2 Kings 19 (BOGWICC)

1 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2 Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. 4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ” 5 Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ” 8 Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. 9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13 Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?” 14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo. 17 “Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18 Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.” 20 Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21 Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:“Namwali wa Ziyoniakukunyoza ndi kukuseka iwe.Mwana wamkazi wa Yerusalemuakupukusa mutu wake kumbuyo kwako. 22 Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?Kodi ndani amene wamufuwulira mawu akondi kumuyangʼana monyada?Wachitiratu izi Woyera wa Israeli! 23 Kudzera mwa amithenga akowonyoza Ambuye.Ndipo wanena kuti,‘Ndi magaleta ochulukandinakwera mapiri ataliatali,pa msonga za mapiri a Lebanoni.Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,mwa nkhalango yake yowirira kwambiri. 24 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendondipo ndinamwa madzi a kumeneko.Ndi mapazi angandawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ” 25 “ ‘Kodi sunamvepo?Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;tsopano ndachita kuti zichitikedi,iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwakukhala milu ya miyala. 26 Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.Ali ngati mbewu za mʼmunda,ngati udzu wanthete,ali ngati udzu womera pa denga,umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ” 27 “ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,kutuluka kwako ndi kulowa kwako,ndi mkwiyo wako pa Ine. 28 Chifukwa chakuti wandikwiyirandipo ndamva za mwano wako,ndidzakola mphuno yako ndi mbedzandi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,ndipo ndidzakubweza pokudzeretsanjira yomwe unadzera pobwera.’ 29 “Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake. 30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsaleadzazika mizu ndi kubereka zipatso. 31 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi. 32 “Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewukapena kuponyamo muvi.Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zakekapena kumanga nthumbira ya nkhondo. 33 Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;sadzalowa mu mzinda umenewu,akutero Yehova. 34 Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ” 35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko. 37 Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Kings 19 in the ANGEFD

2 Kings 19 in the ANTPNG2D

2 Kings 19 in the AS21

2 Kings 19 in the BAGH

2 Kings 19 in the BBPNG

2 Kings 19 in the BBT1E

2 Kings 19 in the BDS

2 Kings 19 in the BEV

2 Kings 19 in the BHAD

2 Kings 19 in the BIB

2 Kings 19 in the BLPT

2 Kings 19 in the BNT

2 Kings 19 in the BNTABOOT

2 Kings 19 in the BNTLV

2 Kings 19 in the BOATCB

2 Kings 19 in the BOATCB2

2 Kings 19 in the BOBCV

2 Kings 19 in the BOCNT

2 Kings 19 in the BOECS

2 Kings 19 in the BOHCB

2 Kings 19 in the BOHCV

2 Kings 19 in the BOHLNT

2 Kings 19 in the BOHNTLTAL

2 Kings 19 in the BOICB

2 Kings 19 in the BOILNTAP

2 Kings 19 in the BOITCV

2 Kings 19 in the BOKCV

2 Kings 19 in the BOKCV2

2 Kings 19 in the BOKHWOG

2 Kings 19 in the BOKSSV

2 Kings 19 in the BOLCB

2 Kings 19 in the BOLCB2

2 Kings 19 in the BOMCV

2 Kings 19 in the BONAV

2 Kings 19 in the BONCB

2 Kings 19 in the BONLT

2 Kings 19 in the BONUT2

2 Kings 19 in the BOPLNT

2 Kings 19 in the BOSCB

2 Kings 19 in the BOSNC

2 Kings 19 in the BOTLNT

2 Kings 19 in the BOVCB

2 Kings 19 in the BOYCB

2 Kings 19 in the BPBB

2 Kings 19 in the BPH

2 Kings 19 in the BSB

2 Kings 19 in the CCB

2 Kings 19 in the CUV

2 Kings 19 in the CUVS

2 Kings 19 in the DBT

2 Kings 19 in the DGDNT

2 Kings 19 in the DHNT

2 Kings 19 in the DNT

2 Kings 19 in the ELBE

2 Kings 19 in the EMTV

2 Kings 19 in the ESV

2 Kings 19 in the FBV

2 Kings 19 in the FEB

2 Kings 19 in the GGMNT

2 Kings 19 in the GNT

2 Kings 19 in the HARY

2 Kings 19 in the HNT

2 Kings 19 in the IRVA

2 Kings 19 in the IRVB

2 Kings 19 in the IRVG

2 Kings 19 in the IRVH

2 Kings 19 in the IRVK

2 Kings 19 in the IRVM

2 Kings 19 in the IRVM2

2 Kings 19 in the IRVO

2 Kings 19 in the IRVP

2 Kings 19 in the IRVT

2 Kings 19 in the IRVT2

2 Kings 19 in the IRVU

2 Kings 19 in the ISVN

2 Kings 19 in the JSNT

2 Kings 19 in the KAPI

2 Kings 19 in the KBT1ETNIK

2 Kings 19 in the KBV

2 Kings 19 in the KJV

2 Kings 19 in the KNFD

2 Kings 19 in the LBA

2 Kings 19 in the LBLA

2 Kings 19 in the LNT

2 Kings 19 in the LSV

2 Kings 19 in the MAAL

2 Kings 19 in the MBV

2 Kings 19 in the MBV2

2 Kings 19 in the MHNT

2 Kings 19 in the MKNFD

2 Kings 19 in the MNG

2 Kings 19 in the MNT

2 Kings 19 in the MNT2

2 Kings 19 in the MRS1T

2 Kings 19 in the NAA

2 Kings 19 in the NASB

2 Kings 19 in the NBLA

2 Kings 19 in the NBS

2 Kings 19 in the NBVTP

2 Kings 19 in the NET2

2 Kings 19 in the NIV11

2 Kings 19 in the NNT

2 Kings 19 in the NNT2

2 Kings 19 in the NNT3

2 Kings 19 in the PDDPT

2 Kings 19 in the PFNT

2 Kings 19 in the RMNT

2 Kings 19 in the SBIAS

2 Kings 19 in the SBIBS

2 Kings 19 in the SBIBS2

2 Kings 19 in the SBICS

2 Kings 19 in the SBIDS

2 Kings 19 in the SBIGS

2 Kings 19 in the SBIHS

2 Kings 19 in the SBIIS

2 Kings 19 in the SBIIS2

2 Kings 19 in the SBIIS3

2 Kings 19 in the SBIKS

2 Kings 19 in the SBIKS2

2 Kings 19 in the SBIMS

2 Kings 19 in the SBIOS

2 Kings 19 in the SBIPS

2 Kings 19 in the SBISS

2 Kings 19 in the SBITS

2 Kings 19 in the SBITS2

2 Kings 19 in the SBITS3

2 Kings 19 in the SBITS4

2 Kings 19 in the SBIUS

2 Kings 19 in the SBIVS

2 Kings 19 in the SBT

2 Kings 19 in the SBT1E

2 Kings 19 in the SCHL

2 Kings 19 in the SNT

2 Kings 19 in the SUSU

2 Kings 19 in the SUSU2

2 Kings 19 in the SYNO

2 Kings 19 in the TBIAOTANT

2 Kings 19 in the TBT1E

2 Kings 19 in the TBT1E2

2 Kings 19 in the TFTIP

2 Kings 19 in the TFTU

2 Kings 19 in the TGNTATF3T

2 Kings 19 in the THAI

2 Kings 19 in the TNFD

2 Kings 19 in the TNT

2 Kings 19 in the TNTIK

2 Kings 19 in the TNTIL

2 Kings 19 in the TNTIN

2 Kings 19 in the TNTIP

2 Kings 19 in the TNTIZ

2 Kings 19 in the TOMA

2 Kings 19 in the TTENT

2 Kings 19 in the UBG

2 Kings 19 in the UGV

2 Kings 19 in the UGV2

2 Kings 19 in the UGV3

2 Kings 19 in the VBL

2 Kings 19 in the VDCC

2 Kings 19 in the YALU

2 Kings 19 in the YAPE

2 Kings 19 in the YBVTP

2 Kings 19 in the ZBP