Exodus 5 (BOGWICC)
1 Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ” 2 Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.” 3 Ndipo iwo anati, “Mulungu wa Ahebri anakumana nafe. Chonde tiloleni tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, ngati sititero iye adzatipweteka ndi miliri kapena lupanga.” 4 Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!” 5 Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.” 6 Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti 7 “Inu musawapatsenso udzu wopangira njerwa monga mumachitira kale, iwo azipita ndi kukatenga udzu wawo. 8 Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ 9 Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.” 10 Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu. 11 Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’ ” 12 Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu. 13 Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.” 14 Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?” 15 Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere? 16 Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.” 17 Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ 18 Pitani tsopano kuntchito. Simudzapatsidwanso udzu komabe muyenera kuwumba muyeso wanu wovomerezeka wa njerwa.” 19 Oyangʼanira anzawo a Chiisraeli anazindikira kuti ali pa mavuto pamene anawuzidwa kuti, “Musachepetse chiwerengero cha njerwa chimene muyenera kuwumba tsiku lililonse.” 20 Atachoka pamaso pa Farao, anakumana ndi Mose ndi Aaroni akuwadikira, 21 ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.” 22 Mose anabwerera kwa Yehova ndipo anati, “Chonde Ambuye, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Kodi munanditumira zimenezi? 23 Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.”
In Other Versions
Exodus 5 in the ANGEFD
Exodus 5 in the ANTPNG2D
Exodus 5 in the AS21
Exodus 5 in the BAGH
Exodus 5 in the BBPNG
Exodus 5 in the BBT1E
Exodus 5 in the BDS
Exodus 5 in the BEV
Exodus 5 in the BHAD
Exodus 5 in the BIB
Exodus 5 in the BLPT
Exodus 5 in the BNT
Exodus 5 in the BNTABOOT
Exodus 5 in the BNTLV
Exodus 5 in the BOATCB
Exodus 5 in the BOATCB2
Exodus 5 in the BOBCV
Exodus 5 in the BOCNT
Exodus 5 in the BOECS
Exodus 5 in the BOHCB
Exodus 5 in the BOHCV
Exodus 5 in the BOHLNT
Exodus 5 in the BOHNTLTAL
Exodus 5 in the BOICB
Exodus 5 in the BOILNTAP
Exodus 5 in the BOITCV
Exodus 5 in the BOKCV
Exodus 5 in the BOKCV2
Exodus 5 in the BOKHWOG
Exodus 5 in the BOKSSV
Exodus 5 in the BOLCB
Exodus 5 in the BOLCB2
Exodus 5 in the BOMCV
Exodus 5 in the BONAV
Exodus 5 in the BONCB
Exodus 5 in the BONLT
Exodus 5 in the BONUT2
Exodus 5 in the BOPLNT
Exodus 5 in the BOSCB
Exodus 5 in the BOSNC
Exodus 5 in the BOTLNT
Exodus 5 in the BOVCB
Exodus 5 in the BOYCB
Exodus 5 in the BPBB
Exodus 5 in the BPH
Exodus 5 in the BSB
Exodus 5 in the CCB
Exodus 5 in the CUV
Exodus 5 in the CUVS
Exodus 5 in the DBT
Exodus 5 in the DGDNT
Exodus 5 in the DHNT
Exodus 5 in the DNT
Exodus 5 in the ELBE
Exodus 5 in the EMTV
Exodus 5 in the ESV
Exodus 5 in the FBV
Exodus 5 in the FEB
Exodus 5 in the GGMNT
Exodus 5 in the GNT
Exodus 5 in the HARY
Exodus 5 in the HNT
Exodus 5 in the IRVA
Exodus 5 in the IRVB
Exodus 5 in the IRVG
Exodus 5 in the IRVH
Exodus 5 in the IRVK
Exodus 5 in the IRVM
Exodus 5 in the IRVM2
Exodus 5 in the IRVO
Exodus 5 in the IRVP
Exodus 5 in the IRVT
Exodus 5 in the IRVT2
Exodus 5 in the IRVU
Exodus 5 in the ISVN
Exodus 5 in the JSNT
Exodus 5 in the KAPI
Exodus 5 in the KBT1ETNIK
Exodus 5 in the KBV
Exodus 5 in the KJV
Exodus 5 in the KNFD
Exodus 5 in the LBA
Exodus 5 in the LBLA
Exodus 5 in the LNT
Exodus 5 in the LSV
Exodus 5 in the MAAL
Exodus 5 in the MBV
Exodus 5 in the MBV2
Exodus 5 in the MHNT
Exodus 5 in the MKNFD
Exodus 5 in the MNG
Exodus 5 in the MNT
Exodus 5 in the MNT2
Exodus 5 in the MRS1T
Exodus 5 in the NAA
Exodus 5 in the NASB
Exodus 5 in the NBLA
Exodus 5 in the NBS
Exodus 5 in the NBVTP
Exodus 5 in the NET2
Exodus 5 in the NIV11
Exodus 5 in the NNT
Exodus 5 in the NNT2
Exodus 5 in the NNT3
Exodus 5 in the PDDPT
Exodus 5 in the PFNT
Exodus 5 in the RMNT
Exodus 5 in the SBIAS
Exodus 5 in the SBIBS
Exodus 5 in the SBIBS2
Exodus 5 in the SBICS
Exodus 5 in the SBIDS
Exodus 5 in the SBIGS
Exodus 5 in the SBIHS
Exodus 5 in the SBIIS
Exodus 5 in the SBIIS2
Exodus 5 in the SBIIS3
Exodus 5 in the SBIKS
Exodus 5 in the SBIKS2
Exodus 5 in the SBIMS
Exodus 5 in the SBIOS
Exodus 5 in the SBIPS
Exodus 5 in the SBISS
Exodus 5 in the SBITS
Exodus 5 in the SBITS2
Exodus 5 in the SBITS3
Exodus 5 in the SBITS4
Exodus 5 in the SBIUS
Exodus 5 in the SBIVS
Exodus 5 in the SBT
Exodus 5 in the SBT1E
Exodus 5 in the SCHL
Exodus 5 in the SNT
Exodus 5 in the SUSU
Exodus 5 in the SUSU2
Exodus 5 in the SYNO
Exodus 5 in the TBIAOTANT
Exodus 5 in the TBT1E
Exodus 5 in the TBT1E2
Exodus 5 in the TFTIP
Exodus 5 in the TFTU
Exodus 5 in the TGNTATF3T
Exodus 5 in the THAI
Exodus 5 in the TNFD
Exodus 5 in the TNT
Exodus 5 in the TNTIK
Exodus 5 in the TNTIL
Exodus 5 in the TNTIN
Exodus 5 in the TNTIP
Exodus 5 in the TNTIZ
Exodus 5 in the TOMA
Exodus 5 in the TTENT
Exodus 5 in the UBG
Exodus 5 in the UGV
Exodus 5 in the UGV2
Exodus 5 in the UGV3
Exodus 5 in the VBL
Exodus 5 in the VDCC
Exodus 5 in the YALU
Exodus 5 in the YAPE
Exodus 5 in the YBVTP
Exodus 5 in the ZBP