2 Samuel 6 (BOGWICC)
1 Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. 2 Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo. 3 Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, 4 imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake. 5 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga. 6 Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 7 Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo. 8 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza. 9 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” 10 Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 11 Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse. 12 Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. 13 Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa. 14 Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala, 15 pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga. 16 Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake. 17 Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. 18 Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse. 19 Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake. 20 Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.” 21 Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova. 22 Ineyo ndidzadzinyoza kuposa apa, ndipo ndidzakhala wonyozeka mʼmaso mwako. Koma pakati pa akapolo aakazi awa amene umanena za iwo, ndidzalemekezedwa.” 23 Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira.
In Other Versions
2 Samuel 6 in the ANGEFD
2 Samuel 6 in the ANTPNG2D
2 Samuel 6 in the AS21
2 Samuel 6 in the BAGH
2 Samuel 6 in the BBPNG
2 Samuel 6 in the BBT1E
2 Samuel 6 in the BDS
2 Samuel 6 in the BEV
2 Samuel 6 in the BHAD
2 Samuel 6 in the BIB
2 Samuel 6 in the BLPT
2 Samuel 6 in the BNT
2 Samuel 6 in the BNTABOOT
2 Samuel 6 in the BNTLV
2 Samuel 6 in the BOATCB
2 Samuel 6 in the BOATCB2
2 Samuel 6 in the BOBCV
2 Samuel 6 in the BOCNT
2 Samuel 6 in the BOECS
2 Samuel 6 in the BOHCB
2 Samuel 6 in the BOHCV
2 Samuel 6 in the BOHLNT
2 Samuel 6 in the BOHNTLTAL
2 Samuel 6 in the BOICB
2 Samuel 6 in the BOILNTAP
2 Samuel 6 in the BOITCV
2 Samuel 6 in the BOKCV
2 Samuel 6 in the BOKCV2
2 Samuel 6 in the BOKHWOG
2 Samuel 6 in the BOKSSV
2 Samuel 6 in the BOLCB
2 Samuel 6 in the BOLCB2
2 Samuel 6 in the BOMCV
2 Samuel 6 in the BONAV
2 Samuel 6 in the BONCB
2 Samuel 6 in the BONLT
2 Samuel 6 in the BONUT2
2 Samuel 6 in the BOPLNT
2 Samuel 6 in the BOSCB
2 Samuel 6 in the BOSNC
2 Samuel 6 in the BOTLNT
2 Samuel 6 in the BOVCB
2 Samuel 6 in the BOYCB
2 Samuel 6 in the BPBB
2 Samuel 6 in the BPH
2 Samuel 6 in the BSB
2 Samuel 6 in the CCB
2 Samuel 6 in the CUV
2 Samuel 6 in the CUVS
2 Samuel 6 in the DBT
2 Samuel 6 in the DGDNT
2 Samuel 6 in the DHNT
2 Samuel 6 in the DNT
2 Samuel 6 in the ELBE
2 Samuel 6 in the EMTV
2 Samuel 6 in the ESV
2 Samuel 6 in the FBV
2 Samuel 6 in the FEB
2 Samuel 6 in the GGMNT
2 Samuel 6 in the GNT
2 Samuel 6 in the HARY
2 Samuel 6 in the HNT
2 Samuel 6 in the IRVA
2 Samuel 6 in the IRVB
2 Samuel 6 in the IRVG
2 Samuel 6 in the IRVH
2 Samuel 6 in the IRVK
2 Samuel 6 in the IRVM
2 Samuel 6 in the IRVM2
2 Samuel 6 in the IRVO
2 Samuel 6 in the IRVP
2 Samuel 6 in the IRVT
2 Samuel 6 in the IRVT2
2 Samuel 6 in the IRVU
2 Samuel 6 in the ISVN
2 Samuel 6 in the JSNT
2 Samuel 6 in the KAPI
2 Samuel 6 in the KBT1ETNIK
2 Samuel 6 in the KBV
2 Samuel 6 in the KJV
2 Samuel 6 in the KNFD
2 Samuel 6 in the LBA
2 Samuel 6 in the LBLA
2 Samuel 6 in the LNT
2 Samuel 6 in the LSV
2 Samuel 6 in the MAAL
2 Samuel 6 in the MBV
2 Samuel 6 in the MBV2
2 Samuel 6 in the MHNT
2 Samuel 6 in the MKNFD
2 Samuel 6 in the MNG
2 Samuel 6 in the MNT
2 Samuel 6 in the MNT2
2 Samuel 6 in the MRS1T
2 Samuel 6 in the NAA
2 Samuel 6 in the NASB
2 Samuel 6 in the NBLA
2 Samuel 6 in the NBS
2 Samuel 6 in the NBVTP
2 Samuel 6 in the NET2
2 Samuel 6 in the NIV11
2 Samuel 6 in the NNT
2 Samuel 6 in the NNT2
2 Samuel 6 in the NNT3
2 Samuel 6 in the PDDPT
2 Samuel 6 in the PFNT
2 Samuel 6 in the RMNT
2 Samuel 6 in the SBIAS
2 Samuel 6 in the SBIBS
2 Samuel 6 in the SBIBS2
2 Samuel 6 in the SBICS
2 Samuel 6 in the SBIDS
2 Samuel 6 in the SBIGS
2 Samuel 6 in the SBIHS
2 Samuel 6 in the SBIIS
2 Samuel 6 in the SBIIS2
2 Samuel 6 in the SBIIS3
2 Samuel 6 in the SBIKS
2 Samuel 6 in the SBIKS2
2 Samuel 6 in the SBIMS
2 Samuel 6 in the SBIOS
2 Samuel 6 in the SBIPS
2 Samuel 6 in the SBISS
2 Samuel 6 in the SBITS
2 Samuel 6 in the SBITS2
2 Samuel 6 in the SBITS3
2 Samuel 6 in the SBITS4
2 Samuel 6 in the SBIUS
2 Samuel 6 in the SBIVS
2 Samuel 6 in the SBT
2 Samuel 6 in the SBT1E
2 Samuel 6 in the SCHL
2 Samuel 6 in the SNT
2 Samuel 6 in the SUSU
2 Samuel 6 in the SUSU2
2 Samuel 6 in the SYNO
2 Samuel 6 in the TBIAOTANT
2 Samuel 6 in the TBT1E
2 Samuel 6 in the TBT1E2
2 Samuel 6 in the TFTIP
2 Samuel 6 in the TFTU
2 Samuel 6 in the TGNTATF3T
2 Samuel 6 in the THAI
2 Samuel 6 in the TNFD
2 Samuel 6 in the TNT
2 Samuel 6 in the TNTIK
2 Samuel 6 in the TNTIL
2 Samuel 6 in the TNTIN
2 Samuel 6 in the TNTIP
2 Samuel 6 in the TNTIZ
2 Samuel 6 in the TOMA
2 Samuel 6 in the TTENT
2 Samuel 6 in the UBG
2 Samuel 6 in the UGV
2 Samuel 6 in the UGV2
2 Samuel 6 in the UGV3
2 Samuel 6 in the VBL
2 Samuel 6 in the VDCC
2 Samuel 6 in the YALU
2 Samuel 6 in the YAPE
2 Samuel 6 in the YBVTP
2 Samuel 6 in the ZBP