2 Corinthians 8 (BOGWICC)

1 Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. 2 Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. 3 Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, 4 ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. 5 Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. 6 Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. 7 Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka. 8 Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. 9 Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere. 10 Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka. 11 Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo. 12 Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe. 13 Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. 14 Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, 15 monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.” 16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. 17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. 18 Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. 19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. 20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. 21 Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu. 22 Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. 23 Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. 24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.

In Other Versions

2 Corinthians 8 in the ANGEFD

2 Corinthians 8 in the ANTPNG2D

2 Corinthians 8 in the AS21

2 Corinthians 8 in the BAGH

2 Corinthians 8 in the BBPNG

2 Corinthians 8 in the BBT1E

2 Corinthians 8 in the BDS

2 Corinthians 8 in the BEV

2 Corinthians 8 in the BHAD

2 Corinthians 8 in the BIB

2 Corinthians 8 in the BLPT

2 Corinthians 8 in the BNT

2 Corinthians 8 in the BNTABOOT

2 Corinthians 8 in the BNTLV

2 Corinthians 8 in the BOATCB

2 Corinthians 8 in the BOATCB2

2 Corinthians 8 in the BOBCV

2 Corinthians 8 in the BOCNT

2 Corinthians 8 in the BOECS

2 Corinthians 8 in the BOHCB

2 Corinthians 8 in the BOHCV

2 Corinthians 8 in the BOHLNT

2 Corinthians 8 in the BOHNTLTAL

2 Corinthians 8 in the BOICB

2 Corinthians 8 in the BOILNTAP

2 Corinthians 8 in the BOITCV

2 Corinthians 8 in the BOKCV

2 Corinthians 8 in the BOKCV2

2 Corinthians 8 in the BOKHWOG

2 Corinthians 8 in the BOKSSV

2 Corinthians 8 in the BOLCB

2 Corinthians 8 in the BOLCB2

2 Corinthians 8 in the BOMCV

2 Corinthians 8 in the BONAV

2 Corinthians 8 in the BONCB

2 Corinthians 8 in the BONLT

2 Corinthians 8 in the BONUT2

2 Corinthians 8 in the BOPLNT

2 Corinthians 8 in the BOSCB

2 Corinthians 8 in the BOSNC

2 Corinthians 8 in the BOTLNT

2 Corinthians 8 in the BOVCB

2 Corinthians 8 in the BOYCB

2 Corinthians 8 in the BPBB

2 Corinthians 8 in the BPH

2 Corinthians 8 in the BSB

2 Corinthians 8 in the CCB

2 Corinthians 8 in the CUV

2 Corinthians 8 in the CUVS

2 Corinthians 8 in the DBT

2 Corinthians 8 in the DGDNT

2 Corinthians 8 in the DHNT

2 Corinthians 8 in the DNT

2 Corinthians 8 in the ELBE

2 Corinthians 8 in the EMTV

2 Corinthians 8 in the ESV

2 Corinthians 8 in the FBV

2 Corinthians 8 in the FEB

2 Corinthians 8 in the GGMNT

2 Corinthians 8 in the GNT

2 Corinthians 8 in the HARY

2 Corinthians 8 in the HNT

2 Corinthians 8 in the IRVA

2 Corinthians 8 in the IRVB

2 Corinthians 8 in the IRVG

2 Corinthians 8 in the IRVH

2 Corinthians 8 in the IRVK

2 Corinthians 8 in the IRVM

2 Corinthians 8 in the IRVM2

2 Corinthians 8 in the IRVO

2 Corinthians 8 in the IRVP

2 Corinthians 8 in the IRVT

2 Corinthians 8 in the IRVT2

2 Corinthians 8 in the IRVU

2 Corinthians 8 in the ISVN

2 Corinthians 8 in the JSNT

2 Corinthians 8 in the KAPI

2 Corinthians 8 in the KBT1ETNIK

2 Corinthians 8 in the KBV

2 Corinthians 8 in the KJV

2 Corinthians 8 in the KNFD

2 Corinthians 8 in the LBA

2 Corinthians 8 in the LBLA

2 Corinthians 8 in the LNT

2 Corinthians 8 in the LSV

2 Corinthians 8 in the MAAL

2 Corinthians 8 in the MBV

2 Corinthians 8 in the MBV2

2 Corinthians 8 in the MHNT

2 Corinthians 8 in the MKNFD

2 Corinthians 8 in the MNG

2 Corinthians 8 in the MNT

2 Corinthians 8 in the MNT2

2 Corinthians 8 in the MRS1T

2 Corinthians 8 in the NAA

2 Corinthians 8 in the NASB

2 Corinthians 8 in the NBLA

2 Corinthians 8 in the NBS

2 Corinthians 8 in the NBVTP

2 Corinthians 8 in the NET2

2 Corinthians 8 in the NIV11

2 Corinthians 8 in the NNT

2 Corinthians 8 in the NNT2

2 Corinthians 8 in the NNT3

2 Corinthians 8 in the PDDPT

2 Corinthians 8 in the PFNT

2 Corinthians 8 in the RMNT

2 Corinthians 8 in the SBIAS

2 Corinthians 8 in the SBIBS

2 Corinthians 8 in the SBIBS2

2 Corinthians 8 in the SBICS

2 Corinthians 8 in the SBIDS

2 Corinthians 8 in the SBIGS

2 Corinthians 8 in the SBIHS

2 Corinthians 8 in the SBIIS

2 Corinthians 8 in the SBIIS2

2 Corinthians 8 in the SBIIS3

2 Corinthians 8 in the SBIKS

2 Corinthians 8 in the SBIKS2

2 Corinthians 8 in the SBIMS

2 Corinthians 8 in the SBIOS

2 Corinthians 8 in the SBIPS

2 Corinthians 8 in the SBISS

2 Corinthians 8 in the SBITS

2 Corinthians 8 in the SBITS2

2 Corinthians 8 in the SBITS3

2 Corinthians 8 in the SBITS4

2 Corinthians 8 in the SBIUS

2 Corinthians 8 in the SBIVS

2 Corinthians 8 in the SBT

2 Corinthians 8 in the SBT1E

2 Corinthians 8 in the SCHL

2 Corinthians 8 in the SNT

2 Corinthians 8 in the SUSU

2 Corinthians 8 in the SUSU2

2 Corinthians 8 in the SYNO

2 Corinthians 8 in the TBIAOTANT

2 Corinthians 8 in the TBT1E

2 Corinthians 8 in the TBT1E2

2 Corinthians 8 in the TFTIP

2 Corinthians 8 in the TFTU

2 Corinthians 8 in the TGNTATF3T

2 Corinthians 8 in the THAI

2 Corinthians 8 in the TNFD

2 Corinthians 8 in the TNT

2 Corinthians 8 in the TNTIK

2 Corinthians 8 in the TNTIL

2 Corinthians 8 in the TNTIN

2 Corinthians 8 in the TNTIP

2 Corinthians 8 in the TNTIZ

2 Corinthians 8 in the TOMA

2 Corinthians 8 in the TTENT

2 Corinthians 8 in the UBG

2 Corinthians 8 in the UGV

2 Corinthians 8 in the UGV2

2 Corinthians 8 in the UGV3

2 Corinthians 8 in the VBL

2 Corinthians 8 in the VDCC

2 Corinthians 8 in the YALU

2 Corinthians 8 in the YAPE

2 Corinthians 8 in the YBVTP

2 Corinthians 8 in the ZBP