Deuteronomy 26 (BOGWICC)
1 Mukalowa ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, 2 mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake 3 ndipo mudzamuwuze wansembe amene ali pa ntchito pa nthawiyo kuti, “Ndikunenetsa lero kwa Yehova Mulungu wanu kuti ndabwera ku dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa ife.” 4 Wansembe adzatenga dengulo mʼmanja mwanu ndi kuliyika pansi patsogolo pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 5 Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka. 6 Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga. 7 Kenaka tinafuwulira Yehova, Mulungu wa makolo athu ndipo Yehova anamva mawu athu ndi kuona kusauka, kuvutika ndi kuponderezedwa kwathu. 8 Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa. 9 Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. 10 Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake. 11 Ndipo inu ndi Alevi pamodzi ndi alendo okhala pakati panu mudzakondwera mʼzinthu zonse zabwino zimene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, inu ndi a pa banja panu. 12 Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta. 13 Kenaka munene kwa Yehova Mulungu wanu kuti “Ndatulutsamo mʼnyumba mwanga gawo lopatulika ndipo ndalipereka kwa Mlevi, mlendo, ana ndi akazi amasiye, monga mwa zonse zimene munalamula. Sindinapatuke pa zimene munalamula kapena kuyiwala ndi chimodzi chomwe. 14 Sindinadye kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndimalira maliro kapena kuchotsapo kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndinali wodetsedwa, kapena kuperekako nsembe kwa akufa kalikonse ka gawoli. Ine ndamvera Yehova Mulungu wanga, ndachita chilichonse chimene inu munandilamula. 15 Yangʼanani pa dziko kuchokera kumwamba, ku malo anu wopatulika, ndi kudalitsa anthu anu Aisraeli ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi limene mwatipatsa ife monga momwe munalonjezera pa malumbiro anu kwa makolo athu.” 16 Yehova Mulungu wanu akukulamulani lero lino kuti mutsate malangizo ndi malamulo ake ndipo muwasunge mosamalitsa ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 17 Mwanena motsimikiza lero lino kuti Yehova ndiye Mulungu wanu ndi kuti mudzayenda mʼnjira zake, kusunga malangizo, malamulo ndi zonse akukulamulani ndi kutinso mudzamumvera. 18 Ndipo Yehova wanenetsa lero lino kuti inu ndinu anthu ake, chuma chake chamtengowapatali monga momwe analonjezera, ndipo mukuyenera kusunga malamulo ake onse. 19 Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.
In Other Versions
Deuteronomy 26 in the ANGEFD
Deuteronomy 26 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 26 in the AS21
Deuteronomy 26 in the BAGH
Deuteronomy 26 in the BBPNG
Deuteronomy 26 in the BBT1E
Deuteronomy 26 in the BDS
Deuteronomy 26 in the BEV
Deuteronomy 26 in the BHAD
Deuteronomy 26 in the BIB
Deuteronomy 26 in the BLPT
Deuteronomy 26 in the BNT
Deuteronomy 26 in the BNTABOOT
Deuteronomy 26 in the BNTLV
Deuteronomy 26 in the BOATCB
Deuteronomy 26 in the BOATCB2
Deuteronomy 26 in the BOBCV
Deuteronomy 26 in the BOCNT
Deuteronomy 26 in the BOECS
Deuteronomy 26 in the BOHCB
Deuteronomy 26 in the BOHCV
Deuteronomy 26 in the BOHLNT
Deuteronomy 26 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 26 in the BOICB
Deuteronomy 26 in the BOILNTAP
Deuteronomy 26 in the BOITCV
Deuteronomy 26 in the BOKCV
Deuteronomy 26 in the BOKCV2
Deuteronomy 26 in the BOKHWOG
Deuteronomy 26 in the BOKSSV
Deuteronomy 26 in the BOLCB
Deuteronomy 26 in the BOLCB2
Deuteronomy 26 in the BOMCV
Deuteronomy 26 in the BONAV
Deuteronomy 26 in the BONCB
Deuteronomy 26 in the BONLT
Deuteronomy 26 in the BONUT2
Deuteronomy 26 in the BOPLNT
Deuteronomy 26 in the BOSCB
Deuteronomy 26 in the BOSNC
Deuteronomy 26 in the BOTLNT
Deuteronomy 26 in the BOVCB
Deuteronomy 26 in the BOYCB
Deuteronomy 26 in the BPBB
Deuteronomy 26 in the BPH
Deuteronomy 26 in the BSB
Deuteronomy 26 in the CCB
Deuteronomy 26 in the CUV
Deuteronomy 26 in the CUVS
Deuteronomy 26 in the DBT
Deuteronomy 26 in the DGDNT
Deuteronomy 26 in the DHNT
Deuteronomy 26 in the DNT
Deuteronomy 26 in the ELBE
Deuteronomy 26 in the EMTV
Deuteronomy 26 in the ESV
Deuteronomy 26 in the FBV
Deuteronomy 26 in the FEB
Deuteronomy 26 in the GGMNT
Deuteronomy 26 in the GNT
Deuteronomy 26 in the HARY
Deuteronomy 26 in the HNT
Deuteronomy 26 in the IRVA
Deuteronomy 26 in the IRVB
Deuteronomy 26 in the IRVG
Deuteronomy 26 in the IRVH
Deuteronomy 26 in the IRVK
Deuteronomy 26 in the IRVM
Deuteronomy 26 in the IRVM2
Deuteronomy 26 in the IRVO
Deuteronomy 26 in the IRVP
Deuteronomy 26 in the IRVT
Deuteronomy 26 in the IRVT2
Deuteronomy 26 in the IRVU
Deuteronomy 26 in the ISVN
Deuteronomy 26 in the JSNT
Deuteronomy 26 in the KAPI
Deuteronomy 26 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 26 in the KBV
Deuteronomy 26 in the KJV
Deuteronomy 26 in the KNFD
Deuteronomy 26 in the LBA
Deuteronomy 26 in the LBLA
Deuteronomy 26 in the LNT
Deuteronomy 26 in the LSV
Deuteronomy 26 in the MAAL
Deuteronomy 26 in the MBV
Deuteronomy 26 in the MBV2
Deuteronomy 26 in the MHNT
Deuteronomy 26 in the MKNFD
Deuteronomy 26 in the MNG
Deuteronomy 26 in the MNT
Deuteronomy 26 in the MNT2
Deuteronomy 26 in the MRS1T
Deuteronomy 26 in the NAA
Deuteronomy 26 in the NASB
Deuteronomy 26 in the NBLA
Deuteronomy 26 in the NBS
Deuteronomy 26 in the NBVTP
Deuteronomy 26 in the NET2
Deuteronomy 26 in the NIV11
Deuteronomy 26 in the NNT
Deuteronomy 26 in the NNT2
Deuteronomy 26 in the NNT3
Deuteronomy 26 in the PDDPT
Deuteronomy 26 in the PFNT
Deuteronomy 26 in the RMNT
Deuteronomy 26 in the SBIAS
Deuteronomy 26 in the SBIBS
Deuteronomy 26 in the SBIBS2
Deuteronomy 26 in the SBICS
Deuteronomy 26 in the SBIDS
Deuteronomy 26 in the SBIGS
Deuteronomy 26 in the SBIHS
Deuteronomy 26 in the SBIIS
Deuteronomy 26 in the SBIIS2
Deuteronomy 26 in the SBIIS3
Deuteronomy 26 in the SBIKS
Deuteronomy 26 in the SBIKS2
Deuteronomy 26 in the SBIMS
Deuteronomy 26 in the SBIOS
Deuteronomy 26 in the SBIPS
Deuteronomy 26 in the SBISS
Deuteronomy 26 in the SBITS
Deuteronomy 26 in the SBITS2
Deuteronomy 26 in the SBITS3
Deuteronomy 26 in the SBITS4
Deuteronomy 26 in the SBIUS
Deuteronomy 26 in the SBIVS
Deuteronomy 26 in the SBT
Deuteronomy 26 in the SBT1E
Deuteronomy 26 in the SCHL
Deuteronomy 26 in the SNT
Deuteronomy 26 in the SUSU
Deuteronomy 26 in the SUSU2
Deuteronomy 26 in the SYNO
Deuteronomy 26 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 26 in the TBT1E
Deuteronomy 26 in the TBT1E2
Deuteronomy 26 in the TFTIP
Deuteronomy 26 in the TFTU
Deuteronomy 26 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 26 in the THAI
Deuteronomy 26 in the TNFD
Deuteronomy 26 in the TNT
Deuteronomy 26 in the TNTIK
Deuteronomy 26 in the TNTIL
Deuteronomy 26 in the TNTIN
Deuteronomy 26 in the TNTIP
Deuteronomy 26 in the TNTIZ
Deuteronomy 26 in the TOMA
Deuteronomy 26 in the TTENT
Deuteronomy 26 in the UBG
Deuteronomy 26 in the UGV
Deuteronomy 26 in the UGV2
Deuteronomy 26 in the UGV3
Deuteronomy 26 in the VBL
Deuteronomy 26 in the VDCC
Deuteronomy 26 in the YALU
Deuteronomy 26 in the YAPE
Deuteronomy 26 in the YBVTP
Deuteronomy 26 in the ZBP