2 Peter 2 (BOGWICC)

1 Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. 2 Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. 3 Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira. 4 Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. 5 Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. 6 Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. 7 Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. 8 (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). 9 Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. 10 Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro.Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. 11 Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. 12 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa. 13 Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. 14 Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! 15 Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. 16 Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo. 17 Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani. 18 Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa. 19 Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira. 20 Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba. 21 Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa. 22 Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”

In Other Versions

2 Peter 2 in the ANGEFD

2 Peter 2 in the ANTPNG2D

2 Peter 2 in the AS21

2 Peter 2 in the BAGH

2 Peter 2 in the BBPNG

2 Peter 2 in the BBT1E

2 Peter 2 in the BDS

2 Peter 2 in the BEV

2 Peter 2 in the BHAD

2 Peter 2 in the BIB

2 Peter 2 in the BLPT

2 Peter 2 in the BNT

2 Peter 2 in the BNTABOOT

2 Peter 2 in the BNTLV

2 Peter 2 in the BOATCB

2 Peter 2 in the BOATCB2

2 Peter 2 in the BOBCV

2 Peter 2 in the BOCNT

2 Peter 2 in the BOECS

2 Peter 2 in the BOHCB

2 Peter 2 in the BOHCV

2 Peter 2 in the BOHLNT

2 Peter 2 in the BOHNTLTAL

2 Peter 2 in the BOICB

2 Peter 2 in the BOILNTAP

2 Peter 2 in the BOITCV

2 Peter 2 in the BOKCV

2 Peter 2 in the BOKCV2

2 Peter 2 in the BOKHWOG

2 Peter 2 in the BOKSSV

2 Peter 2 in the BOLCB

2 Peter 2 in the BOLCB2

2 Peter 2 in the BOMCV

2 Peter 2 in the BONAV

2 Peter 2 in the BONCB

2 Peter 2 in the BONLT

2 Peter 2 in the BONUT2

2 Peter 2 in the BOPLNT

2 Peter 2 in the BOSCB

2 Peter 2 in the BOSNC

2 Peter 2 in the BOTLNT

2 Peter 2 in the BOVCB

2 Peter 2 in the BOYCB

2 Peter 2 in the BPBB

2 Peter 2 in the BPH

2 Peter 2 in the BSB

2 Peter 2 in the CCB

2 Peter 2 in the CUV

2 Peter 2 in the CUVS

2 Peter 2 in the DBT

2 Peter 2 in the DGDNT

2 Peter 2 in the DHNT

2 Peter 2 in the DNT

2 Peter 2 in the ELBE

2 Peter 2 in the EMTV

2 Peter 2 in the ESV

2 Peter 2 in the FBV

2 Peter 2 in the FEB

2 Peter 2 in the GGMNT

2 Peter 2 in the GNT

2 Peter 2 in the HARY

2 Peter 2 in the HNT

2 Peter 2 in the IRVA

2 Peter 2 in the IRVB

2 Peter 2 in the IRVG

2 Peter 2 in the IRVH

2 Peter 2 in the IRVK

2 Peter 2 in the IRVM

2 Peter 2 in the IRVM2

2 Peter 2 in the IRVO

2 Peter 2 in the IRVP

2 Peter 2 in the IRVT

2 Peter 2 in the IRVT2

2 Peter 2 in the IRVU

2 Peter 2 in the ISVN

2 Peter 2 in the JSNT

2 Peter 2 in the KAPI

2 Peter 2 in the KBT1ETNIK

2 Peter 2 in the KBV

2 Peter 2 in the KJV

2 Peter 2 in the KNFD

2 Peter 2 in the LBA

2 Peter 2 in the LBLA

2 Peter 2 in the LNT

2 Peter 2 in the LSV

2 Peter 2 in the MAAL

2 Peter 2 in the MBV

2 Peter 2 in the MBV2

2 Peter 2 in the MHNT

2 Peter 2 in the MKNFD

2 Peter 2 in the MNG

2 Peter 2 in the MNT

2 Peter 2 in the MNT2

2 Peter 2 in the MRS1T

2 Peter 2 in the NAA

2 Peter 2 in the NASB

2 Peter 2 in the NBLA

2 Peter 2 in the NBS

2 Peter 2 in the NBVTP

2 Peter 2 in the NET2

2 Peter 2 in the NIV11

2 Peter 2 in the NNT

2 Peter 2 in the NNT2

2 Peter 2 in the NNT3

2 Peter 2 in the PDDPT

2 Peter 2 in the PFNT

2 Peter 2 in the RMNT

2 Peter 2 in the SBIAS

2 Peter 2 in the SBIBS

2 Peter 2 in the SBIBS2

2 Peter 2 in the SBICS

2 Peter 2 in the SBIDS

2 Peter 2 in the SBIGS

2 Peter 2 in the SBIHS

2 Peter 2 in the SBIIS

2 Peter 2 in the SBIIS2

2 Peter 2 in the SBIIS3

2 Peter 2 in the SBIKS

2 Peter 2 in the SBIKS2

2 Peter 2 in the SBIMS

2 Peter 2 in the SBIOS

2 Peter 2 in the SBIPS

2 Peter 2 in the SBISS

2 Peter 2 in the SBITS

2 Peter 2 in the SBITS2

2 Peter 2 in the SBITS3

2 Peter 2 in the SBITS4

2 Peter 2 in the SBIUS

2 Peter 2 in the SBIVS

2 Peter 2 in the SBT

2 Peter 2 in the SBT1E

2 Peter 2 in the SCHL

2 Peter 2 in the SNT

2 Peter 2 in the SUSU

2 Peter 2 in the SUSU2

2 Peter 2 in the SYNO

2 Peter 2 in the TBIAOTANT

2 Peter 2 in the TBT1E

2 Peter 2 in the TBT1E2

2 Peter 2 in the TFTIP

2 Peter 2 in the TFTU

2 Peter 2 in the TGNTATF3T

2 Peter 2 in the THAI

2 Peter 2 in the TNFD

2 Peter 2 in the TNT

2 Peter 2 in the TNTIK

2 Peter 2 in the TNTIL

2 Peter 2 in the TNTIN

2 Peter 2 in the TNTIP

2 Peter 2 in the TNTIZ

2 Peter 2 in the TOMA

2 Peter 2 in the TTENT

2 Peter 2 in the UBG

2 Peter 2 in the UGV

2 Peter 2 in the UGV2

2 Peter 2 in the UGV3

2 Peter 2 in the VBL

2 Peter 2 in the VDCC

2 Peter 2 in the YALU

2 Peter 2 in the YAPE

2 Peter 2 in the YBVTP

2 Peter 2 in the ZBP