2 Kings 20 (BOGWICC)

1 Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.” 2 Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, 3 “Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri. 4 Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti, 5 “Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova. 6 Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ” 7 Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira. 8 Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?” 9 Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?” 10 Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.” 11 Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga. 12 Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo. 13 Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse. 14 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?”Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.” 15 Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?”Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.” 16 Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena: 17 Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova. 18 Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.” 19 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’ ” 20 Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 21 Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Kings 20 in the ANGEFD

2 Kings 20 in the ANTPNG2D

2 Kings 20 in the AS21

2 Kings 20 in the BAGH

2 Kings 20 in the BBPNG

2 Kings 20 in the BBT1E

2 Kings 20 in the BDS

2 Kings 20 in the BEV

2 Kings 20 in the BHAD

2 Kings 20 in the BIB

2 Kings 20 in the BLPT

2 Kings 20 in the BNT

2 Kings 20 in the BNTABOOT

2 Kings 20 in the BNTLV

2 Kings 20 in the BOATCB

2 Kings 20 in the BOATCB2

2 Kings 20 in the BOBCV

2 Kings 20 in the BOCNT

2 Kings 20 in the BOECS

2 Kings 20 in the BOHCB

2 Kings 20 in the BOHCV

2 Kings 20 in the BOHLNT

2 Kings 20 in the BOHNTLTAL

2 Kings 20 in the BOICB

2 Kings 20 in the BOILNTAP

2 Kings 20 in the BOITCV

2 Kings 20 in the BOKCV

2 Kings 20 in the BOKCV2

2 Kings 20 in the BOKHWOG

2 Kings 20 in the BOKSSV

2 Kings 20 in the BOLCB

2 Kings 20 in the BOLCB2

2 Kings 20 in the BOMCV

2 Kings 20 in the BONAV

2 Kings 20 in the BONCB

2 Kings 20 in the BONLT

2 Kings 20 in the BONUT2

2 Kings 20 in the BOPLNT

2 Kings 20 in the BOSCB

2 Kings 20 in the BOSNC

2 Kings 20 in the BOTLNT

2 Kings 20 in the BOVCB

2 Kings 20 in the BOYCB

2 Kings 20 in the BPBB

2 Kings 20 in the BPH

2 Kings 20 in the BSB

2 Kings 20 in the CCB

2 Kings 20 in the CUV

2 Kings 20 in the CUVS

2 Kings 20 in the DBT

2 Kings 20 in the DGDNT

2 Kings 20 in the DHNT

2 Kings 20 in the DNT

2 Kings 20 in the ELBE

2 Kings 20 in the EMTV

2 Kings 20 in the ESV

2 Kings 20 in the FBV

2 Kings 20 in the FEB

2 Kings 20 in the GGMNT

2 Kings 20 in the GNT

2 Kings 20 in the HARY

2 Kings 20 in the HNT

2 Kings 20 in the IRVA

2 Kings 20 in the IRVB

2 Kings 20 in the IRVG

2 Kings 20 in the IRVH

2 Kings 20 in the IRVK

2 Kings 20 in the IRVM

2 Kings 20 in the IRVM2

2 Kings 20 in the IRVO

2 Kings 20 in the IRVP

2 Kings 20 in the IRVT

2 Kings 20 in the IRVT2

2 Kings 20 in the IRVU

2 Kings 20 in the ISVN

2 Kings 20 in the JSNT

2 Kings 20 in the KAPI

2 Kings 20 in the KBT1ETNIK

2 Kings 20 in the KBV

2 Kings 20 in the KJV

2 Kings 20 in the KNFD

2 Kings 20 in the LBA

2 Kings 20 in the LBLA

2 Kings 20 in the LNT

2 Kings 20 in the LSV

2 Kings 20 in the MAAL

2 Kings 20 in the MBV

2 Kings 20 in the MBV2

2 Kings 20 in the MHNT

2 Kings 20 in the MKNFD

2 Kings 20 in the MNG

2 Kings 20 in the MNT

2 Kings 20 in the MNT2

2 Kings 20 in the MRS1T

2 Kings 20 in the NAA

2 Kings 20 in the NASB

2 Kings 20 in the NBLA

2 Kings 20 in the NBS

2 Kings 20 in the NBVTP

2 Kings 20 in the NET2

2 Kings 20 in the NIV11

2 Kings 20 in the NNT

2 Kings 20 in the NNT2

2 Kings 20 in the NNT3

2 Kings 20 in the PDDPT

2 Kings 20 in the PFNT

2 Kings 20 in the RMNT

2 Kings 20 in the SBIAS

2 Kings 20 in the SBIBS

2 Kings 20 in the SBIBS2

2 Kings 20 in the SBICS

2 Kings 20 in the SBIDS

2 Kings 20 in the SBIGS

2 Kings 20 in the SBIHS

2 Kings 20 in the SBIIS

2 Kings 20 in the SBIIS2

2 Kings 20 in the SBIIS3

2 Kings 20 in the SBIKS

2 Kings 20 in the SBIKS2

2 Kings 20 in the SBIMS

2 Kings 20 in the SBIOS

2 Kings 20 in the SBIPS

2 Kings 20 in the SBISS

2 Kings 20 in the SBITS

2 Kings 20 in the SBITS2

2 Kings 20 in the SBITS3

2 Kings 20 in the SBITS4

2 Kings 20 in the SBIUS

2 Kings 20 in the SBIVS

2 Kings 20 in the SBT

2 Kings 20 in the SBT1E

2 Kings 20 in the SCHL

2 Kings 20 in the SNT

2 Kings 20 in the SUSU

2 Kings 20 in the SUSU2

2 Kings 20 in the SYNO

2 Kings 20 in the TBIAOTANT

2 Kings 20 in the TBT1E

2 Kings 20 in the TBT1E2

2 Kings 20 in the TFTIP

2 Kings 20 in the TFTU

2 Kings 20 in the TGNTATF3T

2 Kings 20 in the THAI

2 Kings 20 in the TNFD

2 Kings 20 in the TNT

2 Kings 20 in the TNTIK

2 Kings 20 in the TNTIL

2 Kings 20 in the TNTIN

2 Kings 20 in the TNTIP

2 Kings 20 in the TNTIZ

2 Kings 20 in the TOMA

2 Kings 20 in the TTENT

2 Kings 20 in the UBG

2 Kings 20 in the UGV

2 Kings 20 in the UGV2

2 Kings 20 in the UGV3

2 Kings 20 in the VBL

2 Kings 20 in the VDCC

2 Kings 20 in the YALU

2 Kings 20 in the YAPE

2 Kings 20 in the YBVTP

2 Kings 20 in the ZBP