1 Thessalonians 4 (BOGWICC)

1 Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. 2 Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu. 3 Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; 4 aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, 5 osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. 6 Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. 7 Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. 8 Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera. 9 Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. 10 Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale. 11 Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. 12 Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense. 13 Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. 14 Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. 15 Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. 16 Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17 Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. 18 Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

In Other Versions

1 Thessalonians 4 in the ANGEFD

1 Thessalonians 4 in the ANTPNG2D

1 Thessalonians 4 in the AS21

1 Thessalonians 4 in the BAGH

1 Thessalonians 4 in the BBPNG

1 Thessalonians 4 in the BBT1E

1 Thessalonians 4 in the BDS

1 Thessalonians 4 in the BEV

1 Thessalonians 4 in the BHAD

1 Thessalonians 4 in the BIB

1 Thessalonians 4 in the BLPT

1 Thessalonians 4 in the BNT

1 Thessalonians 4 in the BNTABOOT

1 Thessalonians 4 in the BNTLV

1 Thessalonians 4 in the BOATCB

1 Thessalonians 4 in the BOATCB2

1 Thessalonians 4 in the BOBCV

1 Thessalonians 4 in the BOCNT

1 Thessalonians 4 in the BOECS

1 Thessalonians 4 in the BOHCB

1 Thessalonians 4 in the BOHCV

1 Thessalonians 4 in the BOHLNT

1 Thessalonians 4 in the BOHNTLTAL

1 Thessalonians 4 in the BOICB

1 Thessalonians 4 in the BOILNTAP

1 Thessalonians 4 in the BOITCV

1 Thessalonians 4 in the BOKCV

1 Thessalonians 4 in the BOKCV2

1 Thessalonians 4 in the BOKHWOG

1 Thessalonians 4 in the BOKSSV

1 Thessalonians 4 in the BOLCB

1 Thessalonians 4 in the BOLCB2

1 Thessalonians 4 in the BOMCV

1 Thessalonians 4 in the BONAV

1 Thessalonians 4 in the BONCB

1 Thessalonians 4 in the BONLT

1 Thessalonians 4 in the BONUT2

1 Thessalonians 4 in the BOPLNT

1 Thessalonians 4 in the BOSCB

1 Thessalonians 4 in the BOSNC

1 Thessalonians 4 in the BOTLNT

1 Thessalonians 4 in the BOVCB

1 Thessalonians 4 in the BOYCB

1 Thessalonians 4 in the BPBB

1 Thessalonians 4 in the BPH

1 Thessalonians 4 in the BSB

1 Thessalonians 4 in the CCB

1 Thessalonians 4 in the CUV

1 Thessalonians 4 in the CUVS

1 Thessalonians 4 in the DBT

1 Thessalonians 4 in the DGDNT

1 Thessalonians 4 in the DHNT

1 Thessalonians 4 in the DNT

1 Thessalonians 4 in the ELBE

1 Thessalonians 4 in the EMTV

1 Thessalonians 4 in the ESV

1 Thessalonians 4 in the FBV

1 Thessalonians 4 in the FEB

1 Thessalonians 4 in the GGMNT

1 Thessalonians 4 in the GNT

1 Thessalonians 4 in the HARY

1 Thessalonians 4 in the HNT

1 Thessalonians 4 in the IRVA

1 Thessalonians 4 in the IRVB

1 Thessalonians 4 in the IRVG

1 Thessalonians 4 in the IRVH

1 Thessalonians 4 in the IRVK

1 Thessalonians 4 in the IRVM

1 Thessalonians 4 in the IRVM2

1 Thessalonians 4 in the IRVO

1 Thessalonians 4 in the IRVP

1 Thessalonians 4 in the IRVT

1 Thessalonians 4 in the IRVT2

1 Thessalonians 4 in the IRVU

1 Thessalonians 4 in the ISVN

1 Thessalonians 4 in the JSNT

1 Thessalonians 4 in the KAPI

1 Thessalonians 4 in the KBT1ETNIK

1 Thessalonians 4 in the KBV

1 Thessalonians 4 in the KJV

1 Thessalonians 4 in the KNFD

1 Thessalonians 4 in the LBA

1 Thessalonians 4 in the LBLA

1 Thessalonians 4 in the LNT

1 Thessalonians 4 in the LSV

1 Thessalonians 4 in the MAAL

1 Thessalonians 4 in the MBV

1 Thessalonians 4 in the MBV2

1 Thessalonians 4 in the MHNT

1 Thessalonians 4 in the MKNFD

1 Thessalonians 4 in the MNG

1 Thessalonians 4 in the MNT

1 Thessalonians 4 in the MNT2

1 Thessalonians 4 in the MRS1T

1 Thessalonians 4 in the NAA

1 Thessalonians 4 in the NASB

1 Thessalonians 4 in the NBLA

1 Thessalonians 4 in the NBS

1 Thessalonians 4 in the NBVTP

1 Thessalonians 4 in the NET2

1 Thessalonians 4 in the NIV11

1 Thessalonians 4 in the NNT

1 Thessalonians 4 in the NNT2

1 Thessalonians 4 in the NNT3

1 Thessalonians 4 in the PDDPT

1 Thessalonians 4 in the PFNT

1 Thessalonians 4 in the RMNT

1 Thessalonians 4 in the SBIAS

1 Thessalonians 4 in the SBIBS

1 Thessalonians 4 in the SBIBS2

1 Thessalonians 4 in the SBICS

1 Thessalonians 4 in the SBIDS

1 Thessalonians 4 in the SBIGS

1 Thessalonians 4 in the SBIHS

1 Thessalonians 4 in the SBIIS

1 Thessalonians 4 in the SBIIS2

1 Thessalonians 4 in the SBIIS3

1 Thessalonians 4 in the SBIKS

1 Thessalonians 4 in the SBIKS2

1 Thessalonians 4 in the SBIMS

1 Thessalonians 4 in the SBIOS

1 Thessalonians 4 in the SBIPS

1 Thessalonians 4 in the SBISS

1 Thessalonians 4 in the SBITS

1 Thessalonians 4 in the SBITS2

1 Thessalonians 4 in the SBITS3

1 Thessalonians 4 in the SBITS4

1 Thessalonians 4 in the SBIUS

1 Thessalonians 4 in the SBIVS

1 Thessalonians 4 in the SBT

1 Thessalonians 4 in the SBT1E

1 Thessalonians 4 in the SCHL

1 Thessalonians 4 in the SNT

1 Thessalonians 4 in the SUSU

1 Thessalonians 4 in the SUSU2

1 Thessalonians 4 in the SYNO

1 Thessalonians 4 in the TBIAOTANT

1 Thessalonians 4 in the TBT1E

1 Thessalonians 4 in the TBT1E2

1 Thessalonians 4 in the TFTIP

1 Thessalonians 4 in the TFTU

1 Thessalonians 4 in the TGNTATF3T

1 Thessalonians 4 in the THAI

1 Thessalonians 4 in the TNFD

1 Thessalonians 4 in the TNT

1 Thessalonians 4 in the TNTIK

1 Thessalonians 4 in the TNTIL

1 Thessalonians 4 in the TNTIN

1 Thessalonians 4 in the TNTIP

1 Thessalonians 4 in the TNTIZ

1 Thessalonians 4 in the TOMA

1 Thessalonians 4 in the TTENT

1 Thessalonians 4 in the UBG

1 Thessalonians 4 in the UGV

1 Thessalonians 4 in the UGV2

1 Thessalonians 4 in the UGV3

1 Thessalonians 4 in the VBL

1 Thessalonians 4 in the VDCC

1 Thessalonians 4 in the YALU

1 Thessalonians 4 in the YAPE

1 Thessalonians 4 in the YBVTP

1 Thessalonians 4 in the ZBP