2 Chronicles 26 (BOGWICC)
1 Kenaka anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya amene anali wa zaka 16, namuyika kukhala mfumu mʼmalo mwa Amaziya abambo ake. 2 Iye anamanganso mzinda wa Eloti ndi kuwubwezeranso ku Yuda abambo ake atamwalira. 3 Uziya anali wa zaka 16 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 70. Dzina la amayi ake linali Yekoliya wa ku Yerusalemu. 4 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake. 5 Iye anapembedza Mulungu nthawi ya Zekariya, amene ankamulangiza za kuopa Mulungu amene anamupatsa chipambano. 6 Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti. 7 Mulungu anamuthandiza polimbana ndi Afilisti ndi Aarabu amene amakhala ku Guri-Baala ndiponso polimbana ndi Ameuni. 8 Aamoni ankabweretsa msonkho kwa Uziya ndipo mbiri yake inamveka mpaka ku malire a dziko la Igupto chifukwa anali wamphamvu kwambiri. 9 Uziya anamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata Chapangodya, ku Chigwa cha Chipata ndi pokhotera mpanda, ndipo anayikamo chitetezo. 10 Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka. 11 Uziya anali ndi gulu lankhondo lophunzitsidwa bwino, lokonzekera kupita ku nkhondo mʼmagulu monga mwa chiwerengero chawo chimene mlembi Yeiyeli ndi Maaseya anasonkhanitsa motsogozedwa ndi Hananiya mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. 12 Chiwerengero chonse cha atsogoleri a mʼmabanja oyangʼanira anthu ochita nkhondo chinali 2,600. 13 Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake. 14 Uziya anawapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zipewa zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta ndi miyala yogendera. 15 Mu Yerusalemu anapanga makina okonzedwa ndi anthu aluso amene amagwiritsidwa ntchito pa malo otetezera a pa nsanja ndi pa ngodya kuponyera mivi ndi kugubuduzira miyala. Mbiri yake inamveka kutali ndi ponseponse pakuti anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu kwambiri. 16 Koma pamene Uziya anakhala wamphamvu kwambiri, kunyada kwake kunamuwononga. Iye sanakhulupirike kwa Yehova Mulungu wake, ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova kukafukiza lubani pa guwa lofukizira. 17 Wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova ena 80 olimba mtima anamutsatira. 18 Iwo anatsutsana naye ndipo anati, “Sibwino kuti inu mfumu muzifukiza lubani koma zidzukulu za Aaroni, zimene zinapatulidwa kuti zizifukiza lubani. Chokani pa malo opatulika ano, pakuti inu mwakhala osakhulupirika, ndipo simudzalemekezedwa ndi Yehova Mulungu.” 19 Uziya, amene anali ndi chofukizira mʼmanja mwake wokonzeka kuti afukize lubani, anapsa mtima. Iye anakwiyira ansembewo. Ndipo ansembe aja akuona patsogolo pa guwa lofukizira lubani mʼNyumba ya Mulungu, khate linayamba pamphumi pake. 20 Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga. 21 Mfumu Uziya anali ndi khate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye amakhala mʼnyumba ya yekha ngati wakhate, ndipo samalowa mʼNyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndiye amayangʼanira nyumba yaufumu ndipo ankalamulira anthu a mʼdzikomo. 22 Ntchito zina za mfumu Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 23 Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
In Other Versions
2 Chronicles 26 in the ANGEFD
2 Chronicles 26 in the ANTPNG2D
2 Chronicles 26 in the AS21
2 Chronicles 26 in the BAGH
2 Chronicles 26 in the BBPNG
2 Chronicles 26 in the BBT1E
2 Chronicles 26 in the BDS
2 Chronicles 26 in the BEV
2 Chronicles 26 in the BHAD
2 Chronicles 26 in the BIB
2 Chronicles 26 in the BLPT
2 Chronicles 26 in the BNT
2 Chronicles 26 in the BNTABOOT
2 Chronicles 26 in the BNTLV
2 Chronicles 26 in the BOATCB
2 Chronicles 26 in the BOATCB2
2 Chronicles 26 in the BOBCV
2 Chronicles 26 in the BOCNT
2 Chronicles 26 in the BOECS
2 Chronicles 26 in the BOHCB
2 Chronicles 26 in the BOHCV
2 Chronicles 26 in the BOHLNT
2 Chronicles 26 in the BOHNTLTAL
2 Chronicles 26 in the BOICB
2 Chronicles 26 in the BOILNTAP
2 Chronicles 26 in the BOITCV
2 Chronicles 26 in the BOKCV
2 Chronicles 26 in the BOKCV2
2 Chronicles 26 in the BOKHWOG
2 Chronicles 26 in the BOKSSV
2 Chronicles 26 in the BOLCB
2 Chronicles 26 in the BOLCB2
2 Chronicles 26 in the BOMCV
2 Chronicles 26 in the BONAV
2 Chronicles 26 in the BONCB
2 Chronicles 26 in the BONLT
2 Chronicles 26 in the BONUT2
2 Chronicles 26 in the BOPLNT
2 Chronicles 26 in the BOSCB
2 Chronicles 26 in the BOSNC
2 Chronicles 26 in the BOTLNT
2 Chronicles 26 in the BOVCB
2 Chronicles 26 in the BOYCB
2 Chronicles 26 in the BPBB
2 Chronicles 26 in the BPH
2 Chronicles 26 in the BSB
2 Chronicles 26 in the CCB
2 Chronicles 26 in the CUV
2 Chronicles 26 in the CUVS
2 Chronicles 26 in the DBT
2 Chronicles 26 in the DGDNT
2 Chronicles 26 in the DHNT
2 Chronicles 26 in the DNT
2 Chronicles 26 in the ELBE
2 Chronicles 26 in the EMTV
2 Chronicles 26 in the ESV
2 Chronicles 26 in the FBV
2 Chronicles 26 in the FEB
2 Chronicles 26 in the GGMNT
2 Chronicles 26 in the GNT
2 Chronicles 26 in the HARY
2 Chronicles 26 in the HNT
2 Chronicles 26 in the IRVA
2 Chronicles 26 in the IRVB
2 Chronicles 26 in the IRVG
2 Chronicles 26 in the IRVH
2 Chronicles 26 in the IRVK
2 Chronicles 26 in the IRVM
2 Chronicles 26 in the IRVM2
2 Chronicles 26 in the IRVO
2 Chronicles 26 in the IRVP
2 Chronicles 26 in the IRVT
2 Chronicles 26 in the IRVT2
2 Chronicles 26 in the IRVU
2 Chronicles 26 in the ISVN
2 Chronicles 26 in the JSNT
2 Chronicles 26 in the KAPI
2 Chronicles 26 in the KBT1ETNIK
2 Chronicles 26 in the KBV
2 Chronicles 26 in the KJV
2 Chronicles 26 in the KNFD
2 Chronicles 26 in the LBA
2 Chronicles 26 in the LBLA
2 Chronicles 26 in the LNT
2 Chronicles 26 in the LSV
2 Chronicles 26 in the MAAL
2 Chronicles 26 in the MBV
2 Chronicles 26 in the MBV2
2 Chronicles 26 in the MHNT
2 Chronicles 26 in the MKNFD
2 Chronicles 26 in the MNG
2 Chronicles 26 in the MNT
2 Chronicles 26 in the MNT2
2 Chronicles 26 in the MRS1T
2 Chronicles 26 in the NAA
2 Chronicles 26 in the NASB
2 Chronicles 26 in the NBLA
2 Chronicles 26 in the NBS
2 Chronicles 26 in the NBVTP
2 Chronicles 26 in the NET2
2 Chronicles 26 in the NIV11
2 Chronicles 26 in the NNT
2 Chronicles 26 in the NNT2
2 Chronicles 26 in the NNT3
2 Chronicles 26 in the PDDPT
2 Chronicles 26 in the PFNT
2 Chronicles 26 in the RMNT
2 Chronicles 26 in the SBIAS
2 Chronicles 26 in the SBIBS
2 Chronicles 26 in the SBIBS2
2 Chronicles 26 in the SBICS
2 Chronicles 26 in the SBIDS
2 Chronicles 26 in the SBIGS
2 Chronicles 26 in the SBIHS
2 Chronicles 26 in the SBIIS
2 Chronicles 26 in the SBIIS2
2 Chronicles 26 in the SBIIS3
2 Chronicles 26 in the SBIKS
2 Chronicles 26 in the SBIKS2
2 Chronicles 26 in the SBIMS
2 Chronicles 26 in the SBIOS
2 Chronicles 26 in the SBIPS
2 Chronicles 26 in the SBISS
2 Chronicles 26 in the SBITS
2 Chronicles 26 in the SBITS2
2 Chronicles 26 in the SBITS3
2 Chronicles 26 in the SBITS4
2 Chronicles 26 in the SBIUS
2 Chronicles 26 in the SBIVS
2 Chronicles 26 in the SBT
2 Chronicles 26 in the SBT1E
2 Chronicles 26 in the SCHL
2 Chronicles 26 in the SNT
2 Chronicles 26 in the SUSU
2 Chronicles 26 in the SUSU2
2 Chronicles 26 in the SYNO
2 Chronicles 26 in the TBIAOTANT
2 Chronicles 26 in the TBT1E
2 Chronicles 26 in the TBT1E2
2 Chronicles 26 in the TFTIP
2 Chronicles 26 in the TFTU
2 Chronicles 26 in the TGNTATF3T
2 Chronicles 26 in the THAI
2 Chronicles 26 in the TNFD
2 Chronicles 26 in the TNT
2 Chronicles 26 in the TNTIK
2 Chronicles 26 in the TNTIL
2 Chronicles 26 in the TNTIN
2 Chronicles 26 in the TNTIP
2 Chronicles 26 in the TNTIZ
2 Chronicles 26 in the TOMA
2 Chronicles 26 in the TTENT
2 Chronicles 26 in the UBG
2 Chronicles 26 in the UGV
2 Chronicles 26 in the UGV2
2 Chronicles 26 in the UGV3
2 Chronicles 26 in the VBL
2 Chronicles 26 in the VDCC
2 Chronicles 26 in the YALU
2 Chronicles 26 in the YAPE
2 Chronicles 26 in the YBVTP
2 Chronicles 26 in the ZBP