2 Chronicles 31 (BOGWICC)

1 Zonse zitatha, Aisraeli onse amene anali kumeneko anapita ku mizinda ya ku Yuda, nakaphwanya miyala yachipembedzo ndi kudula mitengo ya mafano a Asera. Iwo anakawononga malo achipembedzo ndi maguwa ansembe amene anali mʼdziko lonse la Yuda, Benjamini, Efereimu ndi Manase. Atawononga zonsezi, Aisraeli anabwerera ku mizinda yawo ndi ku malo awo. 2 Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova. 3 Kuchokera pa chuma chake, mfumu inapereka nsembe zopsereza za mmawa ndi madzulo ndiponso nsembe zopsereza za pa Chikondwerero cha Masabata, Chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndipo inakhazikitsa zikondwerero monga zinalembedwera mʼmalamulo a Yehova. 4 Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova. 5 Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse. 6 Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu. 7 Anayamba kuchita izi mwezi wachitatu ndipo anatsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. 8 Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli. 9 Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyi; 10 ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.” 11 Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika. 12 Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake. 13 Yehieli, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali oyangʼanira motsogozedwa ndi Konaniya ndi Simei, mʼbale wake. Iwowa anasankhidwa ndi mfumu Hezekiya ndi Azariya mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu. 14 Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika. 15 Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe. 16 Kuwonjezera apa, amagawira ana aamuna a zaka zitatu kapena kupitirira amene mayina awo anali mʼmbiri ya mibado yawo, amene adzalowe mʼNyumba ya Yehova kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku za magulu awo, molingana ndi udindo ndi magulu awo. 17 Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo. 18 Iwo anaphatikizanso ana onse aangʼono, akazi ndiponso ana aamuna ndi ana aakazi a gulu lonse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado yawo iyi, pakuti anakhulupirika pa kudzipatula okha. 19 Kunena za ansembe, zidzukulu za Aaroni, amene amakhala mʼminda yozungulira mizinda yawo kapena mzinda wina uliwonse, anthu anasankhidwa mowatchula mayina kuti azipereka magawo kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pawo ndiponso kwa onse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado ya Alevi. 20 Izi ndi zimene Hezekiya anachita mu Yuda monse, kuchita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21 Pa chilichonse chimene anachita pa ntchito ya Nyumba ya Mulungu ndi pa kumvera malangizo ndi malamulo, iye anafunafuna Mulungu wake ndipo anagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Ndipo zinthu zimamuyendera bwino.

In Other Versions

2 Chronicles 31 in the ANGEFD

2 Chronicles 31 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 31 in the AS21

2 Chronicles 31 in the BAGH

2 Chronicles 31 in the BBPNG

2 Chronicles 31 in the BBT1E

2 Chronicles 31 in the BDS

2 Chronicles 31 in the BEV

2 Chronicles 31 in the BHAD

2 Chronicles 31 in the BIB

2 Chronicles 31 in the BLPT

2 Chronicles 31 in the BNT

2 Chronicles 31 in the BNTABOOT

2 Chronicles 31 in the BNTLV

2 Chronicles 31 in the BOATCB

2 Chronicles 31 in the BOATCB2

2 Chronicles 31 in the BOBCV

2 Chronicles 31 in the BOCNT

2 Chronicles 31 in the BOECS

2 Chronicles 31 in the BOHCB

2 Chronicles 31 in the BOHCV

2 Chronicles 31 in the BOHLNT

2 Chronicles 31 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 31 in the BOICB

2 Chronicles 31 in the BOILNTAP

2 Chronicles 31 in the BOITCV

2 Chronicles 31 in the BOKCV

2 Chronicles 31 in the BOKCV2

2 Chronicles 31 in the BOKHWOG

2 Chronicles 31 in the BOKSSV

2 Chronicles 31 in the BOLCB

2 Chronicles 31 in the BOLCB2

2 Chronicles 31 in the BOMCV

2 Chronicles 31 in the BONAV

2 Chronicles 31 in the BONCB

2 Chronicles 31 in the BONLT

2 Chronicles 31 in the BONUT2

2 Chronicles 31 in the BOPLNT

2 Chronicles 31 in the BOSCB

2 Chronicles 31 in the BOSNC

2 Chronicles 31 in the BOTLNT

2 Chronicles 31 in the BOVCB

2 Chronicles 31 in the BOYCB

2 Chronicles 31 in the BPBB

2 Chronicles 31 in the BPH

2 Chronicles 31 in the BSB

2 Chronicles 31 in the CCB

2 Chronicles 31 in the CUV

2 Chronicles 31 in the CUVS

2 Chronicles 31 in the DBT

2 Chronicles 31 in the DGDNT

2 Chronicles 31 in the DHNT

2 Chronicles 31 in the DNT

2 Chronicles 31 in the ELBE

2 Chronicles 31 in the EMTV

2 Chronicles 31 in the ESV

2 Chronicles 31 in the FBV

2 Chronicles 31 in the FEB

2 Chronicles 31 in the GGMNT

2 Chronicles 31 in the GNT

2 Chronicles 31 in the HARY

2 Chronicles 31 in the HNT

2 Chronicles 31 in the IRVA

2 Chronicles 31 in the IRVB

2 Chronicles 31 in the IRVG

2 Chronicles 31 in the IRVH

2 Chronicles 31 in the IRVK

2 Chronicles 31 in the IRVM

2 Chronicles 31 in the IRVM2

2 Chronicles 31 in the IRVO

2 Chronicles 31 in the IRVP

2 Chronicles 31 in the IRVT

2 Chronicles 31 in the IRVT2

2 Chronicles 31 in the IRVU

2 Chronicles 31 in the ISVN

2 Chronicles 31 in the JSNT

2 Chronicles 31 in the KAPI

2 Chronicles 31 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 31 in the KBV

2 Chronicles 31 in the KJV

2 Chronicles 31 in the KNFD

2 Chronicles 31 in the LBA

2 Chronicles 31 in the LBLA

2 Chronicles 31 in the LNT

2 Chronicles 31 in the LSV

2 Chronicles 31 in the MAAL

2 Chronicles 31 in the MBV

2 Chronicles 31 in the MBV2

2 Chronicles 31 in the MHNT

2 Chronicles 31 in the MKNFD

2 Chronicles 31 in the MNG

2 Chronicles 31 in the MNT

2 Chronicles 31 in the MNT2

2 Chronicles 31 in the MRS1T

2 Chronicles 31 in the NAA

2 Chronicles 31 in the NASB

2 Chronicles 31 in the NBLA

2 Chronicles 31 in the NBS

2 Chronicles 31 in the NBVTP

2 Chronicles 31 in the NET2

2 Chronicles 31 in the NIV11

2 Chronicles 31 in the NNT

2 Chronicles 31 in the NNT2

2 Chronicles 31 in the NNT3

2 Chronicles 31 in the PDDPT

2 Chronicles 31 in the PFNT

2 Chronicles 31 in the RMNT

2 Chronicles 31 in the SBIAS

2 Chronicles 31 in the SBIBS

2 Chronicles 31 in the SBIBS2

2 Chronicles 31 in the SBICS

2 Chronicles 31 in the SBIDS

2 Chronicles 31 in the SBIGS

2 Chronicles 31 in the SBIHS

2 Chronicles 31 in the SBIIS

2 Chronicles 31 in the SBIIS2

2 Chronicles 31 in the SBIIS3

2 Chronicles 31 in the SBIKS

2 Chronicles 31 in the SBIKS2

2 Chronicles 31 in the SBIMS

2 Chronicles 31 in the SBIOS

2 Chronicles 31 in the SBIPS

2 Chronicles 31 in the SBISS

2 Chronicles 31 in the SBITS

2 Chronicles 31 in the SBITS2

2 Chronicles 31 in the SBITS3

2 Chronicles 31 in the SBITS4

2 Chronicles 31 in the SBIUS

2 Chronicles 31 in the SBIVS

2 Chronicles 31 in the SBT

2 Chronicles 31 in the SBT1E

2 Chronicles 31 in the SCHL

2 Chronicles 31 in the SNT

2 Chronicles 31 in the SUSU

2 Chronicles 31 in the SUSU2

2 Chronicles 31 in the SYNO

2 Chronicles 31 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 31 in the TBT1E

2 Chronicles 31 in the TBT1E2

2 Chronicles 31 in the TFTIP

2 Chronicles 31 in the TFTU

2 Chronicles 31 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 31 in the THAI

2 Chronicles 31 in the TNFD

2 Chronicles 31 in the TNT

2 Chronicles 31 in the TNTIK

2 Chronicles 31 in the TNTIL

2 Chronicles 31 in the TNTIN

2 Chronicles 31 in the TNTIP

2 Chronicles 31 in the TNTIZ

2 Chronicles 31 in the TOMA

2 Chronicles 31 in the TTENT

2 Chronicles 31 in the UBG

2 Chronicles 31 in the UGV

2 Chronicles 31 in the UGV2

2 Chronicles 31 in the UGV3

2 Chronicles 31 in the VBL

2 Chronicles 31 in the VDCC

2 Chronicles 31 in the YALU

2 Chronicles 31 in the YAPE

2 Chronicles 31 in the YBVTP

2 Chronicles 31 in the ZBP