2 Samuel 7 (BOGWICC)

1 Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, 2 mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.” 3 Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.” 4 Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati, 5 “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? 6 Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti. 7 Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ” 8 “Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. 9 Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 10 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja, 11 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse.“ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako: 12 Masiku ako akadzatha ndipo ukadzakapuma ndi makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, imene idzachokera mʼthupi mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 13 Iye ndiye amene adzamangire nyumba Dzina langa, ndipo Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 14 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu. 15 Koma sindidzasiya kumukonda, monga ndinachitira ndi Sauli, amene ndinamuchotsa iwe usanakhale mfumu. 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ” 17 Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira. 18 Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati:“Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?” 19 Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse? 20 Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu? Pakuti Inu Ambuye Wamphamvuzonse mukumudziwa mtumiki wanu. 21 Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu. 22 Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu. 23 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 24 Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo. 25 “Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera, 26 kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. 27 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 28 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 29 Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”

In Other Versions

2 Samuel 7 in the ANGEFD

2 Samuel 7 in the ANTPNG2D

2 Samuel 7 in the AS21

2 Samuel 7 in the BAGH

2 Samuel 7 in the BBPNG

2 Samuel 7 in the BBT1E

2 Samuel 7 in the BDS

2 Samuel 7 in the BEV

2 Samuel 7 in the BHAD

2 Samuel 7 in the BIB

2 Samuel 7 in the BLPT

2 Samuel 7 in the BNT

2 Samuel 7 in the BNTABOOT

2 Samuel 7 in the BNTLV

2 Samuel 7 in the BOATCB

2 Samuel 7 in the BOATCB2

2 Samuel 7 in the BOBCV

2 Samuel 7 in the BOCNT

2 Samuel 7 in the BOECS

2 Samuel 7 in the BOHCB

2 Samuel 7 in the BOHCV

2 Samuel 7 in the BOHLNT

2 Samuel 7 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 7 in the BOICB

2 Samuel 7 in the BOILNTAP

2 Samuel 7 in the BOITCV

2 Samuel 7 in the BOKCV

2 Samuel 7 in the BOKCV2

2 Samuel 7 in the BOKHWOG

2 Samuel 7 in the BOKSSV

2 Samuel 7 in the BOLCB

2 Samuel 7 in the BOLCB2

2 Samuel 7 in the BOMCV

2 Samuel 7 in the BONAV

2 Samuel 7 in the BONCB

2 Samuel 7 in the BONLT

2 Samuel 7 in the BONUT2

2 Samuel 7 in the BOPLNT

2 Samuel 7 in the BOSCB

2 Samuel 7 in the BOSNC

2 Samuel 7 in the BOTLNT

2 Samuel 7 in the BOVCB

2 Samuel 7 in the BOYCB

2 Samuel 7 in the BPBB

2 Samuel 7 in the BPH

2 Samuel 7 in the BSB

2 Samuel 7 in the CCB

2 Samuel 7 in the CUV

2 Samuel 7 in the CUVS

2 Samuel 7 in the DBT

2 Samuel 7 in the DGDNT

2 Samuel 7 in the DHNT

2 Samuel 7 in the DNT

2 Samuel 7 in the ELBE

2 Samuel 7 in the EMTV

2 Samuel 7 in the ESV

2 Samuel 7 in the FBV

2 Samuel 7 in the FEB

2 Samuel 7 in the GGMNT

2 Samuel 7 in the GNT

2 Samuel 7 in the HARY

2 Samuel 7 in the HNT

2 Samuel 7 in the IRVA

2 Samuel 7 in the IRVB

2 Samuel 7 in the IRVG

2 Samuel 7 in the IRVH

2 Samuel 7 in the IRVK

2 Samuel 7 in the IRVM

2 Samuel 7 in the IRVM2

2 Samuel 7 in the IRVO

2 Samuel 7 in the IRVP

2 Samuel 7 in the IRVT

2 Samuel 7 in the IRVT2

2 Samuel 7 in the IRVU

2 Samuel 7 in the ISVN

2 Samuel 7 in the JSNT

2 Samuel 7 in the KAPI

2 Samuel 7 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 7 in the KBV

2 Samuel 7 in the KJV

2 Samuel 7 in the KNFD

2 Samuel 7 in the LBA

2 Samuel 7 in the LBLA

2 Samuel 7 in the LNT

2 Samuel 7 in the LSV

2 Samuel 7 in the MAAL

2 Samuel 7 in the MBV

2 Samuel 7 in the MBV2

2 Samuel 7 in the MHNT

2 Samuel 7 in the MKNFD

2 Samuel 7 in the MNG

2 Samuel 7 in the MNT

2 Samuel 7 in the MNT2

2 Samuel 7 in the MRS1T

2 Samuel 7 in the NAA

2 Samuel 7 in the NASB

2 Samuel 7 in the NBLA

2 Samuel 7 in the NBS

2 Samuel 7 in the NBVTP

2 Samuel 7 in the NET2

2 Samuel 7 in the NIV11

2 Samuel 7 in the NNT

2 Samuel 7 in the NNT2

2 Samuel 7 in the NNT3

2 Samuel 7 in the PDDPT

2 Samuel 7 in the PFNT

2 Samuel 7 in the RMNT

2 Samuel 7 in the SBIAS

2 Samuel 7 in the SBIBS

2 Samuel 7 in the SBIBS2

2 Samuel 7 in the SBICS

2 Samuel 7 in the SBIDS

2 Samuel 7 in the SBIGS

2 Samuel 7 in the SBIHS

2 Samuel 7 in the SBIIS

2 Samuel 7 in the SBIIS2

2 Samuel 7 in the SBIIS3

2 Samuel 7 in the SBIKS

2 Samuel 7 in the SBIKS2

2 Samuel 7 in the SBIMS

2 Samuel 7 in the SBIOS

2 Samuel 7 in the SBIPS

2 Samuel 7 in the SBISS

2 Samuel 7 in the SBITS

2 Samuel 7 in the SBITS2

2 Samuel 7 in the SBITS3

2 Samuel 7 in the SBITS4

2 Samuel 7 in the SBIUS

2 Samuel 7 in the SBIVS

2 Samuel 7 in the SBT

2 Samuel 7 in the SBT1E

2 Samuel 7 in the SCHL

2 Samuel 7 in the SNT

2 Samuel 7 in the SUSU

2 Samuel 7 in the SUSU2

2 Samuel 7 in the SYNO

2 Samuel 7 in the TBIAOTANT

2 Samuel 7 in the TBT1E

2 Samuel 7 in the TBT1E2

2 Samuel 7 in the TFTIP

2 Samuel 7 in the TFTU

2 Samuel 7 in the TGNTATF3T

2 Samuel 7 in the THAI

2 Samuel 7 in the TNFD

2 Samuel 7 in the TNT

2 Samuel 7 in the TNTIK

2 Samuel 7 in the TNTIL

2 Samuel 7 in the TNTIN

2 Samuel 7 in the TNTIP

2 Samuel 7 in the TNTIZ

2 Samuel 7 in the TOMA

2 Samuel 7 in the TTENT

2 Samuel 7 in the UBG

2 Samuel 7 in the UGV

2 Samuel 7 in the UGV2

2 Samuel 7 in the UGV3

2 Samuel 7 in the VBL

2 Samuel 7 in the VDCC

2 Samuel 7 in the YALU

2 Samuel 7 in the YAPE

2 Samuel 7 in the YBVTP

2 Samuel 7 in the ZBP