Deuteronomy 19 (BOGWICC)
1 Yehova Mulungu wanu akadzawononga anthu amene dziko lawo akukupatsani, ndipo inu mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼmizinda ndi mʼnyumba zawo, 2 mukapatule mizinda itatu imene ili pakati pa dziko lomwe Yehova Mulungu akukupatsani kukhala lanu. 3 Mudzakonze misewu ndi kuligawa patatu dzikolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, kuti aliyense wopha munthu akhoza kuthawirako. 4 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa. 5 Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake. 6 Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala. 7 Ichi ndi chifukwa chake ndikukulamulani kuti mudzipatulire nokha mizinda itatu. 8 Ngati Yehova Mulungu wanu akulitsa malire anu monga analonjezera pa malumbiro ndi makolo anu, nakupatsani dziko lonse monga analonjezera, 9 chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera. 10 Muchite zimenezi kuti musakhetse magazi wosalakwa mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa, ndipo kuti musapezeke ndi mlandu wokhetsa magazi. 11 Koma ngati munthu adana ndi mnzake namubisalira panjira nʼkumuvulaza mpaka kumupha, nathawira ku umodzi mwa mizindayi, 12 akuluakulu a mu mzinda wake akamugwire ndi kumubwezera ku mzinda wake namupereka kwa wolipsira kuti aphedwe. 13 Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino. 14 Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 15 Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu. 16 Ngati mboni yonama ifuna kunamizira munthu mlandu, 17 anthu awiri okhudzidwa ndi mlanduwo ayenera kuyima pamaso pa Yehova pali ansembe ndi oweruza amene ali pa ntchito pa nthawiyo. 18 Oweruza afufuze bwinobwino, ndipo ngati zatsimikizika kuti mboniyo ndi yabodza, yopereka umboni wonama pa mʼbale wake, 19 ndiye kuti amuchitire iyeyo zimene anafuna kuchitira mʼbale wakezo. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 20 Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu. 21 Osachita chisoni, moyo uzilipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja ndi phazi kulipira phazi.
In Other Versions
Deuteronomy 19 in the ANGEFD
Deuteronomy 19 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 19 in the AS21
Deuteronomy 19 in the BAGH
Deuteronomy 19 in the BBPNG
Deuteronomy 19 in the BBT1E
Deuteronomy 19 in the BDS
Deuteronomy 19 in the BEV
Deuteronomy 19 in the BHAD
Deuteronomy 19 in the BIB
Deuteronomy 19 in the BLPT
Deuteronomy 19 in the BNT
Deuteronomy 19 in the BNTABOOT
Deuteronomy 19 in the BNTLV
Deuteronomy 19 in the BOATCB
Deuteronomy 19 in the BOATCB2
Deuteronomy 19 in the BOBCV
Deuteronomy 19 in the BOCNT
Deuteronomy 19 in the BOECS
Deuteronomy 19 in the BOHCB
Deuteronomy 19 in the BOHCV
Deuteronomy 19 in the BOHLNT
Deuteronomy 19 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 19 in the BOICB
Deuteronomy 19 in the BOILNTAP
Deuteronomy 19 in the BOITCV
Deuteronomy 19 in the BOKCV
Deuteronomy 19 in the BOKCV2
Deuteronomy 19 in the BOKHWOG
Deuteronomy 19 in the BOKSSV
Deuteronomy 19 in the BOLCB
Deuteronomy 19 in the BOLCB2
Deuteronomy 19 in the BOMCV
Deuteronomy 19 in the BONAV
Deuteronomy 19 in the BONCB
Deuteronomy 19 in the BONLT
Deuteronomy 19 in the BONUT2
Deuteronomy 19 in the BOPLNT
Deuteronomy 19 in the BOSCB
Deuteronomy 19 in the BOSNC
Deuteronomy 19 in the BOTLNT
Deuteronomy 19 in the BOVCB
Deuteronomy 19 in the BOYCB
Deuteronomy 19 in the BPBB
Deuteronomy 19 in the BPH
Deuteronomy 19 in the BSB
Deuteronomy 19 in the CCB
Deuteronomy 19 in the CUV
Deuteronomy 19 in the CUVS
Deuteronomy 19 in the DBT
Deuteronomy 19 in the DGDNT
Deuteronomy 19 in the DHNT
Deuteronomy 19 in the DNT
Deuteronomy 19 in the ELBE
Deuteronomy 19 in the EMTV
Deuteronomy 19 in the ESV
Deuteronomy 19 in the FBV
Deuteronomy 19 in the FEB
Deuteronomy 19 in the GGMNT
Deuteronomy 19 in the GNT
Deuteronomy 19 in the HARY
Deuteronomy 19 in the HNT
Deuteronomy 19 in the IRVA
Deuteronomy 19 in the IRVB
Deuteronomy 19 in the IRVG
Deuteronomy 19 in the IRVH
Deuteronomy 19 in the IRVK
Deuteronomy 19 in the IRVM
Deuteronomy 19 in the IRVM2
Deuteronomy 19 in the IRVO
Deuteronomy 19 in the IRVP
Deuteronomy 19 in the IRVT
Deuteronomy 19 in the IRVT2
Deuteronomy 19 in the IRVU
Deuteronomy 19 in the ISVN
Deuteronomy 19 in the JSNT
Deuteronomy 19 in the KAPI
Deuteronomy 19 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 19 in the KBV
Deuteronomy 19 in the KJV
Deuteronomy 19 in the KNFD
Deuteronomy 19 in the LBA
Deuteronomy 19 in the LBLA
Deuteronomy 19 in the LNT
Deuteronomy 19 in the LSV
Deuteronomy 19 in the MAAL
Deuteronomy 19 in the MBV
Deuteronomy 19 in the MBV2
Deuteronomy 19 in the MHNT
Deuteronomy 19 in the MKNFD
Deuteronomy 19 in the MNG
Deuteronomy 19 in the MNT
Deuteronomy 19 in the MNT2
Deuteronomy 19 in the MRS1T
Deuteronomy 19 in the NAA
Deuteronomy 19 in the NASB
Deuteronomy 19 in the NBLA
Deuteronomy 19 in the NBS
Deuteronomy 19 in the NBVTP
Deuteronomy 19 in the NET2
Deuteronomy 19 in the NIV11
Deuteronomy 19 in the NNT
Deuteronomy 19 in the NNT2
Deuteronomy 19 in the NNT3
Deuteronomy 19 in the PDDPT
Deuteronomy 19 in the PFNT
Deuteronomy 19 in the RMNT
Deuteronomy 19 in the SBIAS
Deuteronomy 19 in the SBIBS
Deuteronomy 19 in the SBIBS2
Deuteronomy 19 in the SBICS
Deuteronomy 19 in the SBIDS
Deuteronomy 19 in the SBIGS
Deuteronomy 19 in the SBIHS
Deuteronomy 19 in the SBIIS
Deuteronomy 19 in the SBIIS2
Deuteronomy 19 in the SBIIS3
Deuteronomy 19 in the SBIKS
Deuteronomy 19 in the SBIKS2
Deuteronomy 19 in the SBIMS
Deuteronomy 19 in the SBIOS
Deuteronomy 19 in the SBIPS
Deuteronomy 19 in the SBISS
Deuteronomy 19 in the SBITS
Deuteronomy 19 in the SBITS2
Deuteronomy 19 in the SBITS3
Deuteronomy 19 in the SBITS4
Deuteronomy 19 in the SBIUS
Deuteronomy 19 in the SBIVS
Deuteronomy 19 in the SBT
Deuteronomy 19 in the SBT1E
Deuteronomy 19 in the SCHL
Deuteronomy 19 in the SNT
Deuteronomy 19 in the SUSU
Deuteronomy 19 in the SUSU2
Deuteronomy 19 in the SYNO
Deuteronomy 19 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 19 in the TBT1E
Deuteronomy 19 in the TBT1E2
Deuteronomy 19 in the TFTIP
Deuteronomy 19 in the TFTU
Deuteronomy 19 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 19 in the THAI
Deuteronomy 19 in the TNFD
Deuteronomy 19 in the TNT
Deuteronomy 19 in the TNTIK
Deuteronomy 19 in the TNTIL
Deuteronomy 19 in the TNTIN
Deuteronomy 19 in the TNTIP
Deuteronomy 19 in the TNTIZ
Deuteronomy 19 in the TOMA
Deuteronomy 19 in the TTENT
Deuteronomy 19 in the UBG
Deuteronomy 19 in the UGV
Deuteronomy 19 in the UGV2
Deuteronomy 19 in the UGV3
Deuteronomy 19 in the VBL
Deuteronomy 19 in the VDCC
Deuteronomy 19 in the YALU
Deuteronomy 19 in the YAPE
Deuteronomy 19 in the YBVTP
Deuteronomy 19 in the ZBP