Exodus 40 (BOGWICC)
1 Kenaka Yehova anati kwa Mose, 2 “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi. 3 Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani. 4 Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake. 5 Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema. 6 “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano. 7 Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi. 8 Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo. 9 “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa. 10 Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri. 11 Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule. 12 “Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. 13 Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe. 14 Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro. 15 Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado” 16 Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira. 17 Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri. 18 Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi. 19 Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose. 20 Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake. 21 Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye. 22 Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani, 23 ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose. 24 Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema. 25 Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose. 26 Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani 27 ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira. 28 Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema. 29 Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira. 30 Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba, 31 ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo. 32 Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose. 33 Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito. 34 Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. 35 Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. 36 Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. 37 Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke. 38 Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.
In Other Versions
Exodus 40 in the ANGEFD
Exodus 40 in the ANTPNG2D
Exodus 40 in the AS21
Exodus 40 in the BAGH
Exodus 40 in the BBPNG
Exodus 40 in the BBT1E
Exodus 40 in the BDS
Exodus 40 in the BEV
Exodus 40 in the BHAD
Exodus 40 in the BIB
Exodus 40 in the BLPT
Exodus 40 in the BNT
Exodus 40 in the BNTABOOT
Exodus 40 in the BNTLV
Exodus 40 in the BOATCB
Exodus 40 in the BOATCB2
Exodus 40 in the BOBCV
Exodus 40 in the BOCNT
Exodus 40 in the BOECS
Exodus 40 in the BOHCB
Exodus 40 in the BOHCV
Exodus 40 in the BOHLNT
Exodus 40 in the BOHNTLTAL
Exodus 40 in the BOICB
Exodus 40 in the BOILNTAP
Exodus 40 in the BOITCV
Exodus 40 in the BOKCV
Exodus 40 in the BOKCV2
Exodus 40 in the BOKHWOG
Exodus 40 in the BOKSSV
Exodus 40 in the BOLCB
Exodus 40 in the BOLCB2
Exodus 40 in the BOMCV
Exodus 40 in the BONAV
Exodus 40 in the BONCB
Exodus 40 in the BONLT
Exodus 40 in the BONUT2
Exodus 40 in the BOPLNT
Exodus 40 in the BOSCB
Exodus 40 in the BOSNC
Exodus 40 in the BOTLNT
Exodus 40 in the BOVCB
Exodus 40 in the BOYCB
Exodus 40 in the BPBB
Exodus 40 in the BPH
Exodus 40 in the BSB
Exodus 40 in the CCB
Exodus 40 in the CUV
Exodus 40 in the CUVS
Exodus 40 in the DBT
Exodus 40 in the DGDNT
Exodus 40 in the DHNT
Exodus 40 in the DNT
Exodus 40 in the ELBE
Exodus 40 in the EMTV
Exodus 40 in the ESV
Exodus 40 in the FBV
Exodus 40 in the FEB
Exodus 40 in the GGMNT
Exodus 40 in the GNT
Exodus 40 in the HARY
Exodus 40 in the HNT
Exodus 40 in the IRVA
Exodus 40 in the IRVB
Exodus 40 in the IRVG
Exodus 40 in the IRVH
Exodus 40 in the IRVK
Exodus 40 in the IRVM
Exodus 40 in the IRVM2
Exodus 40 in the IRVO
Exodus 40 in the IRVP
Exodus 40 in the IRVT
Exodus 40 in the IRVT2
Exodus 40 in the IRVU
Exodus 40 in the ISVN
Exodus 40 in the JSNT
Exodus 40 in the KAPI
Exodus 40 in the KBT1ETNIK
Exodus 40 in the KBV
Exodus 40 in the KJV
Exodus 40 in the KNFD
Exodus 40 in the LBA
Exodus 40 in the LBLA
Exodus 40 in the LNT
Exodus 40 in the LSV
Exodus 40 in the MAAL
Exodus 40 in the MBV
Exodus 40 in the MBV2
Exodus 40 in the MHNT
Exodus 40 in the MKNFD
Exodus 40 in the MNG
Exodus 40 in the MNT
Exodus 40 in the MNT2
Exodus 40 in the MRS1T
Exodus 40 in the NAA
Exodus 40 in the NASB
Exodus 40 in the NBLA
Exodus 40 in the NBS
Exodus 40 in the NBVTP
Exodus 40 in the NET2
Exodus 40 in the NIV11
Exodus 40 in the NNT
Exodus 40 in the NNT2
Exodus 40 in the NNT3
Exodus 40 in the PDDPT
Exodus 40 in the PFNT
Exodus 40 in the RMNT
Exodus 40 in the SBIAS
Exodus 40 in the SBIBS
Exodus 40 in the SBIBS2
Exodus 40 in the SBICS
Exodus 40 in the SBIDS
Exodus 40 in the SBIGS
Exodus 40 in the SBIHS
Exodus 40 in the SBIIS
Exodus 40 in the SBIIS2
Exodus 40 in the SBIIS3
Exodus 40 in the SBIKS
Exodus 40 in the SBIKS2
Exodus 40 in the SBIMS
Exodus 40 in the SBIOS
Exodus 40 in the SBIPS
Exodus 40 in the SBISS
Exodus 40 in the SBITS
Exodus 40 in the SBITS2
Exodus 40 in the SBITS3
Exodus 40 in the SBITS4
Exodus 40 in the SBIUS
Exodus 40 in the SBIVS
Exodus 40 in the SBT
Exodus 40 in the SBT1E
Exodus 40 in the SCHL
Exodus 40 in the SNT
Exodus 40 in the SUSU
Exodus 40 in the SUSU2
Exodus 40 in the SYNO
Exodus 40 in the TBIAOTANT
Exodus 40 in the TBT1E
Exodus 40 in the TBT1E2
Exodus 40 in the TFTIP
Exodus 40 in the TFTU
Exodus 40 in the TGNTATF3T
Exodus 40 in the THAI
Exodus 40 in the TNFD
Exodus 40 in the TNT
Exodus 40 in the TNTIK
Exodus 40 in the TNTIL
Exodus 40 in the TNTIN
Exodus 40 in the TNTIP
Exodus 40 in the TNTIZ
Exodus 40 in the TOMA
Exodus 40 in the TTENT
Exodus 40 in the UBG
Exodus 40 in the UGV
Exodus 40 in the UGV2
Exodus 40 in the UGV3
Exodus 40 in the VBL
Exodus 40 in the VDCC
Exodus 40 in the YALU
Exodus 40 in the YAPE
Exodus 40 in the YBVTP
Exodus 40 in the ZBP