1 Samuel 28 (BOGWICC)

1 Mʼmasiku amenewo Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo kuti akamenyane ndi Aisraeli. Akisi anawuza Davide kuti, “Udziwe kuti iwe pamodzi ndi anthu ako mudzapita nane ku nkhondo.” 2 Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.”Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.” 3 Nthawi imeneyi nʼkuti Samueli atamwalira, ndipo Aisraeli onse anamulira namuyika mʼmanda ku mzinda wake wa Rama. Sauli anali atachotsa mʼdzikomo anthu owombeza mawula ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. 4 Tsono Afilisti anasonkhana nabwera kudzamanga misasa yawo ku Sunemu. Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kumanga misasa yawo ku Gilibowa. 5 Sauli ataona gulu lankhondo la Afilisti anaopa ndipo ananjenjemera kwambiri. 6 Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri. 7 Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, “Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye.”Nduna zakezo zinamuyankha kuti, “Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori.” 8 Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.” 9 Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?” 10 Koma Sauli analonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Yehova wamoyo, iweyo sudzalangidwa chifukwa cha zimenezi.” 11 Kenaka mkaziyo anafunsa, “Ndikuyitanireni yani?”Iye anati, “Undiyitanire Samueli.” 12 Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!” 13 Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?”Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.” 14 Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?”Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.”Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi. 15 Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?”Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.” 16 Samueli anati, “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa ine, pakuti tsopano Yehova wakufulatira ndipo wasanduka mdani wako? 17 Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide. 18 Yehova wachita zimenezi lero chifukwa sunamvere mawu ake ndipo sunawawonongeretu Aamaleki. 19 Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.” 20 Nthawi yomweyo Sauli anagwa pansi atadzazidwa ndi mantha chifukwa cha mawu a Samueli. Analibenso mphamvu, pakuti sanadye tsiku lonse. 21 Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza. 22 Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.” 23 Iye anakana ndipo anati, “Ayi, ine sindidya.”Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo anamuwumiriza, ndipo anawamvera. Choncho anadzuka pansi nakhala pa bedi. 24 Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti. 25 Tsono anapereka bulediyo kwa Sauli ndi nduna zake ndipo anadya. Pambuyo pake ananyamuka kupita kwawo usiku womwewo.

In Other Versions

1 Samuel 28 in the ANGEFD

1 Samuel 28 in the ANTPNG2D

1 Samuel 28 in the AS21

1 Samuel 28 in the BAGH

1 Samuel 28 in the BBPNG

1 Samuel 28 in the BBT1E

1 Samuel 28 in the BDS

1 Samuel 28 in the BEV

1 Samuel 28 in the BHAD

1 Samuel 28 in the BIB

1 Samuel 28 in the BLPT

1 Samuel 28 in the BNT

1 Samuel 28 in the BNTABOOT

1 Samuel 28 in the BNTLV

1 Samuel 28 in the BOATCB

1 Samuel 28 in the BOATCB2

1 Samuel 28 in the BOBCV

1 Samuel 28 in the BOCNT

1 Samuel 28 in the BOECS

1 Samuel 28 in the BOHCB

1 Samuel 28 in the BOHCV

1 Samuel 28 in the BOHLNT

1 Samuel 28 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 28 in the BOICB

1 Samuel 28 in the BOILNTAP

1 Samuel 28 in the BOITCV

1 Samuel 28 in the BOKCV

1 Samuel 28 in the BOKCV2

1 Samuel 28 in the BOKHWOG

1 Samuel 28 in the BOKSSV

1 Samuel 28 in the BOLCB

1 Samuel 28 in the BOLCB2

1 Samuel 28 in the BOMCV

1 Samuel 28 in the BONAV

1 Samuel 28 in the BONCB

1 Samuel 28 in the BONLT

1 Samuel 28 in the BONUT2

1 Samuel 28 in the BOPLNT

1 Samuel 28 in the BOSCB

1 Samuel 28 in the BOSNC

1 Samuel 28 in the BOTLNT

1 Samuel 28 in the BOVCB

1 Samuel 28 in the BOYCB

1 Samuel 28 in the BPBB

1 Samuel 28 in the BPH

1 Samuel 28 in the BSB

1 Samuel 28 in the CCB

1 Samuel 28 in the CUV

1 Samuel 28 in the CUVS

1 Samuel 28 in the DBT

1 Samuel 28 in the DGDNT

1 Samuel 28 in the DHNT

1 Samuel 28 in the DNT

1 Samuel 28 in the ELBE

1 Samuel 28 in the EMTV

1 Samuel 28 in the ESV

1 Samuel 28 in the FBV

1 Samuel 28 in the FEB

1 Samuel 28 in the GGMNT

1 Samuel 28 in the GNT

1 Samuel 28 in the HARY

1 Samuel 28 in the HNT

1 Samuel 28 in the IRVA

1 Samuel 28 in the IRVB

1 Samuel 28 in the IRVG

1 Samuel 28 in the IRVH

1 Samuel 28 in the IRVK

1 Samuel 28 in the IRVM

1 Samuel 28 in the IRVM2

1 Samuel 28 in the IRVO

1 Samuel 28 in the IRVP

1 Samuel 28 in the IRVT

1 Samuel 28 in the IRVT2

1 Samuel 28 in the IRVU

1 Samuel 28 in the ISVN

1 Samuel 28 in the JSNT

1 Samuel 28 in the KAPI

1 Samuel 28 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 28 in the KBV

1 Samuel 28 in the KJV

1 Samuel 28 in the KNFD

1 Samuel 28 in the LBA

1 Samuel 28 in the LBLA

1 Samuel 28 in the LNT

1 Samuel 28 in the LSV

1 Samuel 28 in the MAAL

1 Samuel 28 in the MBV

1 Samuel 28 in the MBV2

1 Samuel 28 in the MHNT

1 Samuel 28 in the MKNFD

1 Samuel 28 in the MNG

1 Samuel 28 in the MNT

1 Samuel 28 in the MNT2

1 Samuel 28 in the MRS1T

1 Samuel 28 in the NAA

1 Samuel 28 in the NASB

1 Samuel 28 in the NBLA

1 Samuel 28 in the NBS

1 Samuel 28 in the NBVTP

1 Samuel 28 in the NET2

1 Samuel 28 in the NIV11

1 Samuel 28 in the NNT

1 Samuel 28 in the NNT2

1 Samuel 28 in the NNT3

1 Samuel 28 in the PDDPT

1 Samuel 28 in the PFNT

1 Samuel 28 in the RMNT

1 Samuel 28 in the SBIAS

1 Samuel 28 in the SBIBS

1 Samuel 28 in the SBIBS2

1 Samuel 28 in the SBICS

1 Samuel 28 in the SBIDS

1 Samuel 28 in the SBIGS

1 Samuel 28 in the SBIHS

1 Samuel 28 in the SBIIS

1 Samuel 28 in the SBIIS2

1 Samuel 28 in the SBIIS3

1 Samuel 28 in the SBIKS

1 Samuel 28 in the SBIKS2

1 Samuel 28 in the SBIMS

1 Samuel 28 in the SBIOS

1 Samuel 28 in the SBIPS

1 Samuel 28 in the SBISS

1 Samuel 28 in the SBITS

1 Samuel 28 in the SBITS2

1 Samuel 28 in the SBITS3

1 Samuel 28 in the SBITS4

1 Samuel 28 in the SBIUS

1 Samuel 28 in the SBIVS

1 Samuel 28 in the SBT

1 Samuel 28 in the SBT1E

1 Samuel 28 in the SCHL

1 Samuel 28 in the SNT

1 Samuel 28 in the SUSU

1 Samuel 28 in the SUSU2

1 Samuel 28 in the SYNO

1 Samuel 28 in the TBIAOTANT

1 Samuel 28 in the TBT1E

1 Samuel 28 in the TBT1E2

1 Samuel 28 in the TFTIP

1 Samuel 28 in the TFTU

1 Samuel 28 in the TGNTATF3T

1 Samuel 28 in the THAI

1 Samuel 28 in the TNFD

1 Samuel 28 in the TNT

1 Samuel 28 in the TNTIK

1 Samuel 28 in the TNTIL

1 Samuel 28 in the TNTIN

1 Samuel 28 in the TNTIP

1 Samuel 28 in the TNTIZ

1 Samuel 28 in the TOMA

1 Samuel 28 in the TTENT

1 Samuel 28 in the UBG

1 Samuel 28 in the UGV

1 Samuel 28 in the UGV2

1 Samuel 28 in the UGV3

1 Samuel 28 in the VBL

1 Samuel 28 in the VDCC

1 Samuel 28 in the YALU

1 Samuel 28 in the YAPE

1 Samuel 28 in the YBVTP

1 Samuel 28 in the ZBP