Deuteronomy 13 (BOGWICC)

1 Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, 2 chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), 3 musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 4 Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo. 5 Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu. 6 Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe, 7 milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi), 8 musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza. 9 Mumuphe ndithu. Dzanja lanu likhale loyambirira kumupha, kenaka manja a anthu ena onse. 10 Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo. 11 Tsono Aisraeli onse adzamva nachita mantha, ndipo palibe mmodzi pakati panu amene adzachitenso choyipa chotere. 12 Ngati mumvetsedwa kuti ku umodzi mwa mizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mukhalemo, 13 kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe), 14 mukuyenera kufunsa, kulondola ndi kufufuza bwino nkhaniyo. Ndipo ngati zitatsimikizikadi kuti ndi zoona kuti chinthu chonyansa chotere chachitikadi pakati panu, 15 muyenera kuwapha onse okhala mu mzinda umenewo. Muwonongeretu kwathunthu mzindawo, anthu ake ndi ziweto zake zomwe. 16 Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso. 17 Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu, 18 chifukwa mumamvera Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino ndi kuchita zoyenera pamaso pake.

In Other Versions

Deuteronomy 13 in the ANGEFD

Deuteronomy 13 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 13 in the AS21

Deuteronomy 13 in the BAGH

Deuteronomy 13 in the BBPNG

Deuteronomy 13 in the BBT1E

Deuteronomy 13 in the BDS

Deuteronomy 13 in the BEV

Deuteronomy 13 in the BHAD

Deuteronomy 13 in the BIB

Deuteronomy 13 in the BLPT

Deuteronomy 13 in the BNT

Deuteronomy 13 in the BNTABOOT

Deuteronomy 13 in the BNTLV

Deuteronomy 13 in the BOATCB

Deuteronomy 13 in the BOATCB2

Deuteronomy 13 in the BOBCV

Deuteronomy 13 in the BOCNT

Deuteronomy 13 in the BOECS

Deuteronomy 13 in the BOHCB

Deuteronomy 13 in the BOHCV

Deuteronomy 13 in the BOHLNT

Deuteronomy 13 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 13 in the BOICB

Deuteronomy 13 in the BOILNTAP

Deuteronomy 13 in the BOITCV

Deuteronomy 13 in the BOKCV

Deuteronomy 13 in the BOKCV2

Deuteronomy 13 in the BOKHWOG

Deuteronomy 13 in the BOKSSV

Deuteronomy 13 in the BOLCB

Deuteronomy 13 in the BOLCB2

Deuteronomy 13 in the BOMCV

Deuteronomy 13 in the BONAV

Deuteronomy 13 in the BONCB

Deuteronomy 13 in the BONLT

Deuteronomy 13 in the BONUT2

Deuteronomy 13 in the BOPLNT

Deuteronomy 13 in the BOSCB

Deuteronomy 13 in the BOSNC

Deuteronomy 13 in the BOTLNT

Deuteronomy 13 in the BOVCB

Deuteronomy 13 in the BOYCB

Deuteronomy 13 in the BPBB

Deuteronomy 13 in the BPH

Deuteronomy 13 in the BSB

Deuteronomy 13 in the CCB

Deuteronomy 13 in the CUV

Deuteronomy 13 in the CUVS

Deuteronomy 13 in the DBT

Deuteronomy 13 in the DGDNT

Deuteronomy 13 in the DHNT

Deuteronomy 13 in the DNT

Deuteronomy 13 in the ELBE

Deuteronomy 13 in the EMTV

Deuteronomy 13 in the ESV

Deuteronomy 13 in the FBV

Deuteronomy 13 in the FEB

Deuteronomy 13 in the GGMNT

Deuteronomy 13 in the GNT

Deuteronomy 13 in the HARY

Deuteronomy 13 in the HNT

Deuteronomy 13 in the IRVA

Deuteronomy 13 in the IRVB

Deuteronomy 13 in the IRVG

Deuteronomy 13 in the IRVH

Deuteronomy 13 in the IRVK

Deuteronomy 13 in the IRVM

Deuteronomy 13 in the IRVM2

Deuteronomy 13 in the IRVO

Deuteronomy 13 in the IRVP

Deuteronomy 13 in the IRVT

Deuteronomy 13 in the IRVT2

Deuteronomy 13 in the IRVU

Deuteronomy 13 in the ISVN

Deuteronomy 13 in the JSNT

Deuteronomy 13 in the KAPI

Deuteronomy 13 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 13 in the KBV

Deuteronomy 13 in the KJV

Deuteronomy 13 in the KNFD

Deuteronomy 13 in the LBA

Deuteronomy 13 in the LBLA

Deuteronomy 13 in the LNT

Deuteronomy 13 in the LSV

Deuteronomy 13 in the MAAL

Deuteronomy 13 in the MBV

Deuteronomy 13 in the MBV2

Deuteronomy 13 in the MHNT

Deuteronomy 13 in the MKNFD

Deuteronomy 13 in the MNG

Deuteronomy 13 in the MNT

Deuteronomy 13 in the MNT2

Deuteronomy 13 in the MRS1T

Deuteronomy 13 in the NAA

Deuteronomy 13 in the NASB

Deuteronomy 13 in the NBLA

Deuteronomy 13 in the NBS

Deuteronomy 13 in the NBVTP

Deuteronomy 13 in the NET2

Deuteronomy 13 in the NIV11

Deuteronomy 13 in the NNT

Deuteronomy 13 in the NNT2

Deuteronomy 13 in the NNT3

Deuteronomy 13 in the PDDPT

Deuteronomy 13 in the PFNT

Deuteronomy 13 in the RMNT

Deuteronomy 13 in the SBIAS

Deuteronomy 13 in the SBIBS

Deuteronomy 13 in the SBIBS2

Deuteronomy 13 in the SBICS

Deuteronomy 13 in the SBIDS

Deuteronomy 13 in the SBIGS

Deuteronomy 13 in the SBIHS

Deuteronomy 13 in the SBIIS

Deuteronomy 13 in the SBIIS2

Deuteronomy 13 in the SBIIS3

Deuteronomy 13 in the SBIKS

Deuteronomy 13 in the SBIKS2

Deuteronomy 13 in the SBIMS

Deuteronomy 13 in the SBIOS

Deuteronomy 13 in the SBIPS

Deuteronomy 13 in the SBISS

Deuteronomy 13 in the SBITS

Deuteronomy 13 in the SBITS2

Deuteronomy 13 in the SBITS3

Deuteronomy 13 in the SBITS4

Deuteronomy 13 in the SBIUS

Deuteronomy 13 in the SBIVS

Deuteronomy 13 in the SBT

Deuteronomy 13 in the SBT1E

Deuteronomy 13 in the SCHL

Deuteronomy 13 in the SNT

Deuteronomy 13 in the SUSU

Deuteronomy 13 in the SUSU2

Deuteronomy 13 in the SYNO

Deuteronomy 13 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 13 in the TBT1E

Deuteronomy 13 in the TBT1E2

Deuteronomy 13 in the TFTIP

Deuteronomy 13 in the TFTU

Deuteronomy 13 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 13 in the THAI

Deuteronomy 13 in the TNFD

Deuteronomy 13 in the TNT

Deuteronomy 13 in the TNTIK

Deuteronomy 13 in the TNTIL

Deuteronomy 13 in the TNTIN

Deuteronomy 13 in the TNTIP

Deuteronomy 13 in the TNTIZ

Deuteronomy 13 in the TOMA

Deuteronomy 13 in the TTENT

Deuteronomy 13 in the UBG

Deuteronomy 13 in the UGV

Deuteronomy 13 in the UGV2

Deuteronomy 13 in the UGV3

Deuteronomy 13 in the VBL

Deuteronomy 13 in the VDCC

Deuteronomy 13 in the YALU

Deuteronomy 13 in the YAPE

Deuteronomy 13 in the YBVTP

Deuteronomy 13 in the ZBP