Exodus 6 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.” 2 Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova. 3 Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova. 4 Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo. 5 Ndamvanso kubuwula kwa Aisraeli, amene Aigupto awayesa akapolo ndipo ndakumbukira pangano langa.” 6 “Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo. 7 Ndidzakutengani kukhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼgoli la Aigupto. 8 Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanu. Ine ndine Yehova.’ ” 9 Mose anawafotokozera Aisraeli zimenezi, koma iwo sanamumvere chifukwa cha kukhumudwa ndi goli lankhanza. 10 Kenaka Yehova anati kwa Mose, 11 “Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.” 12 Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?” 13 Ndipo Yehova analamula Mose ndi Aaroni kuti awuze Aisraeli ndi Farao mfumu ya Igupto kuti Aisraeli ayenera kutuluka mʼdziko la Igupto. 14 Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni. 15 Ana a Simeoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Saulo mwana wa kwa mkazi wa Chikanaani. Awa anali mafuko a Simeoni. 16 Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. 17 Ana a Geresoni, mwa mafuko awo, anali Libini ndi Simei. 18 Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. 19 Ana a Merari anali Mali ndi Musi.Awa anali mafuko a Levi monga mwa mibado yawo. 20 Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137. 21 Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri. 22 Ana a Uzieli anali Misaeli, Elizafani ndi Sitiri. 23 Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 24 Ana a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu. Awa ndiwo mafuko a Kora. 25 Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi. Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo. 26 Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.” 27 Mose ndi Aaroni ndiwo amene anayankhula ndi Farao mfumu ya Igupto kuti atulutse Aisraeli mu Igupto. 28 Tsopano pamene Yehova anayankhula kwa Mose mu Igupto, 29 anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.” 30 Koma Mose anati kwa Yehova, “Farao akandimvera bwanji, pakuti ine sinditha kuyankhula bwino?”

In Other Versions

Exodus 6 in the ANGEFD

Exodus 6 in the ANTPNG2D

Exodus 6 in the AS21

Exodus 6 in the BAGH

Exodus 6 in the BBPNG

Exodus 6 in the BBT1E

Exodus 6 in the BDS

Exodus 6 in the BEV

Exodus 6 in the BHAD

Exodus 6 in the BIB

Exodus 6 in the BLPT

Exodus 6 in the BNT

Exodus 6 in the BNTABOOT

Exodus 6 in the BNTLV

Exodus 6 in the BOATCB

Exodus 6 in the BOATCB2

Exodus 6 in the BOBCV

Exodus 6 in the BOCNT

Exodus 6 in the BOECS

Exodus 6 in the BOHCB

Exodus 6 in the BOHCV

Exodus 6 in the BOHLNT

Exodus 6 in the BOHNTLTAL

Exodus 6 in the BOICB

Exodus 6 in the BOILNTAP

Exodus 6 in the BOITCV

Exodus 6 in the BOKCV

Exodus 6 in the BOKCV2

Exodus 6 in the BOKHWOG

Exodus 6 in the BOKSSV

Exodus 6 in the BOLCB

Exodus 6 in the BOLCB2

Exodus 6 in the BOMCV

Exodus 6 in the BONAV

Exodus 6 in the BONCB

Exodus 6 in the BONLT

Exodus 6 in the BONUT2

Exodus 6 in the BOPLNT

Exodus 6 in the BOSCB

Exodus 6 in the BOSNC

Exodus 6 in the BOTLNT

Exodus 6 in the BOVCB

Exodus 6 in the BOYCB

Exodus 6 in the BPBB

Exodus 6 in the BPH

Exodus 6 in the BSB

Exodus 6 in the CCB

Exodus 6 in the CUV

Exodus 6 in the CUVS

Exodus 6 in the DBT

Exodus 6 in the DGDNT

Exodus 6 in the DHNT

Exodus 6 in the DNT

Exodus 6 in the ELBE

Exodus 6 in the EMTV

Exodus 6 in the ESV

Exodus 6 in the FBV

Exodus 6 in the FEB

Exodus 6 in the GGMNT

Exodus 6 in the GNT

Exodus 6 in the HARY

Exodus 6 in the HNT

Exodus 6 in the IRVA

Exodus 6 in the IRVB

Exodus 6 in the IRVG

Exodus 6 in the IRVH

Exodus 6 in the IRVK

Exodus 6 in the IRVM

Exodus 6 in the IRVM2

Exodus 6 in the IRVO

Exodus 6 in the IRVP

Exodus 6 in the IRVT

Exodus 6 in the IRVT2

Exodus 6 in the IRVU

Exodus 6 in the ISVN

Exodus 6 in the JSNT

Exodus 6 in the KAPI

Exodus 6 in the KBT1ETNIK

Exodus 6 in the KBV

Exodus 6 in the KJV

Exodus 6 in the KNFD

Exodus 6 in the LBA

Exodus 6 in the LBLA

Exodus 6 in the LNT

Exodus 6 in the LSV

Exodus 6 in the MAAL

Exodus 6 in the MBV

Exodus 6 in the MBV2

Exodus 6 in the MHNT

Exodus 6 in the MKNFD

Exodus 6 in the MNG

Exodus 6 in the MNT

Exodus 6 in the MNT2

Exodus 6 in the MRS1T

Exodus 6 in the NAA

Exodus 6 in the NASB

Exodus 6 in the NBLA

Exodus 6 in the NBS

Exodus 6 in the NBVTP

Exodus 6 in the NET2

Exodus 6 in the NIV11

Exodus 6 in the NNT

Exodus 6 in the NNT2

Exodus 6 in the NNT3

Exodus 6 in the PDDPT

Exodus 6 in the PFNT

Exodus 6 in the RMNT

Exodus 6 in the SBIAS

Exodus 6 in the SBIBS

Exodus 6 in the SBIBS2

Exodus 6 in the SBICS

Exodus 6 in the SBIDS

Exodus 6 in the SBIGS

Exodus 6 in the SBIHS

Exodus 6 in the SBIIS

Exodus 6 in the SBIIS2

Exodus 6 in the SBIIS3

Exodus 6 in the SBIKS

Exodus 6 in the SBIKS2

Exodus 6 in the SBIMS

Exodus 6 in the SBIOS

Exodus 6 in the SBIPS

Exodus 6 in the SBISS

Exodus 6 in the SBITS

Exodus 6 in the SBITS2

Exodus 6 in the SBITS3

Exodus 6 in the SBITS4

Exodus 6 in the SBIUS

Exodus 6 in the SBIVS

Exodus 6 in the SBT

Exodus 6 in the SBT1E

Exodus 6 in the SCHL

Exodus 6 in the SNT

Exodus 6 in the SUSU

Exodus 6 in the SUSU2

Exodus 6 in the SYNO

Exodus 6 in the TBIAOTANT

Exodus 6 in the TBT1E

Exodus 6 in the TBT1E2

Exodus 6 in the TFTIP

Exodus 6 in the TFTU

Exodus 6 in the TGNTATF3T

Exodus 6 in the THAI

Exodus 6 in the TNFD

Exodus 6 in the TNT

Exodus 6 in the TNTIK

Exodus 6 in the TNTIL

Exodus 6 in the TNTIN

Exodus 6 in the TNTIP

Exodus 6 in the TNTIZ

Exodus 6 in the TOMA

Exodus 6 in the TTENT

Exodus 6 in the UBG

Exodus 6 in the UGV

Exodus 6 in the UGV2

Exodus 6 in the UGV3

Exodus 6 in the VBL

Exodus 6 in the VDCC

Exodus 6 in the YALU

Exodus 6 in the YAPE

Exodus 6 in the YBVTP

Exodus 6 in the ZBP