Esther 6 (BOGWICC)
1 Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. 2 Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. 3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.” 4 Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera. 5 Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira. 6 Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” 7 Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: 8 Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. 9 Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ” 10 Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.” 11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!” 12 Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13 Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14 Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.
In Other Versions
Esther 6 in the ANGEFD
Esther 6 in the ANTPNG2D
Esther 6 in the AS21
Esther 6 in the BAGH
Esther 6 in the BBPNG
Esther 6 in the BBT1E
Esther 6 in the BDS
Esther 6 in the BEV
Esther 6 in the BHAD
Esther 6 in the BIB
Esther 6 in the BLPT
Esther 6 in the BNT
Esther 6 in the BNTABOOT
Esther 6 in the BNTLV
Esther 6 in the BOATCB
Esther 6 in the BOATCB2
Esther 6 in the BOBCV
Esther 6 in the BOCNT
Esther 6 in the BOECS
Esther 6 in the BOHCB
Esther 6 in the BOHCV
Esther 6 in the BOHLNT
Esther 6 in the BOHNTLTAL
Esther 6 in the BOICB
Esther 6 in the BOILNTAP
Esther 6 in the BOITCV
Esther 6 in the BOKCV
Esther 6 in the BOKCV2
Esther 6 in the BOKHWOG
Esther 6 in the BOKSSV
Esther 6 in the BOLCB
Esther 6 in the BOLCB2
Esther 6 in the BOMCV
Esther 6 in the BONAV
Esther 6 in the BONCB
Esther 6 in the BONLT
Esther 6 in the BONUT2
Esther 6 in the BOPLNT
Esther 6 in the BOSCB
Esther 6 in the BOSNC
Esther 6 in the BOTLNT
Esther 6 in the BOVCB
Esther 6 in the BOYCB
Esther 6 in the BPBB
Esther 6 in the BPH
Esther 6 in the BSB
Esther 6 in the CCB
Esther 6 in the CUV
Esther 6 in the CUVS
Esther 6 in the DBT
Esther 6 in the DGDNT
Esther 6 in the DHNT
Esther 6 in the DNT
Esther 6 in the ELBE
Esther 6 in the EMTV
Esther 6 in the ESV
Esther 6 in the FBV
Esther 6 in the FEB
Esther 6 in the GGMNT
Esther 6 in the GNT
Esther 6 in the HARY
Esther 6 in the HNT
Esther 6 in the IRVA
Esther 6 in the IRVB
Esther 6 in the IRVG
Esther 6 in the IRVH
Esther 6 in the IRVK
Esther 6 in the IRVM
Esther 6 in the IRVM2
Esther 6 in the IRVO
Esther 6 in the IRVP
Esther 6 in the IRVT
Esther 6 in the IRVT2
Esther 6 in the IRVU
Esther 6 in the ISVN
Esther 6 in the JSNT
Esther 6 in the KAPI
Esther 6 in the KBT1ETNIK
Esther 6 in the KBV
Esther 6 in the KJV
Esther 6 in the KNFD
Esther 6 in the LBA
Esther 6 in the LBLA
Esther 6 in the LNT
Esther 6 in the LSV
Esther 6 in the MAAL
Esther 6 in the MBV
Esther 6 in the MBV2
Esther 6 in the MHNT
Esther 6 in the MKNFD
Esther 6 in the MNG
Esther 6 in the MNT
Esther 6 in the MNT2
Esther 6 in the MRS1T
Esther 6 in the NAA
Esther 6 in the NASB
Esther 6 in the NBLA
Esther 6 in the NBS
Esther 6 in the NBVTP
Esther 6 in the NET2
Esther 6 in the NIV11
Esther 6 in the NNT
Esther 6 in the NNT2
Esther 6 in the NNT3
Esther 6 in the PDDPT
Esther 6 in the PFNT
Esther 6 in the RMNT
Esther 6 in the SBIAS
Esther 6 in the SBIBS
Esther 6 in the SBIBS2
Esther 6 in the SBICS
Esther 6 in the SBIDS
Esther 6 in the SBIGS
Esther 6 in the SBIHS
Esther 6 in the SBIIS
Esther 6 in the SBIIS2
Esther 6 in the SBIIS3
Esther 6 in the SBIKS
Esther 6 in the SBIKS2
Esther 6 in the SBIMS
Esther 6 in the SBIOS
Esther 6 in the SBIPS
Esther 6 in the SBISS
Esther 6 in the SBITS
Esther 6 in the SBITS2
Esther 6 in the SBITS3
Esther 6 in the SBITS4
Esther 6 in the SBIUS
Esther 6 in the SBIVS
Esther 6 in the SBT
Esther 6 in the SBT1E
Esther 6 in the SCHL
Esther 6 in the SNT
Esther 6 in the SUSU
Esther 6 in the SUSU2
Esther 6 in the SYNO
Esther 6 in the TBIAOTANT
Esther 6 in the TBT1E
Esther 6 in the TBT1E2
Esther 6 in the TFTIP
Esther 6 in the TFTU
Esther 6 in the TGNTATF3T
Esther 6 in the THAI
Esther 6 in the TNFD
Esther 6 in the TNT
Esther 6 in the TNTIK
Esther 6 in the TNTIL
Esther 6 in the TNTIN
Esther 6 in the TNTIP
Esther 6 in the TNTIZ
Esther 6 in the TOMA
Esther 6 in the TTENT
Esther 6 in the UBG
Esther 6 in the UGV
Esther 6 in the UGV2
Esther 6 in the UGV3
Esther 6 in the VBL
Esther 6 in the VDCC
Esther 6 in the YALU
Esther 6 in the YAPE
Esther 6 in the YBVTP
Esther 6 in the ZBP