Exodus 20 (BOGWICC)
1 Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati: 2 “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. 3 “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” 4 “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 5 Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. 6 Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga. 7 “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika. 8 “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. 9 Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11 Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera. 12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 13 “Usaphe. 14 “Usachite chigololo. 15 “Usabe. 16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako. 17 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” 18 Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.” 20 Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.” 21 Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu. 22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. 23 Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ” 24 Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. 25 Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida. 26 Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu.
In Other Versions
Exodus 20 in the ANGEFD
Exodus 20 in the ANTPNG2D
Exodus 20 in the AS21
Exodus 20 in the BAGH
Exodus 20 in the BBPNG
Exodus 20 in the BBT1E
Exodus 20 in the BDS
Exodus 20 in the BEV
Exodus 20 in the BHAD
Exodus 20 in the BIB
Exodus 20 in the BLPT
Exodus 20 in the BNT
Exodus 20 in the BNTABOOT
Exodus 20 in the BNTLV
Exodus 20 in the BOATCB
Exodus 20 in the BOATCB2
Exodus 20 in the BOBCV
Exodus 20 in the BOCNT
Exodus 20 in the BOECS
Exodus 20 in the BOHCB
Exodus 20 in the BOHCV
Exodus 20 in the BOHLNT
Exodus 20 in the BOHNTLTAL
Exodus 20 in the BOICB
Exodus 20 in the BOILNTAP
Exodus 20 in the BOITCV
Exodus 20 in the BOKCV
Exodus 20 in the BOKCV2
Exodus 20 in the BOKHWOG
Exodus 20 in the BOKSSV
Exodus 20 in the BOLCB
Exodus 20 in the BOLCB2
Exodus 20 in the BOMCV
Exodus 20 in the BONAV
Exodus 20 in the BONCB
Exodus 20 in the BONLT
Exodus 20 in the BONUT2
Exodus 20 in the BOPLNT
Exodus 20 in the BOSCB
Exodus 20 in the BOSNC
Exodus 20 in the BOTLNT
Exodus 20 in the BOVCB
Exodus 20 in the BOYCB
Exodus 20 in the BPBB
Exodus 20 in the BPH
Exodus 20 in the BSB
Exodus 20 in the CCB
Exodus 20 in the CUV
Exodus 20 in the CUVS
Exodus 20 in the DBT
Exodus 20 in the DGDNT
Exodus 20 in the DHNT
Exodus 20 in the DNT
Exodus 20 in the ELBE
Exodus 20 in the EMTV
Exodus 20 in the ESV
Exodus 20 in the FBV
Exodus 20 in the FEB
Exodus 20 in the GGMNT
Exodus 20 in the GNT
Exodus 20 in the HARY
Exodus 20 in the HNT
Exodus 20 in the IRVA
Exodus 20 in the IRVB
Exodus 20 in the IRVG
Exodus 20 in the IRVH
Exodus 20 in the IRVK
Exodus 20 in the IRVM
Exodus 20 in the IRVM2
Exodus 20 in the IRVO
Exodus 20 in the IRVP
Exodus 20 in the IRVT
Exodus 20 in the IRVT2
Exodus 20 in the IRVU
Exodus 20 in the ISVN
Exodus 20 in the JSNT
Exodus 20 in the KAPI
Exodus 20 in the KBT1ETNIK
Exodus 20 in the KBV
Exodus 20 in the KJV
Exodus 20 in the KNFD
Exodus 20 in the LBA
Exodus 20 in the LBLA
Exodus 20 in the LNT
Exodus 20 in the LSV
Exodus 20 in the MAAL
Exodus 20 in the MBV
Exodus 20 in the MBV2
Exodus 20 in the MHNT
Exodus 20 in the MKNFD
Exodus 20 in the MNG
Exodus 20 in the MNT
Exodus 20 in the MNT2
Exodus 20 in the MRS1T
Exodus 20 in the NAA
Exodus 20 in the NASB
Exodus 20 in the NBLA
Exodus 20 in the NBS
Exodus 20 in the NBVTP
Exodus 20 in the NET2
Exodus 20 in the NIV11
Exodus 20 in the NNT
Exodus 20 in the NNT2
Exodus 20 in the NNT3
Exodus 20 in the PDDPT
Exodus 20 in the PFNT
Exodus 20 in the RMNT
Exodus 20 in the SBIAS
Exodus 20 in the SBIBS
Exodus 20 in the SBIBS2
Exodus 20 in the SBICS
Exodus 20 in the SBIDS
Exodus 20 in the SBIGS
Exodus 20 in the SBIHS
Exodus 20 in the SBIIS
Exodus 20 in the SBIIS2
Exodus 20 in the SBIIS3
Exodus 20 in the SBIKS
Exodus 20 in the SBIKS2
Exodus 20 in the SBIMS
Exodus 20 in the SBIOS
Exodus 20 in the SBIPS
Exodus 20 in the SBISS
Exodus 20 in the SBITS
Exodus 20 in the SBITS2
Exodus 20 in the SBITS3
Exodus 20 in the SBITS4
Exodus 20 in the SBIUS
Exodus 20 in the SBIVS
Exodus 20 in the SBT
Exodus 20 in the SBT1E
Exodus 20 in the SCHL
Exodus 20 in the SNT
Exodus 20 in the SUSU
Exodus 20 in the SUSU2
Exodus 20 in the SYNO
Exodus 20 in the TBIAOTANT
Exodus 20 in the TBT1E
Exodus 20 in the TBT1E2
Exodus 20 in the TFTIP
Exodus 20 in the TFTU
Exodus 20 in the TGNTATF3T
Exodus 20 in the THAI
Exodus 20 in the TNFD
Exodus 20 in the TNT
Exodus 20 in the TNTIK
Exodus 20 in the TNTIL
Exodus 20 in the TNTIN
Exodus 20 in the TNTIP
Exodus 20 in the TNTIZ
Exodus 20 in the TOMA
Exodus 20 in the TTENT
Exodus 20 in the UBG
Exodus 20 in the UGV
Exodus 20 in the UGV2
Exodus 20 in the UGV3
Exodus 20 in the VBL
Exodus 20 in the VDCC
Exodus 20 in the YALU
Exodus 20 in the YAPE
Exodus 20 in the YBVTP
Exodus 20 in the ZBP