Daniel 9 (BOGWICC)

1 Mʼchaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero (wochokera kwa Amedi), amene anakhala mfumu ya ku Babuloni, 2 ine Danieli ndinazindikira powerenga mawu a Yehova opatsidwa kwa mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja kwa zaka 70. 3 Choncho ndinatembenukira kwa Ambuye Mulungu ndipo ndinamudandaulira ndi kupempha posala kudya, ndi kuvala chiguduli ndi kudzola phulusa. 4 Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa:Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu, 5 tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu. 6 Sitinamvere aneneri atumiki anu, amene anayankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, makolo athu, ndi kwa anthu onse a mʼdziko. 7 “Ambuye ndinu olungama, koma lero tili ndi manyazi, ife anthu a ku Yuda, a ku Yerusalemu ndi Israeli yense, apafupi ndi akutali omwe, ku mayiko onse kumene munatipirikitsira chifukwa cha kusakhulupirika kwathu. 8 Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani. 9 Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira: 10 Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake. 11 Aisraeli onse anachimwira lamulo lanu motero anapatuka, nakana kukumverani.“Choncho matemberero ndi olumbira amene alembedwa mʼmalamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera chifukwa takuchimwirani. 12 Inu mwakwaniritsa mawu amene munayankhula otitsutsa ife ndi otsutsa otilamulira potibweretsera tsoka lalikulu. Pa dziko lapansi sipanachitikenso zinthu ngati zimene zaonekera Yerusalemu. 13 Monga kunalembedwa mʼMalamulo a Mose, tsoka lililonse latifikira chikhalirecho sitinapemphe Yehova Mulungu wathu kuti atikomere mtima. Sitinasiye machimo athu, ndipo sitinasamale choonadi chanu. 14 Choncho Yehova anakonza kuti atigwetsere tsoka limeneli, ndipo wachitadi popeza Yehova Mulungu wathu ndi wolungama mu chilichonse amachita; chikhalirecho ife sitinamumvere. 15 “Inu Ambuye Mulungu wathu, munatulutsa anthu anu ku Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo dzina lanu ndi lotchuka mpaka lero. Ife tachimwa, tachita zolakwa. 16 Inu Ambuye, molingana ndi zochita zanu zolungama, tikukupemphani kuti muchotse mkwiyo ndi ukali wanu pa Yerusalemu mzinda wanu, phiri lanu loyera. Machimo athu ndi mphulupulu za makolo athu zachititsa kuti onse otizungulira atonze Yerusalemu ndi anthu anu. 17 “Tsopano Mulungu wathu, imvani mapemphero ndi zopempha za mtumiki wanu. Kuti anthu onse akudziweni kuti ndinu Ambuye, komerani mtima malo anu opatulika amene asanduka bwinja. 18 Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu. 19 Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.” 20 Ndikuyankhula ndi kupemphera, kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraeli ndi kupempherera phiri lake loyera kwa Yehova Mulungu wanga, 21 Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo. 22 Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu. 23 Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya. 24 “Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa. 25 “Tsono udziwe ndipo uzindikire izi kuti kuyambira pamene lamulo linaperekedwa kuti Yerusalemu akonzedwenso mpaka pamene mfumu Yodzozedwa idzafike padzapita zaka 49. Pa zaka 434 mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso, ndipo mabwalo ndi ngalande zake zidzatetezedwa. Koma nthawiyi idzakhala ya masautso. 26 Patatha zaka 434, Wodzozedwayo adzaphedwa ndipo sadzakhala ndi aliyense. Anthu a wolamulira amene adzabwere adzawononga mzinda ndi Nyumba ya Mulungu. Kutha kwake kudzafika ngati chigumula. Komabe nkhondo idzapitirira mpaka chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu chitachitika. 27 Adzachita pangano lolimba ndi anthu ambiri kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Koma pakatinʼpakati pa sabata limodzilo iye adzaletsa kupereka nsembe ndi chopereka. Chonyansa chosakaza chija adzachiyika mʼNyumba ya Mulungu, ndipo chidzakhalapobe mpaka wochita zimenezi atalangidwa ndi chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu.”

In Other Versions

Daniel 9 in the ANGEFD

Daniel 9 in the ANTPNG2D

Daniel 9 in the AS21

Daniel 9 in the BAGH

Daniel 9 in the BBPNG

Daniel 9 in the BBT1E

Daniel 9 in the BDS

Daniel 9 in the BEV

Daniel 9 in the BHAD

Daniel 9 in the BIB

Daniel 9 in the BLPT

Daniel 9 in the BNT

Daniel 9 in the BNTABOOT

Daniel 9 in the BNTLV

Daniel 9 in the BOATCB

Daniel 9 in the BOATCB2

Daniel 9 in the BOBCV

Daniel 9 in the BOCNT

Daniel 9 in the BOECS

Daniel 9 in the BOHCB

Daniel 9 in the BOHCV

Daniel 9 in the BOHLNT

Daniel 9 in the BOHNTLTAL

Daniel 9 in the BOICB

Daniel 9 in the BOILNTAP

Daniel 9 in the BOITCV

Daniel 9 in the BOKCV

Daniel 9 in the BOKCV2

Daniel 9 in the BOKHWOG

Daniel 9 in the BOKSSV

Daniel 9 in the BOLCB

Daniel 9 in the BOLCB2

Daniel 9 in the BOMCV

Daniel 9 in the BONAV

Daniel 9 in the BONCB

Daniel 9 in the BONLT

Daniel 9 in the BONUT2

Daniel 9 in the BOPLNT

Daniel 9 in the BOSCB

Daniel 9 in the BOSNC

Daniel 9 in the BOTLNT

Daniel 9 in the BOVCB

Daniel 9 in the BOYCB

Daniel 9 in the BPBB

Daniel 9 in the BPH

Daniel 9 in the BSB

Daniel 9 in the CCB

Daniel 9 in the CUV

Daniel 9 in the CUVS

Daniel 9 in the DBT

Daniel 9 in the DGDNT

Daniel 9 in the DHNT

Daniel 9 in the DNT

Daniel 9 in the ELBE

Daniel 9 in the EMTV

Daniel 9 in the ESV

Daniel 9 in the FBV

Daniel 9 in the FEB

Daniel 9 in the GGMNT

Daniel 9 in the GNT

Daniel 9 in the HARY

Daniel 9 in the HNT

Daniel 9 in the IRVA

Daniel 9 in the IRVB

Daniel 9 in the IRVG

Daniel 9 in the IRVH

Daniel 9 in the IRVK

Daniel 9 in the IRVM

Daniel 9 in the IRVM2

Daniel 9 in the IRVO

Daniel 9 in the IRVP

Daniel 9 in the IRVT

Daniel 9 in the IRVT2

Daniel 9 in the IRVU

Daniel 9 in the ISVN

Daniel 9 in the JSNT

Daniel 9 in the KAPI

Daniel 9 in the KBT1ETNIK

Daniel 9 in the KBV

Daniel 9 in the KJV

Daniel 9 in the KNFD

Daniel 9 in the LBA

Daniel 9 in the LBLA

Daniel 9 in the LNT

Daniel 9 in the LSV

Daniel 9 in the MAAL

Daniel 9 in the MBV

Daniel 9 in the MBV2

Daniel 9 in the MHNT

Daniel 9 in the MKNFD

Daniel 9 in the MNG

Daniel 9 in the MNT

Daniel 9 in the MNT2

Daniel 9 in the MRS1T

Daniel 9 in the NAA

Daniel 9 in the NASB

Daniel 9 in the NBLA

Daniel 9 in the NBS

Daniel 9 in the NBVTP

Daniel 9 in the NET2

Daniel 9 in the NIV11

Daniel 9 in the NNT

Daniel 9 in the NNT2

Daniel 9 in the NNT3

Daniel 9 in the PDDPT

Daniel 9 in the PFNT

Daniel 9 in the RMNT

Daniel 9 in the SBIAS

Daniel 9 in the SBIBS

Daniel 9 in the SBIBS2

Daniel 9 in the SBICS

Daniel 9 in the SBIDS

Daniel 9 in the SBIGS

Daniel 9 in the SBIHS

Daniel 9 in the SBIIS

Daniel 9 in the SBIIS2

Daniel 9 in the SBIIS3

Daniel 9 in the SBIKS

Daniel 9 in the SBIKS2

Daniel 9 in the SBIMS

Daniel 9 in the SBIOS

Daniel 9 in the SBIPS

Daniel 9 in the SBISS

Daniel 9 in the SBITS

Daniel 9 in the SBITS2

Daniel 9 in the SBITS3

Daniel 9 in the SBITS4

Daniel 9 in the SBIUS

Daniel 9 in the SBIVS

Daniel 9 in the SBT

Daniel 9 in the SBT1E

Daniel 9 in the SCHL

Daniel 9 in the SNT

Daniel 9 in the SUSU

Daniel 9 in the SUSU2

Daniel 9 in the SYNO

Daniel 9 in the TBIAOTANT

Daniel 9 in the TBT1E

Daniel 9 in the TBT1E2

Daniel 9 in the TFTIP

Daniel 9 in the TFTU

Daniel 9 in the TGNTATF3T

Daniel 9 in the THAI

Daniel 9 in the TNFD

Daniel 9 in the TNT

Daniel 9 in the TNTIK

Daniel 9 in the TNTIL

Daniel 9 in the TNTIN

Daniel 9 in the TNTIP

Daniel 9 in the TNTIZ

Daniel 9 in the TOMA

Daniel 9 in the TTENT

Daniel 9 in the UBG

Daniel 9 in the UGV

Daniel 9 in the UGV2

Daniel 9 in the UGV3

Daniel 9 in the VBL

Daniel 9 in the VDCC

Daniel 9 in the YALU

Daniel 9 in the YAPE

Daniel 9 in the YBVTP

Daniel 9 in the ZBP