Ezekiel 11 (BOGWICC)
1 Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. 2 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. 3 Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. 4 Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ” 5 Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ 6 Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo. 7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. 8 Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. 9 Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. 10 Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11 Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. 12 Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ” 13 Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?” 14 Yehova anayankhula nane kuti, 15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ” 16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’ 17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli. 18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.” 22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.
In Other Versions
Ezekiel 11 in the ANGEFD
Ezekiel 11 in the ANTPNG2D
Ezekiel 11 in the AS21
Ezekiel 11 in the BAGH
Ezekiel 11 in the BBPNG
Ezekiel 11 in the BBT1E
Ezekiel 11 in the BDS
Ezekiel 11 in the BEV
Ezekiel 11 in the BHAD
Ezekiel 11 in the BIB
Ezekiel 11 in the BLPT
Ezekiel 11 in the BNT
Ezekiel 11 in the BNTABOOT
Ezekiel 11 in the BNTLV
Ezekiel 11 in the BOATCB
Ezekiel 11 in the BOATCB2
Ezekiel 11 in the BOBCV
Ezekiel 11 in the BOCNT
Ezekiel 11 in the BOECS
Ezekiel 11 in the BOHCB
Ezekiel 11 in the BOHCV
Ezekiel 11 in the BOHLNT
Ezekiel 11 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 11 in the BOICB
Ezekiel 11 in the BOILNTAP
Ezekiel 11 in the BOITCV
Ezekiel 11 in the BOKCV
Ezekiel 11 in the BOKCV2
Ezekiel 11 in the BOKHWOG
Ezekiel 11 in the BOKSSV
Ezekiel 11 in the BOLCB
Ezekiel 11 in the BOLCB2
Ezekiel 11 in the BOMCV
Ezekiel 11 in the BONAV
Ezekiel 11 in the BONCB
Ezekiel 11 in the BONLT
Ezekiel 11 in the BONUT2
Ezekiel 11 in the BOPLNT
Ezekiel 11 in the BOSCB
Ezekiel 11 in the BOSNC
Ezekiel 11 in the BOTLNT
Ezekiel 11 in the BOVCB
Ezekiel 11 in the BOYCB
Ezekiel 11 in the BPBB
Ezekiel 11 in the BPH
Ezekiel 11 in the BSB
Ezekiel 11 in the CCB
Ezekiel 11 in the CUV
Ezekiel 11 in the CUVS
Ezekiel 11 in the DBT
Ezekiel 11 in the DGDNT
Ezekiel 11 in the DHNT
Ezekiel 11 in the DNT
Ezekiel 11 in the ELBE
Ezekiel 11 in the EMTV
Ezekiel 11 in the ESV
Ezekiel 11 in the FBV
Ezekiel 11 in the FEB
Ezekiel 11 in the GGMNT
Ezekiel 11 in the GNT
Ezekiel 11 in the HARY
Ezekiel 11 in the HNT
Ezekiel 11 in the IRVA
Ezekiel 11 in the IRVB
Ezekiel 11 in the IRVG
Ezekiel 11 in the IRVH
Ezekiel 11 in the IRVK
Ezekiel 11 in the IRVM
Ezekiel 11 in the IRVM2
Ezekiel 11 in the IRVO
Ezekiel 11 in the IRVP
Ezekiel 11 in the IRVT
Ezekiel 11 in the IRVT2
Ezekiel 11 in the IRVU
Ezekiel 11 in the ISVN
Ezekiel 11 in the JSNT
Ezekiel 11 in the KAPI
Ezekiel 11 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 11 in the KBV
Ezekiel 11 in the KJV
Ezekiel 11 in the KNFD
Ezekiel 11 in the LBA
Ezekiel 11 in the LBLA
Ezekiel 11 in the LNT
Ezekiel 11 in the LSV
Ezekiel 11 in the MAAL
Ezekiel 11 in the MBV
Ezekiel 11 in the MBV2
Ezekiel 11 in the MHNT
Ezekiel 11 in the MKNFD
Ezekiel 11 in the MNG
Ezekiel 11 in the MNT
Ezekiel 11 in the MNT2
Ezekiel 11 in the MRS1T
Ezekiel 11 in the NAA
Ezekiel 11 in the NASB
Ezekiel 11 in the NBLA
Ezekiel 11 in the NBS
Ezekiel 11 in the NBVTP
Ezekiel 11 in the NET2
Ezekiel 11 in the NIV11
Ezekiel 11 in the NNT
Ezekiel 11 in the NNT2
Ezekiel 11 in the NNT3
Ezekiel 11 in the PDDPT
Ezekiel 11 in the PFNT
Ezekiel 11 in the RMNT
Ezekiel 11 in the SBIAS
Ezekiel 11 in the SBIBS
Ezekiel 11 in the SBIBS2
Ezekiel 11 in the SBICS
Ezekiel 11 in the SBIDS
Ezekiel 11 in the SBIGS
Ezekiel 11 in the SBIHS
Ezekiel 11 in the SBIIS
Ezekiel 11 in the SBIIS2
Ezekiel 11 in the SBIIS3
Ezekiel 11 in the SBIKS
Ezekiel 11 in the SBIKS2
Ezekiel 11 in the SBIMS
Ezekiel 11 in the SBIOS
Ezekiel 11 in the SBIPS
Ezekiel 11 in the SBISS
Ezekiel 11 in the SBITS
Ezekiel 11 in the SBITS2
Ezekiel 11 in the SBITS3
Ezekiel 11 in the SBITS4
Ezekiel 11 in the SBIUS
Ezekiel 11 in the SBIVS
Ezekiel 11 in the SBT
Ezekiel 11 in the SBT1E
Ezekiel 11 in the SCHL
Ezekiel 11 in the SNT
Ezekiel 11 in the SUSU
Ezekiel 11 in the SUSU2
Ezekiel 11 in the SYNO
Ezekiel 11 in the TBIAOTANT
Ezekiel 11 in the TBT1E
Ezekiel 11 in the TBT1E2
Ezekiel 11 in the TFTIP
Ezekiel 11 in the TFTU
Ezekiel 11 in the TGNTATF3T
Ezekiel 11 in the THAI
Ezekiel 11 in the TNFD
Ezekiel 11 in the TNT
Ezekiel 11 in the TNTIK
Ezekiel 11 in the TNTIL
Ezekiel 11 in the TNTIN
Ezekiel 11 in the TNTIP
Ezekiel 11 in the TNTIZ
Ezekiel 11 in the TOMA
Ezekiel 11 in the TTENT
Ezekiel 11 in the UBG
Ezekiel 11 in the UGV
Ezekiel 11 in the UGV2
Ezekiel 11 in the UGV3
Ezekiel 11 in the VBL
Ezekiel 11 in the VDCC
Ezekiel 11 in the YALU
Ezekiel 11 in the YAPE
Ezekiel 11 in the YBVTP
Ezekiel 11 in the ZBP