Esther 5 (BOGWICC)

1 Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. 2 Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo. 3 Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.” 4 Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.” 5 Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.”Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. 6 Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.” 7 Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: 8 Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.” 9 Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, 10 komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake.Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. 11 Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. 12 Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. 13 Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.” 14 Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.

In Other Versions

Esther 5 in the ANGEFD

Esther 5 in the ANTPNG2D

Esther 5 in the AS21

Esther 5 in the BAGH

Esther 5 in the BBPNG

Esther 5 in the BBT1E

Esther 5 in the BDS

Esther 5 in the BEV

Esther 5 in the BHAD

Esther 5 in the BIB

Esther 5 in the BLPT

Esther 5 in the BNT

Esther 5 in the BNTABOOT

Esther 5 in the BNTLV

Esther 5 in the BOATCB

Esther 5 in the BOATCB2

Esther 5 in the BOBCV

Esther 5 in the BOCNT

Esther 5 in the BOECS

Esther 5 in the BOHCB

Esther 5 in the BOHCV

Esther 5 in the BOHLNT

Esther 5 in the BOHNTLTAL

Esther 5 in the BOICB

Esther 5 in the BOILNTAP

Esther 5 in the BOITCV

Esther 5 in the BOKCV

Esther 5 in the BOKCV2

Esther 5 in the BOKHWOG

Esther 5 in the BOKSSV

Esther 5 in the BOLCB

Esther 5 in the BOLCB2

Esther 5 in the BOMCV

Esther 5 in the BONAV

Esther 5 in the BONCB

Esther 5 in the BONLT

Esther 5 in the BONUT2

Esther 5 in the BOPLNT

Esther 5 in the BOSCB

Esther 5 in the BOSNC

Esther 5 in the BOTLNT

Esther 5 in the BOVCB

Esther 5 in the BOYCB

Esther 5 in the BPBB

Esther 5 in the BPH

Esther 5 in the BSB

Esther 5 in the CCB

Esther 5 in the CUV

Esther 5 in the CUVS

Esther 5 in the DBT

Esther 5 in the DGDNT

Esther 5 in the DHNT

Esther 5 in the DNT

Esther 5 in the ELBE

Esther 5 in the EMTV

Esther 5 in the ESV

Esther 5 in the FBV

Esther 5 in the FEB

Esther 5 in the GGMNT

Esther 5 in the GNT

Esther 5 in the HARY

Esther 5 in the HNT

Esther 5 in the IRVA

Esther 5 in the IRVB

Esther 5 in the IRVG

Esther 5 in the IRVH

Esther 5 in the IRVK

Esther 5 in the IRVM

Esther 5 in the IRVM2

Esther 5 in the IRVO

Esther 5 in the IRVP

Esther 5 in the IRVT

Esther 5 in the IRVT2

Esther 5 in the IRVU

Esther 5 in the ISVN

Esther 5 in the JSNT

Esther 5 in the KAPI

Esther 5 in the KBT1ETNIK

Esther 5 in the KBV

Esther 5 in the KJV

Esther 5 in the KNFD

Esther 5 in the LBA

Esther 5 in the LBLA

Esther 5 in the LNT

Esther 5 in the LSV

Esther 5 in the MAAL

Esther 5 in the MBV

Esther 5 in the MBV2

Esther 5 in the MHNT

Esther 5 in the MKNFD

Esther 5 in the MNG

Esther 5 in the MNT

Esther 5 in the MNT2

Esther 5 in the MRS1T

Esther 5 in the NAA

Esther 5 in the NASB

Esther 5 in the NBLA

Esther 5 in the NBS

Esther 5 in the NBVTP

Esther 5 in the NET2

Esther 5 in the NIV11

Esther 5 in the NNT

Esther 5 in the NNT2

Esther 5 in the NNT3

Esther 5 in the PDDPT

Esther 5 in the PFNT

Esther 5 in the RMNT

Esther 5 in the SBIAS

Esther 5 in the SBIBS

Esther 5 in the SBIBS2

Esther 5 in the SBICS

Esther 5 in the SBIDS

Esther 5 in the SBIGS

Esther 5 in the SBIHS

Esther 5 in the SBIIS

Esther 5 in the SBIIS2

Esther 5 in the SBIIS3

Esther 5 in the SBIKS

Esther 5 in the SBIKS2

Esther 5 in the SBIMS

Esther 5 in the SBIOS

Esther 5 in the SBIPS

Esther 5 in the SBISS

Esther 5 in the SBITS

Esther 5 in the SBITS2

Esther 5 in the SBITS3

Esther 5 in the SBITS4

Esther 5 in the SBIUS

Esther 5 in the SBIVS

Esther 5 in the SBT

Esther 5 in the SBT1E

Esther 5 in the SCHL

Esther 5 in the SNT

Esther 5 in the SUSU

Esther 5 in the SUSU2

Esther 5 in the SYNO

Esther 5 in the TBIAOTANT

Esther 5 in the TBT1E

Esther 5 in the TBT1E2

Esther 5 in the TFTIP

Esther 5 in the TFTU

Esther 5 in the TGNTATF3T

Esther 5 in the THAI

Esther 5 in the TNFD

Esther 5 in the TNT

Esther 5 in the TNTIK

Esther 5 in the TNTIL

Esther 5 in the TNTIN

Esther 5 in the TNTIP

Esther 5 in the TNTIZ

Esther 5 in the TOMA

Esther 5 in the TTENT

Esther 5 in the UBG

Esther 5 in the UGV

Esther 5 in the UGV2

Esther 5 in the UGV3

Esther 5 in the VBL

Esther 5 in the VDCC

Esther 5 in the YALU

Esther 5 in the YAPE

Esther 5 in the YBVTP

Esther 5 in the ZBP