Exodus 1 (BOGWICC)

1 Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake: 2 Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda; 3 Isakara, Zebuloni, Benjamini; 4 Dani, Nafutali; Gadi ndi Aseri. 5 Anthu onse obadwa mwa Yakobo analipo 70. Yosefe nʼkuti ali kale ku Igupto. 6 Tsono Yosefe ndi abale ake onse ndiponso mʼbado wawo wonse anamwalira. 7 Koma Aisraeli anaberekana ndi kuchuluka kwambiri nakhala amphamvu kwambiri, kotero kuti anadzaza dzikolo. 8 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. 9 Iyo inati kwa anthu ake, “Taonani, Aisraeli achuluka ndipo ndi amphamvu kwambiri kuposa ife. 10 Tiyeni tiwachenjerere. Tikapanda kutero adzachuluka kuposa ife, ndipo ngati kutakhala nkhondo, adzadziphatika kwa adani athu nadzamenyana nafe, kenaka nʼkudzachoka mʼdziko muno.” 11 Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya. 12 Koma pamene ankawazunza kwambiri, Aisraeli ndiye ankachulukirachulukira mpaka kubalalikira mʼdziko lonse. Kotero Aigupto anayamba kuopa Aisraeliwo 13 ndipo anawagwiritsa ntchito mwankhanza kwambiri. 14 Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi. 15 Mfumu ya Igupto inati kwa azamba a Chihebri omwe mayina awo anali Sifira ndi Puwa, 16 “Mukamathandiza amayi a Chihebri pa mwala wochirira, muzionetsetsa kuti akabadwa mwana wamwamuna muzipha, koma akakhala wamkazi muzimuleka akhale ndi moyo.” 17 Koma azambawo ankaopa Mulungu ndipo sanachite zimene mfumu ya Igupto inawawuza kuti achite. Iwo analeka ana aamuna kuti akhale ndi moyo. 18 Kenaka mfumu ya Igupto inayitanitsa azamba aja ndi kuwafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? Bwanji mwasiya ana aamuna kuti akhale ndi moyo?” 19 Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.” 20 Kotero Mulungu anawakomera mtima azambawo, ndipo Aisraeli anapitirirabe kuchulukana nakhala amphamvu kwambiri. 21 Pakuti azambawo ankaopa Mulungu, Iye anawapatsa mabanja awoawo. 22 Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.”

In Other Versions

Exodus 1 in the ANGEFD

Exodus 1 in the ANTPNG2D

Exodus 1 in the AS21

Exodus 1 in the BAGH

Exodus 1 in the BBPNG

Exodus 1 in the BBT1E

Exodus 1 in the BDS

Exodus 1 in the BEV

Exodus 1 in the BHAD

Exodus 1 in the BIB

Exodus 1 in the BLPT

Exodus 1 in the BNT

Exodus 1 in the BNTABOOT

Exodus 1 in the BNTLV

Exodus 1 in the BOATCB

Exodus 1 in the BOATCB2

Exodus 1 in the BOBCV

Exodus 1 in the BOCNT

Exodus 1 in the BOECS

Exodus 1 in the BOHCB

Exodus 1 in the BOHCV

Exodus 1 in the BOHLNT

Exodus 1 in the BOHNTLTAL

Exodus 1 in the BOICB

Exodus 1 in the BOILNTAP

Exodus 1 in the BOITCV

Exodus 1 in the BOKCV

Exodus 1 in the BOKCV2

Exodus 1 in the BOKHWOG

Exodus 1 in the BOKSSV

Exodus 1 in the BOLCB

Exodus 1 in the BOLCB2

Exodus 1 in the BOMCV

Exodus 1 in the BONAV

Exodus 1 in the BONCB

Exodus 1 in the BONLT

Exodus 1 in the BONUT2

Exodus 1 in the BOPLNT

Exodus 1 in the BOSCB

Exodus 1 in the BOSNC

Exodus 1 in the BOTLNT

Exodus 1 in the BOVCB

Exodus 1 in the BOYCB

Exodus 1 in the BPBB

Exodus 1 in the BPH

Exodus 1 in the BSB

Exodus 1 in the CCB

Exodus 1 in the CUV

Exodus 1 in the CUVS

Exodus 1 in the DBT

Exodus 1 in the DGDNT

Exodus 1 in the DHNT

Exodus 1 in the DNT

Exodus 1 in the ELBE

Exodus 1 in the EMTV

Exodus 1 in the ESV

Exodus 1 in the FBV

Exodus 1 in the FEB

Exodus 1 in the GGMNT

Exodus 1 in the GNT

Exodus 1 in the HARY

Exodus 1 in the HNT

Exodus 1 in the IRVA

Exodus 1 in the IRVB

Exodus 1 in the IRVG

Exodus 1 in the IRVH

Exodus 1 in the IRVK

Exodus 1 in the IRVM

Exodus 1 in the IRVM2

Exodus 1 in the IRVO

Exodus 1 in the IRVP

Exodus 1 in the IRVT

Exodus 1 in the IRVT2

Exodus 1 in the IRVU

Exodus 1 in the ISVN

Exodus 1 in the JSNT

Exodus 1 in the KAPI

Exodus 1 in the KBT1ETNIK

Exodus 1 in the KBV

Exodus 1 in the KJV

Exodus 1 in the KNFD

Exodus 1 in the LBA

Exodus 1 in the LBLA

Exodus 1 in the LNT

Exodus 1 in the LSV

Exodus 1 in the MAAL

Exodus 1 in the MBV

Exodus 1 in the MBV2

Exodus 1 in the MHNT

Exodus 1 in the MKNFD

Exodus 1 in the MNG

Exodus 1 in the MNT

Exodus 1 in the MNT2

Exodus 1 in the MRS1T

Exodus 1 in the NAA

Exodus 1 in the NASB

Exodus 1 in the NBLA

Exodus 1 in the NBS

Exodus 1 in the NBVTP

Exodus 1 in the NET2

Exodus 1 in the NIV11

Exodus 1 in the NNT

Exodus 1 in the NNT2

Exodus 1 in the NNT3

Exodus 1 in the PDDPT

Exodus 1 in the PFNT

Exodus 1 in the RMNT

Exodus 1 in the SBIAS

Exodus 1 in the SBIBS

Exodus 1 in the SBIBS2

Exodus 1 in the SBICS

Exodus 1 in the SBIDS

Exodus 1 in the SBIGS

Exodus 1 in the SBIHS

Exodus 1 in the SBIIS

Exodus 1 in the SBIIS2

Exodus 1 in the SBIIS3

Exodus 1 in the SBIKS

Exodus 1 in the SBIKS2

Exodus 1 in the SBIMS

Exodus 1 in the SBIOS

Exodus 1 in the SBIPS

Exodus 1 in the SBISS

Exodus 1 in the SBITS

Exodus 1 in the SBITS2

Exodus 1 in the SBITS3

Exodus 1 in the SBITS4

Exodus 1 in the SBIUS

Exodus 1 in the SBIVS

Exodus 1 in the SBT

Exodus 1 in the SBT1E

Exodus 1 in the SCHL

Exodus 1 in the SNT

Exodus 1 in the SUSU

Exodus 1 in the SUSU2

Exodus 1 in the SYNO

Exodus 1 in the TBIAOTANT

Exodus 1 in the TBT1E

Exodus 1 in the TBT1E2

Exodus 1 in the TFTIP

Exodus 1 in the TFTU

Exodus 1 in the TGNTATF3T

Exodus 1 in the THAI

Exodus 1 in the TNFD

Exodus 1 in the TNT

Exodus 1 in the TNTIK

Exodus 1 in the TNTIL

Exodus 1 in the TNTIN

Exodus 1 in the TNTIP

Exodus 1 in the TNTIZ

Exodus 1 in the TOMA

Exodus 1 in the TTENT

Exodus 1 in the UBG

Exodus 1 in the UGV

Exodus 1 in the UGV2

Exodus 1 in the UGV3

Exodus 1 in the VBL

Exodus 1 in the VDCC

Exodus 1 in the YALU

Exodus 1 in the YAPE

Exodus 1 in the YBVTP

Exodus 1 in the ZBP