2 Samuel 22 (BOGWICC)

1 Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. 2 Iye anati,“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga. 3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. 4 “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga. 5 “Mafunde a imfa anandizinga;mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri. 6 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;misampha ya imfa inalimbana nane. 7 “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;ndinapemphera kwa Mulungu wanga.Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake. 8 “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,maziko a miyamba anagwedezeka;ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya. 9 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake. 10 Iye anangʼamba thambo natsika pansi;pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda. 11 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;nawuluka ndi mphepo mwaliwiro. 12 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,mitambo yakuda ya mlengalenga. 13 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pakemunkachokera makala amoto alawilawi. 14 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse. 15 Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake,ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa. 16 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera,ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera,Yehova atabangula mwaukali,pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake. 17 “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;anandivuwula mʼmadzi ozama. 18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,adani anga amene anali amphamvu kuposa ine. 19 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,koma Yehova anali thandizo langa. 20 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane. 21 “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa. 22 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga. 23 Malamulo ake onse ali pamaso panga,sindinasiye malangizo ake. 24 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pakendipo ndakhala ndi kupewa tchimo. 25 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake. 26 “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu,kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino, 27 Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo. 28 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa. 29 Inu Yehova, ndinu nyale yanga;Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika. 30 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo,ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu. 31 “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;mawu a Yehova alibe cholakwika.Iye ndi chishangokwa onse amene amathawira kwa iye. 32 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu? 33 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvundi kulungamitsa njira yanga. 34 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri. 35 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo. 36 Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso;mumawerama kuti mundikweze. 37 Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino,kuti mapazi anga asaterereke. 38 “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha;sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa. 39 Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso;Iwo anagwera pansi pa mapazi anga. 40 Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo;munagwaditsa adani anga pa mapazi anga. 41 Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa;ndipo ndinawononga adani anga. 42 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe. 43 Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi;ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu. 44 “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu;Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga. 45 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;akangomva za ine, amandigonjera. 46 Iwo onse anataya mtima;anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera. 47 “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa.Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga! 48 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga, 49 amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga.Inu munandikuza kuposa adani anga;munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. 50 Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu. 51 “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake,amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake,kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”

In Other Versions

2 Samuel 22 in the ANGEFD

2 Samuel 22 in the ANTPNG2D

2 Samuel 22 in the AS21

2 Samuel 22 in the BAGH

2 Samuel 22 in the BBPNG

2 Samuel 22 in the BBT1E

2 Samuel 22 in the BDS

2 Samuel 22 in the BEV

2 Samuel 22 in the BHAD

2 Samuel 22 in the BIB

2 Samuel 22 in the BLPT

2 Samuel 22 in the BNT

2 Samuel 22 in the BNTABOOT

2 Samuel 22 in the BNTLV

2 Samuel 22 in the BOATCB

2 Samuel 22 in the BOATCB2

2 Samuel 22 in the BOBCV

2 Samuel 22 in the BOCNT

2 Samuel 22 in the BOECS

2 Samuel 22 in the BOHCB

2 Samuel 22 in the BOHCV

2 Samuel 22 in the BOHLNT

2 Samuel 22 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 22 in the BOICB

2 Samuel 22 in the BOILNTAP

2 Samuel 22 in the BOITCV

2 Samuel 22 in the BOKCV

2 Samuel 22 in the BOKCV2

2 Samuel 22 in the BOKHWOG

2 Samuel 22 in the BOKSSV

2 Samuel 22 in the BOLCB

2 Samuel 22 in the BOLCB2

2 Samuel 22 in the BOMCV

2 Samuel 22 in the BONAV

2 Samuel 22 in the BONCB

2 Samuel 22 in the BONLT

2 Samuel 22 in the BONUT2

2 Samuel 22 in the BOPLNT

2 Samuel 22 in the BOSCB

2 Samuel 22 in the BOSNC

2 Samuel 22 in the BOTLNT

2 Samuel 22 in the BOVCB

2 Samuel 22 in the BOYCB

2 Samuel 22 in the BPBB

2 Samuel 22 in the BPH

2 Samuel 22 in the BSB

2 Samuel 22 in the CCB

2 Samuel 22 in the CUV

2 Samuel 22 in the CUVS

2 Samuel 22 in the DBT

2 Samuel 22 in the DGDNT

2 Samuel 22 in the DHNT

2 Samuel 22 in the DNT

2 Samuel 22 in the ELBE

2 Samuel 22 in the EMTV

2 Samuel 22 in the ESV

2 Samuel 22 in the FBV

2 Samuel 22 in the FEB

2 Samuel 22 in the GGMNT

2 Samuel 22 in the GNT

2 Samuel 22 in the HARY

2 Samuel 22 in the HNT

2 Samuel 22 in the IRVA

2 Samuel 22 in the IRVB

2 Samuel 22 in the IRVG

2 Samuel 22 in the IRVH

2 Samuel 22 in the IRVK

2 Samuel 22 in the IRVM

2 Samuel 22 in the IRVM2

2 Samuel 22 in the IRVO

2 Samuel 22 in the IRVP

2 Samuel 22 in the IRVT

2 Samuel 22 in the IRVT2

2 Samuel 22 in the IRVU

2 Samuel 22 in the ISVN

2 Samuel 22 in the JSNT

2 Samuel 22 in the KAPI

2 Samuel 22 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 22 in the KBV

2 Samuel 22 in the KJV

2 Samuel 22 in the KNFD

2 Samuel 22 in the LBA

2 Samuel 22 in the LBLA

2 Samuel 22 in the LNT

2 Samuel 22 in the LSV

2 Samuel 22 in the MAAL

2 Samuel 22 in the MBV

2 Samuel 22 in the MBV2

2 Samuel 22 in the MHNT

2 Samuel 22 in the MKNFD

2 Samuel 22 in the MNG

2 Samuel 22 in the MNT

2 Samuel 22 in the MNT2

2 Samuel 22 in the MRS1T

2 Samuel 22 in the NAA

2 Samuel 22 in the NASB

2 Samuel 22 in the NBLA

2 Samuel 22 in the NBS

2 Samuel 22 in the NBVTP

2 Samuel 22 in the NET2

2 Samuel 22 in the NIV11

2 Samuel 22 in the NNT

2 Samuel 22 in the NNT2

2 Samuel 22 in the NNT3

2 Samuel 22 in the PDDPT

2 Samuel 22 in the PFNT

2 Samuel 22 in the RMNT

2 Samuel 22 in the SBIAS

2 Samuel 22 in the SBIBS

2 Samuel 22 in the SBIBS2

2 Samuel 22 in the SBICS

2 Samuel 22 in the SBIDS

2 Samuel 22 in the SBIGS

2 Samuel 22 in the SBIHS

2 Samuel 22 in the SBIIS

2 Samuel 22 in the SBIIS2

2 Samuel 22 in the SBIIS3

2 Samuel 22 in the SBIKS

2 Samuel 22 in the SBIKS2

2 Samuel 22 in the SBIMS

2 Samuel 22 in the SBIOS

2 Samuel 22 in the SBIPS

2 Samuel 22 in the SBISS

2 Samuel 22 in the SBITS

2 Samuel 22 in the SBITS2

2 Samuel 22 in the SBITS3

2 Samuel 22 in the SBITS4

2 Samuel 22 in the SBIUS

2 Samuel 22 in the SBIVS

2 Samuel 22 in the SBT

2 Samuel 22 in the SBT1E

2 Samuel 22 in the SCHL

2 Samuel 22 in the SNT

2 Samuel 22 in the SUSU

2 Samuel 22 in the SUSU2

2 Samuel 22 in the SYNO

2 Samuel 22 in the TBIAOTANT

2 Samuel 22 in the TBT1E

2 Samuel 22 in the TBT1E2

2 Samuel 22 in the TFTIP

2 Samuel 22 in the TFTU

2 Samuel 22 in the TGNTATF3T

2 Samuel 22 in the THAI

2 Samuel 22 in the TNFD

2 Samuel 22 in the TNT

2 Samuel 22 in the TNTIK

2 Samuel 22 in the TNTIL

2 Samuel 22 in the TNTIN

2 Samuel 22 in the TNTIP

2 Samuel 22 in the TNTIZ

2 Samuel 22 in the TOMA

2 Samuel 22 in the TTENT

2 Samuel 22 in the UBG

2 Samuel 22 in the UGV

2 Samuel 22 in the UGV2

2 Samuel 22 in the UGV3

2 Samuel 22 in the VBL

2 Samuel 22 in the VDCC

2 Samuel 22 in the YALU

2 Samuel 22 in the YAPE

2 Samuel 22 in the YBVTP

2 Samuel 22 in the ZBP