Deuteronomy 10 (BOGWICC)
1 Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa. 2 Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.” 3 Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga. 4 Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine. 5 Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo. 6 Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake. 7 Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi. 8 Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero. 9 Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira. 10 Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni. 11 Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.” 12 Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, 13 ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino. 14 Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 15 Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero. 16 Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza. 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. 18 Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. 19 Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto. 20 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake. 21 Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija. 22 Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.
In Other Versions
Deuteronomy 10 in the ANGEFD
Deuteronomy 10 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 10 in the AS21
Deuteronomy 10 in the BAGH
Deuteronomy 10 in the BBPNG
Deuteronomy 10 in the BBT1E
Deuteronomy 10 in the BDS
Deuteronomy 10 in the BEV
Deuteronomy 10 in the BHAD
Deuteronomy 10 in the BIB
Deuteronomy 10 in the BLPT
Deuteronomy 10 in the BNT
Deuteronomy 10 in the BNTABOOT
Deuteronomy 10 in the BNTLV
Deuteronomy 10 in the BOATCB
Deuteronomy 10 in the BOATCB2
Deuteronomy 10 in the BOBCV
Deuteronomy 10 in the BOCNT
Deuteronomy 10 in the BOECS
Deuteronomy 10 in the BOHCB
Deuteronomy 10 in the BOHCV
Deuteronomy 10 in the BOHLNT
Deuteronomy 10 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 10 in the BOICB
Deuteronomy 10 in the BOILNTAP
Deuteronomy 10 in the BOITCV
Deuteronomy 10 in the BOKCV
Deuteronomy 10 in the BOKCV2
Deuteronomy 10 in the BOKHWOG
Deuteronomy 10 in the BOKSSV
Deuteronomy 10 in the BOLCB
Deuteronomy 10 in the BOLCB2
Deuteronomy 10 in the BOMCV
Deuteronomy 10 in the BONAV
Deuteronomy 10 in the BONCB
Deuteronomy 10 in the BONLT
Deuteronomy 10 in the BONUT2
Deuteronomy 10 in the BOPLNT
Deuteronomy 10 in the BOSCB
Deuteronomy 10 in the BOSNC
Deuteronomy 10 in the BOTLNT
Deuteronomy 10 in the BOVCB
Deuteronomy 10 in the BOYCB
Deuteronomy 10 in the BPBB
Deuteronomy 10 in the BPH
Deuteronomy 10 in the BSB
Deuteronomy 10 in the CCB
Deuteronomy 10 in the CUV
Deuteronomy 10 in the CUVS
Deuteronomy 10 in the DBT
Deuteronomy 10 in the DGDNT
Deuteronomy 10 in the DHNT
Deuteronomy 10 in the DNT
Deuteronomy 10 in the ELBE
Deuteronomy 10 in the EMTV
Deuteronomy 10 in the ESV
Deuteronomy 10 in the FBV
Deuteronomy 10 in the FEB
Deuteronomy 10 in the GGMNT
Deuteronomy 10 in the GNT
Deuteronomy 10 in the HARY
Deuteronomy 10 in the HNT
Deuteronomy 10 in the IRVA
Deuteronomy 10 in the IRVB
Deuteronomy 10 in the IRVG
Deuteronomy 10 in the IRVH
Deuteronomy 10 in the IRVK
Deuteronomy 10 in the IRVM
Deuteronomy 10 in the IRVM2
Deuteronomy 10 in the IRVO
Deuteronomy 10 in the IRVP
Deuteronomy 10 in the IRVT
Deuteronomy 10 in the IRVT2
Deuteronomy 10 in the IRVU
Deuteronomy 10 in the ISVN
Deuteronomy 10 in the JSNT
Deuteronomy 10 in the KAPI
Deuteronomy 10 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 10 in the KBV
Deuteronomy 10 in the KJV
Deuteronomy 10 in the KNFD
Deuteronomy 10 in the LBA
Deuteronomy 10 in the LBLA
Deuteronomy 10 in the LNT
Deuteronomy 10 in the LSV
Deuteronomy 10 in the MAAL
Deuteronomy 10 in the MBV
Deuteronomy 10 in the MBV2
Deuteronomy 10 in the MHNT
Deuteronomy 10 in the MKNFD
Deuteronomy 10 in the MNG
Deuteronomy 10 in the MNT
Deuteronomy 10 in the MNT2
Deuteronomy 10 in the MRS1T
Deuteronomy 10 in the NAA
Deuteronomy 10 in the NASB
Deuteronomy 10 in the NBLA
Deuteronomy 10 in the NBS
Deuteronomy 10 in the NBVTP
Deuteronomy 10 in the NET2
Deuteronomy 10 in the NIV11
Deuteronomy 10 in the NNT
Deuteronomy 10 in the NNT2
Deuteronomy 10 in the NNT3
Deuteronomy 10 in the PDDPT
Deuteronomy 10 in the PFNT
Deuteronomy 10 in the RMNT
Deuteronomy 10 in the SBIAS
Deuteronomy 10 in the SBIBS
Deuteronomy 10 in the SBIBS2
Deuteronomy 10 in the SBICS
Deuteronomy 10 in the SBIDS
Deuteronomy 10 in the SBIGS
Deuteronomy 10 in the SBIHS
Deuteronomy 10 in the SBIIS
Deuteronomy 10 in the SBIIS2
Deuteronomy 10 in the SBIIS3
Deuteronomy 10 in the SBIKS
Deuteronomy 10 in the SBIKS2
Deuteronomy 10 in the SBIMS
Deuteronomy 10 in the SBIOS
Deuteronomy 10 in the SBIPS
Deuteronomy 10 in the SBISS
Deuteronomy 10 in the SBITS
Deuteronomy 10 in the SBITS2
Deuteronomy 10 in the SBITS3
Deuteronomy 10 in the SBITS4
Deuteronomy 10 in the SBIUS
Deuteronomy 10 in the SBIVS
Deuteronomy 10 in the SBT
Deuteronomy 10 in the SBT1E
Deuteronomy 10 in the SCHL
Deuteronomy 10 in the SNT
Deuteronomy 10 in the SUSU
Deuteronomy 10 in the SUSU2
Deuteronomy 10 in the SYNO
Deuteronomy 10 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 10 in the TBT1E
Deuteronomy 10 in the TBT1E2
Deuteronomy 10 in the TFTIP
Deuteronomy 10 in the TFTU
Deuteronomy 10 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 10 in the THAI
Deuteronomy 10 in the TNFD
Deuteronomy 10 in the TNT
Deuteronomy 10 in the TNTIK
Deuteronomy 10 in the TNTIL
Deuteronomy 10 in the TNTIN
Deuteronomy 10 in the TNTIP
Deuteronomy 10 in the TNTIZ
Deuteronomy 10 in the TOMA
Deuteronomy 10 in the TTENT
Deuteronomy 10 in the UBG
Deuteronomy 10 in the UGV
Deuteronomy 10 in the UGV2
Deuteronomy 10 in the UGV3
Deuteronomy 10 in the VBL
Deuteronomy 10 in the VDCC
Deuteronomy 10 in the YALU
Deuteronomy 10 in the YAPE
Deuteronomy 10 in the YBVTP
Deuteronomy 10 in the ZBP