Ezekiel 34 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? 3 Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. 4 Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. 5 Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. 6 Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna. 7 “ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 8 Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. 9 Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 10 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso. 11 “ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. 12 Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. 13 Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. 14 Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. 15 Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16 Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo. 17 “ ‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna. 18 Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu? 19 Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu? 20 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda. 21 Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali, 22 tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. 23 Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo. 24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula. 25 “ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo. 26 Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso. 27 Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo. 28 Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze. 29 Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso. 30 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 31 Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”

In Other Versions

Ezekiel 34 in the ANGEFD

Ezekiel 34 in the ANTPNG2D

Ezekiel 34 in the AS21

Ezekiel 34 in the BAGH

Ezekiel 34 in the BBPNG

Ezekiel 34 in the BBT1E

Ezekiel 34 in the BDS

Ezekiel 34 in the BEV

Ezekiel 34 in the BHAD

Ezekiel 34 in the BIB

Ezekiel 34 in the BLPT

Ezekiel 34 in the BNT

Ezekiel 34 in the BNTABOOT

Ezekiel 34 in the BNTLV

Ezekiel 34 in the BOATCB

Ezekiel 34 in the BOATCB2

Ezekiel 34 in the BOBCV

Ezekiel 34 in the BOCNT

Ezekiel 34 in the BOECS

Ezekiel 34 in the BOHCB

Ezekiel 34 in the BOHCV

Ezekiel 34 in the BOHLNT

Ezekiel 34 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 34 in the BOICB

Ezekiel 34 in the BOILNTAP

Ezekiel 34 in the BOITCV

Ezekiel 34 in the BOKCV

Ezekiel 34 in the BOKCV2

Ezekiel 34 in the BOKHWOG

Ezekiel 34 in the BOKSSV

Ezekiel 34 in the BOLCB

Ezekiel 34 in the BOLCB2

Ezekiel 34 in the BOMCV

Ezekiel 34 in the BONAV

Ezekiel 34 in the BONCB

Ezekiel 34 in the BONLT

Ezekiel 34 in the BONUT2

Ezekiel 34 in the BOPLNT

Ezekiel 34 in the BOSCB

Ezekiel 34 in the BOSNC

Ezekiel 34 in the BOTLNT

Ezekiel 34 in the BOVCB

Ezekiel 34 in the BOYCB

Ezekiel 34 in the BPBB

Ezekiel 34 in the BPH

Ezekiel 34 in the BSB

Ezekiel 34 in the CCB

Ezekiel 34 in the CUV

Ezekiel 34 in the CUVS

Ezekiel 34 in the DBT

Ezekiel 34 in the DGDNT

Ezekiel 34 in the DHNT

Ezekiel 34 in the DNT

Ezekiel 34 in the ELBE

Ezekiel 34 in the EMTV

Ezekiel 34 in the ESV

Ezekiel 34 in the FBV

Ezekiel 34 in the FEB

Ezekiel 34 in the GGMNT

Ezekiel 34 in the GNT

Ezekiel 34 in the HARY

Ezekiel 34 in the HNT

Ezekiel 34 in the IRVA

Ezekiel 34 in the IRVB

Ezekiel 34 in the IRVG

Ezekiel 34 in the IRVH

Ezekiel 34 in the IRVK

Ezekiel 34 in the IRVM

Ezekiel 34 in the IRVM2

Ezekiel 34 in the IRVO

Ezekiel 34 in the IRVP

Ezekiel 34 in the IRVT

Ezekiel 34 in the IRVT2

Ezekiel 34 in the IRVU

Ezekiel 34 in the ISVN

Ezekiel 34 in the JSNT

Ezekiel 34 in the KAPI

Ezekiel 34 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 34 in the KBV

Ezekiel 34 in the KJV

Ezekiel 34 in the KNFD

Ezekiel 34 in the LBA

Ezekiel 34 in the LBLA

Ezekiel 34 in the LNT

Ezekiel 34 in the LSV

Ezekiel 34 in the MAAL

Ezekiel 34 in the MBV

Ezekiel 34 in the MBV2

Ezekiel 34 in the MHNT

Ezekiel 34 in the MKNFD

Ezekiel 34 in the MNG

Ezekiel 34 in the MNT

Ezekiel 34 in the MNT2

Ezekiel 34 in the MRS1T

Ezekiel 34 in the NAA

Ezekiel 34 in the NASB

Ezekiel 34 in the NBLA

Ezekiel 34 in the NBS

Ezekiel 34 in the NBVTP

Ezekiel 34 in the NET2

Ezekiel 34 in the NIV11

Ezekiel 34 in the NNT

Ezekiel 34 in the NNT2

Ezekiel 34 in the NNT3

Ezekiel 34 in the PDDPT

Ezekiel 34 in the PFNT

Ezekiel 34 in the RMNT

Ezekiel 34 in the SBIAS

Ezekiel 34 in the SBIBS

Ezekiel 34 in the SBIBS2

Ezekiel 34 in the SBICS

Ezekiel 34 in the SBIDS

Ezekiel 34 in the SBIGS

Ezekiel 34 in the SBIHS

Ezekiel 34 in the SBIIS

Ezekiel 34 in the SBIIS2

Ezekiel 34 in the SBIIS3

Ezekiel 34 in the SBIKS

Ezekiel 34 in the SBIKS2

Ezekiel 34 in the SBIMS

Ezekiel 34 in the SBIOS

Ezekiel 34 in the SBIPS

Ezekiel 34 in the SBISS

Ezekiel 34 in the SBITS

Ezekiel 34 in the SBITS2

Ezekiel 34 in the SBITS3

Ezekiel 34 in the SBITS4

Ezekiel 34 in the SBIUS

Ezekiel 34 in the SBIVS

Ezekiel 34 in the SBT

Ezekiel 34 in the SBT1E

Ezekiel 34 in the SCHL

Ezekiel 34 in the SNT

Ezekiel 34 in the SUSU

Ezekiel 34 in the SUSU2

Ezekiel 34 in the SYNO

Ezekiel 34 in the TBIAOTANT

Ezekiel 34 in the TBT1E

Ezekiel 34 in the TBT1E2

Ezekiel 34 in the TFTIP

Ezekiel 34 in the TFTU

Ezekiel 34 in the TGNTATF3T

Ezekiel 34 in the THAI

Ezekiel 34 in the TNFD

Ezekiel 34 in the TNT

Ezekiel 34 in the TNTIK

Ezekiel 34 in the TNTIL

Ezekiel 34 in the TNTIN

Ezekiel 34 in the TNTIP

Ezekiel 34 in the TNTIZ

Ezekiel 34 in the TOMA

Ezekiel 34 in the TTENT

Ezekiel 34 in the UBG

Ezekiel 34 in the UGV

Ezekiel 34 in the UGV2

Ezekiel 34 in the UGV3

Ezekiel 34 in the VBL

Ezekiel 34 in the VDCC

Ezekiel 34 in the YALU

Ezekiel 34 in the YAPE

Ezekiel 34 in the YBVTP

Ezekiel 34 in the ZBP