Exodus 13 (BOGWICC)
1 Yehova anati kwa Mose, 2 “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.” 3 Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti. 4 Pa tsiku la lero mwezi uno wa Abibu, mukutuluka mʼdziko la Igupto. 5 Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno. 6 Muzidzadya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri ndipo tsiku lachisanu ndi chiwirilo muzichita chikondwerero cha Yehova. 7 Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu. 8 Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’ 9 Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu. 10 Muzichita mwambo uwu pa nthawi yake chaka ndi chaka. 11 “Yehova akadzakulowetsani ndi kukupatsani dziko la Kanaani monga analonjezera kwa inu ndi makolo anu, 12 muzikapereka kwa Ambuye ana onse oyamba kubadwa. Ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa ndi za Ambuye. 13 Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola. 14 “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu. 15 Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’ 16 Ndipo chidzakhala kwa inu ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi pamphumi panu kuonetsa kuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.” 17 Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” 18 Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo. 19 Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.” 20 Atachoka ku Sukoti anakagona ku Etamu mʼmphepete mwa chipululu. 21 Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku. 22 Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja.
In Other Versions
Exodus 13 in the ANGEFD
Exodus 13 in the ANTPNG2D
Exodus 13 in the AS21
Exodus 13 in the BAGH
Exodus 13 in the BBPNG
Exodus 13 in the BBT1E
Exodus 13 in the BDS
Exodus 13 in the BEV
Exodus 13 in the BHAD
Exodus 13 in the BIB
Exodus 13 in the BLPT
Exodus 13 in the BNT
Exodus 13 in the BNTABOOT
Exodus 13 in the BNTLV
Exodus 13 in the BOATCB
Exodus 13 in the BOATCB2
Exodus 13 in the BOBCV
Exodus 13 in the BOCNT
Exodus 13 in the BOECS
Exodus 13 in the BOHCB
Exodus 13 in the BOHCV
Exodus 13 in the BOHLNT
Exodus 13 in the BOHNTLTAL
Exodus 13 in the BOICB
Exodus 13 in the BOILNTAP
Exodus 13 in the BOITCV
Exodus 13 in the BOKCV
Exodus 13 in the BOKCV2
Exodus 13 in the BOKHWOG
Exodus 13 in the BOKSSV
Exodus 13 in the BOLCB
Exodus 13 in the BOLCB2
Exodus 13 in the BOMCV
Exodus 13 in the BONAV
Exodus 13 in the BONCB
Exodus 13 in the BONLT
Exodus 13 in the BONUT2
Exodus 13 in the BOPLNT
Exodus 13 in the BOSCB
Exodus 13 in the BOSNC
Exodus 13 in the BOTLNT
Exodus 13 in the BOVCB
Exodus 13 in the BOYCB
Exodus 13 in the BPBB
Exodus 13 in the BPH
Exodus 13 in the BSB
Exodus 13 in the CCB
Exodus 13 in the CUV
Exodus 13 in the CUVS
Exodus 13 in the DBT
Exodus 13 in the DGDNT
Exodus 13 in the DHNT
Exodus 13 in the DNT
Exodus 13 in the ELBE
Exodus 13 in the EMTV
Exodus 13 in the ESV
Exodus 13 in the FBV
Exodus 13 in the FEB
Exodus 13 in the GGMNT
Exodus 13 in the GNT
Exodus 13 in the HARY
Exodus 13 in the HNT
Exodus 13 in the IRVA
Exodus 13 in the IRVB
Exodus 13 in the IRVG
Exodus 13 in the IRVH
Exodus 13 in the IRVK
Exodus 13 in the IRVM
Exodus 13 in the IRVM2
Exodus 13 in the IRVO
Exodus 13 in the IRVP
Exodus 13 in the IRVT
Exodus 13 in the IRVT2
Exodus 13 in the IRVU
Exodus 13 in the ISVN
Exodus 13 in the JSNT
Exodus 13 in the KAPI
Exodus 13 in the KBT1ETNIK
Exodus 13 in the KBV
Exodus 13 in the KJV
Exodus 13 in the KNFD
Exodus 13 in the LBA
Exodus 13 in the LBLA
Exodus 13 in the LNT
Exodus 13 in the LSV
Exodus 13 in the MAAL
Exodus 13 in the MBV
Exodus 13 in the MBV2
Exodus 13 in the MHNT
Exodus 13 in the MKNFD
Exodus 13 in the MNG
Exodus 13 in the MNT
Exodus 13 in the MNT2
Exodus 13 in the MRS1T
Exodus 13 in the NAA
Exodus 13 in the NASB
Exodus 13 in the NBLA
Exodus 13 in the NBS
Exodus 13 in the NBVTP
Exodus 13 in the NET2
Exodus 13 in the NIV11
Exodus 13 in the NNT
Exodus 13 in the NNT2
Exodus 13 in the NNT3
Exodus 13 in the PDDPT
Exodus 13 in the PFNT
Exodus 13 in the RMNT
Exodus 13 in the SBIAS
Exodus 13 in the SBIBS
Exodus 13 in the SBIBS2
Exodus 13 in the SBICS
Exodus 13 in the SBIDS
Exodus 13 in the SBIGS
Exodus 13 in the SBIHS
Exodus 13 in the SBIIS
Exodus 13 in the SBIIS2
Exodus 13 in the SBIIS3
Exodus 13 in the SBIKS
Exodus 13 in the SBIKS2
Exodus 13 in the SBIMS
Exodus 13 in the SBIOS
Exodus 13 in the SBIPS
Exodus 13 in the SBISS
Exodus 13 in the SBITS
Exodus 13 in the SBITS2
Exodus 13 in the SBITS3
Exodus 13 in the SBITS4
Exodus 13 in the SBIUS
Exodus 13 in the SBIVS
Exodus 13 in the SBT
Exodus 13 in the SBT1E
Exodus 13 in the SCHL
Exodus 13 in the SNT
Exodus 13 in the SUSU
Exodus 13 in the SUSU2
Exodus 13 in the SYNO
Exodus 13 in the TBIAOTANT
Exodus 13 in the TBT1E
Exodus 13 in the TBT1E2
Exodus 13 in the TFTIP
Exodus 13 in the TFTU
Exodus 13 in the TGNTATF3T
Exodus 13 in the THAI
Exodus 13 in the TNFD
Exodus 13 in the TNT
Exodus 13 in the TNTIK
Exodus 13 in the TNTIL
Exodus 13 in the TNTIN
Exodus 13 in the TNTIP
Exodus 13 in the TNTIZ
Exodus 13 in the TOMA
Exodus 13 in the TTENT
Exodus 13 in the UBG
Exodus 13 in the UGV
Exodus 13 in the UGV2
Exodus 13 in the UGV3
Exodus 13 in the VBL
Exodus 13 in the VDCC
Exodus 13 in the YALU
Exodus 13 in the YAPE
Exodus 13 in the YBVTP
Exodus 13 in the ZBP