in the SBIKS2

1 Samuel 18 in the SBIMS

1 Samuel 18 in the SBIOS

1 Samuel 18 in the SBIPS

1 Samuel 18 in the SBISS

1 Samuel 18 in the SBITS

1 Samuel 18 in the SBITS2

1 Samuel 18 in the SBITS3

1 Samuel 18 in the SBITS4

1 Samuel 18 in the SBIUS

1 Samuel 18 in the SBIVS

1 Samuel 18 in the SBT

1 Samuel 18 in the SBT1E

1 Samuel 18 in the SCHL

1 Samuel 18 in the SNT

1 Samuel 18 in the SUSU

1 Samuel 18 in the SUSU2

1 Samuel 18 in the SYNO

1 Samuel 18 in the TBIAOTANT

1 Samuel 18 in the TBT1E

1 Samuel 18 in the TBT1E2

1 Samuel 18 in the TFTIP

1 Samuel 18 in the TFTU

1 Samuel 18 in the TGNTATF3T

1 Samuel 18 in the THAI

1 Samuel 18 in the TNFD

1 Samuel 18 in the TNT

1 Samuel 18 in the TNTIK

1 Samuel 18 in the TNTIL

1 Samuel 18 in the TNTIN

1 Samuel 18 in the TNTIP

1 Samuel 18 in the TNTIZ

1 Samuel 18 in the TOMA

1 Samuel 18 in the TTENT

1 Samuel 18 in the UBG

1 Samuel 18 in the UGV

1 Samuel 18 in the UGV2

1 Samuel 18 in the UGV3

1 Samuel 18 in the VBL

1 Samuel 18 in the VDCC

1 Samuel 18 in the YALU

1 Samuel 18 in the YAPE

1 Samuel 18 in the YBVTP

1 Samuel 18 in the ZBP