Ezekiel 10 (BOGWICC)
1 Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro. 2 Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona. 3 Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati. 4 Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo. 5 Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula. 6 Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi. 7 Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka. 8 Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu. 9 Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti. 10 Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake. 11 Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka. 12 Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija. 13 Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.” 14 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga. 15 Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. 16 Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo. 17 Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo. 18 Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi. 19 Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 20 Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi. 21 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu. 22 Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.
In Other Versions
Ezekiel 10 in the ANGEFD
Ezekiel 10 in the ANTPNG2D
Ezekiel 10 in the AS21
Ezekiel 10 in the BAGH
Ezekiel 10 in the BBPNG
Ezekiel 10 in the BBT1E
Ezekiel 10 in the BDS
Ezekiel 10 in the BEV
Ezekiel 10 in the BHAD
Ezekiel 10 in the BIB
Ezekiel 10 in the BLPT
Ezekiel 10 in the BNT
Ezekiel 10 in the BNTABOOT
Ezekiel 10 in the BNTLV
Ezekiel 10 in the BOATCB
Ezekiel 10 in the BOATCB2
Ezekiel 10 in the BOBCV
Ezekiel 10 in the BOCNT
Ezekiel 10 in the BOECS
Ezekiel 10 in the BOHCB
Ezekiel 10 in the BOHCV
Ezekiel 10 in the BOHLNT
Ezekiel 10 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 10 in the BOICB
Ezekiel 10 in the BOILNTAP
Ezekiel 10 in the BOITCV
Ezekiel 10 in the BOKCV
Ezekiel 10 in the BOKCV2
Ezekiel 10 in the BOKHWOG
Ezekiel 10 in the BOKSSV
Ezekiel 10 in the BOLCB
Ezekiel 10 in the BOLCB2
Ezekiel 10 in the BOMCV
Ezekiel 10 in the BONAV
Ezekiel 10 in the BONCB
Ezekiel 10 in the BONLT
Ezekiel 10 in the BONUT2
Ezekiel 10 in the BOPLNT
Ezekiel 10 in the BOSCB
Ezekiel 10 in the BOSNC
Ezekiel 10 in the BOTLNT
Ezekiel 10 in the BOVCB
Ezekiel 10 in the BOYCB
Ezekiel 10 in the BPBB
Ezekiel 10 in the BPH
Ezekiel 10 in the BSB
Ezekiel 10 in the CCB
Ezekiel 10 in the CUV
Ezekiel 10 in the CUVS
Ezekiel 10 in the DBT
Ezekiel 10 in the DGDNT
Ezekiel 10 in the DHNT
Ezekiel 10 in the DNT
Ezekiel 10 in the ELBE
Ezekiel 10 in the EMTV
Ezekiel 10 in the ESV
Ezekiel 10 in the FBV
Ezekiel 10 in the FEB
Ezekiel 10 in the GGMNT
Ezekiel 10 in the GNT
Ezekiel 10 in the HARY
Ezekiel 10 in the HNT
Ezekiel 10 in the IRVA
Ezekiel 10 in the IRVB
Ezekiel 10 in the IRVG
Ezekiel 10 in the IRVH
Ezekiel 10 in the IRVK
Ezekiel 10 in the IRVM
Ezekiel 10 in the IRVM2
Ezekiel 10 in the IRVO
Ezekiel 10 in the IRVP
Ezekiel 10 in the IRVT
Ezekiel 10 in the IRVT2
Ezekiel 10 in the IRVU
Ezekiel 10 in the ISVN
Ezekiel 10 in the JSNT
Ezekiel 10 in the KAPI
Ezekiel 10 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 10 in the KBV
Ezekiel 10 in the KJV
Ezekiel 10 in the KNFD
Ezekiel 10 in the LBA
Ezekiel 10 in the LBLA
Ezekiel 10 in the LNT
Ezekiel 10 in the LSV
Ezekiel 10 in the MAAL
Ezekiel 10 in the MBV
Ezekiel 10 in the MBV2
Ezekiel 10 in the MHNT
Ezekiel 10 in the MKNFD
Ezekiel 10 in the MNG
Ezekiel 10 in the MNT
Ezekiel 10 in the MNT2
Ezekiel 10 in the MRS1T
Ezekiel 10 in the NAA
Ezekiel 10 in the NASB
Ezekiel 10 in the NBLA
Ezekiel 10 in the NBS
Ezekiel 10 in the NBVTP
Ezekiel 10 in the NET2
Ezekiel 10 in the NIV11
Ezekiel 10 in the NNT
Ezekiel 10 in the NNT2
Ezekiel 10 in the NNT3
Ezekiel 10 in the PDDPT
Ezekiel 10 in the PFNT
Ezekiel 10 in the RMNT
Ezekiel 10 in the SBIAS
Ezekiel 10 in the SBIBS
Ezekiel 10 in the SBIBS2
Ezekiel 10 in the SBICS
Ezekiel 10 in the SBIDS
Ezekiel 10 in the SBIGS
Ezekiel 10 in the SBIHS
Ezekiel 10 in the SBIIS
Ezekiel 10 in the SBIIS2
Ezekiel 10 in the SBIIS3
Ezekiel 10 in the SBIKS
Ezekiel 10 in the SBIKS2
Ezekiel 10 in the SBIMS
Ezekiel 10 in the SBIOS
Ezekiel 10 in the SBIPS
Ezekiel 10 in the SBISS
Ezekiel 10 in the SBITS
Ezekiel 10 in the SBITS2
Ezekiel 10 in the SBITS3
Ezekiel 10 in the SBITS4
Ezekiel 10 in the SBIUS
Ezekiel 10 in the SBIVS
Ezekiel 10 in the SBT
Ezekiel 10 in the SBT1E
Ezekiel 10 in the SCHL
Ezekiel 10 in the SNT
Ezekiel 10 in the SUSU
Ezekiel 10 in the SUSU2
Ezekiel 10 in the SYNO
Ezekiel 10 in the TBIAOTANT
Ezekiel 10 in the TBT1E
Ezekiel 10 in the TBT1E2
Ezekiel 10 in the TFTIP
Ezekiel 10 in the TFTU
Ezekiel 10 in the TGNTATF3T
Ezekiel 10 in the THAI
Ezekiel 10 in the TNFD
Ezekiel 10 in the TNT
Ezekiel 10 in the TNTIK
Ezekiel 10 in the TNTIL
Ezekiel 10 in the TNTIN
Ezekiel 10 in the TNTIP
Ezekiel 10 in the TNTIZ
Ezekiel 10 in the TOMA
Ezekiel 10 in the TTENT
Ezekiel 10 in the UBG
Ezekiel 10 in the UGV
Ezekiel 10 in the UGV2
Ezekiel 10 in the UGV3
Ezekiel 10 in the VBL
Ezekiel 10 in the VDCC
Ezekiel 10 in the YALU
Ezekiel 10 in the YAPE
Ezekiel 10 in the YBVTP
Ezekiel 10 in the ZBP