Ezekiel 37 (BOGWICC)

1 Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. 2 Yehova anandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo anali ochuluka kwambiri mʼchigwa monsemo ndipo anali owuma kwambiri. 3 Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?”Ndinayankha kuti, “Inu Ambuye Yehova, Inuyo nokha ndiye mukudziwa.” 4 Pamenepo anandiwuza kuti, “Lengeza kwa mafupa amenewa ndi kuwawuza kuti amve mawu a Ine Yehova! 5 Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. 6 Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.” 7 Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake. 8 Ine ndinayangʼana, ndipo mitsempha ndi mnofu zinabwera pa mafupawo ndipo khungu linaphimba pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo. 9 Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’ 10 Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.” 11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’ 12 Nʼchifukwa chake nenera ndi kuwawuza kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo ndi kukubwezerani ku dziko la Israeli. 13 Ndipo inu, anthu anga, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzafukula manda anu ndikukutulutsanimo. 14 Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’ ” 15 Yehova anandiyankhula kuti: 16 “Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’ 17 Ulumikize ndodo ziwirizi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako. 18 “Anthu a mtundu wako akadzakufunsa tanthauzo la zimenezi 19 iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’ 20 Ndodo ziwiri zimene udzalembepozo zikadzakhala mʼmanja mwako pamaso pa anthu onse, 21 udzawawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzawachotsa Aisraeli pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapita ku ukapolo. Ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku dziko lawolawo. 22 Ndidzawasandutsa mtundu umodzi mʼdzikomo, pa mapiri a Israeli. Padzakhala mfumu imodzi yowalamulira, ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawikana maufumu awiri. 23 Sadzadziyipitsanso ndi mafano awo, kapena ndi zinthu zawo zonyansa, kapenanso ndi ntchito zawo zoyipa zilizonse. Ndidzawapulumutsa ku machimo awo onse ndi kuwayeretsa. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 24 “ ‘Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo, motero onsewa adzakhala ndi mʼbusa mmodzi. Iwo adzatsatira malamulo anga ndipo adzasamalira kusunga malangizo anga. 25 Iwo adzakhala mʼdziko limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhalamo. Iwo ndi ana awo pamodzi ndi zidzukulu zawo adzakhala kumeneko ndipo Davide adzakhala mfumu yawo kwa muyaya. 26 Ndidzachita nawo pangano lamtendere; lidzakhala pangano lamuyaya. Ndidzawakhazikitsa ndi kuwachulukitsa, ndipo ndidzayika malo anga opatulika pakati pawo kwamuyaya. 27 Nyumba yanga yokhalamo idzakhala pakati pawo; Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga. 28 Pamenepo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti Ine Yehova ndiye amene ndimasandutsa Israeli kukhala woyera, pamene malo anga opatulika adzakhala pakati pawo kwamuyaya!’ ”

In Other Versions

Ezekiel 37 in the ANGEFD

Ezekiel 37 in the ANTPNG2D

Ezekiel 37 in the AS21

Ezekiel 37 in the BAGH

Ezekiel 37 in the BBPNG

Ezekiel 37 in the BBT1E

Ezekiel 37 in the BDS

Ezekiel 37 in the BEV

Ezekiel 37 in the BHAD

Ezekiel 37 in the BIB

Ezekiel 37 in the BLPT

Ezekiel 37 in the BNT

Ezekiel 37 in the BNTABOOT

Ezekiel 37 in the BNTLV

Ezekiel 37 in the BOATCB

Ezekiel 37 in the BOATCB2

Ezekiel 37 in the BOBCV

Ezekiel 37 in the BOCNT

Ezekiel 37 in the BOECS

Ezekiel 37 in the BOHCB

Ezekiel 37 in the BOHCV

Ezekiel 37 in the BOHLNT

Ezekiel 37 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 37 in the BOICB

Ezekiel 37 in the BOILNTAP

Ezekiel 37 in the BOITCV

Ezekiel 37 in the BOKCV

Ezekiel 37 in the BOKCV2

Ezekiel 37 in the BOKHWOG

Ezekiel 37 in the BOKSSV

Ezekiel 37 in the BOLCB

Ezekiel 37 in the BOLCB2

Ezekiel 37 in the BOMCV

Ezekiel 37 in the BONAV

Ezekiel 37 in the BONCB

Ezekiel 37 in the BONLT

Ezekiel 37 in the BONUT2

Ezekiel 37 in the BOPLNT

Ezekiel 37 in the BOSCB

Ezekiel 37 in the BOSNC

Ezekiel 37 in the BOTLNT

Ezekiel 37 in the BOVCB

Ezekiel 37 in the BOYCB

Ezekiel 37 in the BPBB

Ezekiel 37 in the BPH

Ezekiel 37 in the BSB

Ezekiel 37 in the CCB

Ezekiel 37 in the CUV

Ezekiel 37 in the CUVS

Ezekiel 37 in the DBT

Ezekiel 37 in the DGDNT

Ezekiel 37 in the DHNT

Ezekiel 37 in the DNT

Ezekiel 37 in the ELBE

Ezekiel 37 in the EMTV

Ezekiel 37 in the ESV

Ezekiel 37 in the FBV

Ezekiel 37 in the FEB

Ezekiel 37 in the GGMNT

Ezekiel 37 in the GNT

Ezekiel 37 in the HARY

Ezekiel 37 in the HNT

Ezekiel 37 in the IRVA

Ezekiel 37 in the IRVB

Ezekiel 37 in the IRVG

Ezekiel 37 in the IRVH

Ezekiel 37 in the IRVK

Ezekiel 37 in the IRVM

Ezekiel 37 in the IRVM2

Ezekiel 37 in the IRVO

Ezekiel 37 in the IRVP

Ezekiel 37 in the IRVT

Ezekiel 37 in the IRVT2

Ezekiel 37 in the IRVU

Ezekiel 37 in the ISVN

Ezekiel 37 in the JSNT

Ezekiel 37 in the KAPI

Ezekiel 37 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 37 in the KBV

Ezekiel 37 in the KJV

Ezekiel 37 in the KNFD

Ezekiel 37 in the LBA

Ezekiel 37 in the LBLA

Ezekiel 37 in the LNT

Ezekiel 37 in the LSV

Ezekiel 37 in the MAAL

Ezekiel 37 in the MBV

Ezekiel 37 in the MBV2

Ezekiel 37 in the MHNT

Ezekiel 37 in the MKNFD

Ezekiel 37 in the MNG

Ezekiel 37 in the MNT

Ezekiel 37 in the MNT2

Ezekiel 37 in the MRS1T

Ezekiel 37 in the NAA

Ezekiel 37 in the NASB

Ezekiel 37 in the NBLA

Ezekiel 37 in the NBS

Ezekiel 37 in the NBVTP

Ezekiel 37 in the NET2

Ezekiel 37 in the NIV11

Ezekiel 37 in the NNT

Ezekiel 37 in the NNT2

Ezekiel 37 in the NNT3

Ezekiel 37 in the PDDPT

Ezekiel 37 in the PFNT

Ezekiel 37 in the RMNT

Ezekiel 37 in the SBIAS

Ezekiel 37 in the SBIBS

Ezekiel 37 in the SBIBS2

Ezekiel 37 in the SBICS

Ezekiel 37 in the SBIDS

Ezekiel 37 in the SBIGS

Ezekiel 37 in the SBIHS

Ezekiel 37 in the SBIIS

Ezekiel 37 in the SBIIS2

Ezekiel 37 in the SBIIS3

Ezekiel 37 in the SBIKS

Ezekiel 37 in the SBIKS2

Ezekiel 37 in the SBIMS

Ezekiel 37 in the SBIOS

Ezekiel 37 in the SBIPS

Ezekiel 37 in the SBISS

Ezekiel 37 in the SBITS

Ezekiel 37 in the SBITS2

Ezekiel 37 in the SBITS3

Ezekiel 37 in the SBITS4

Ezekiel 37 in the SBIUS

Ezekiel 37 in the SBIVS

Ezekiel 37 in the SBT

Ezekiel 37 in the SBT1E

Ezekiel 37 in the SCHL

Ezekiel 37 in the SNT

Ezekiel 37 in the SUSU

Ezekiel 37 in the SUSU2

Ezekiel 37 in the SYNO

Ezekiel 37 in the TBIAOTANT

Ezekiel 37 in the TBT1E

Ezekiel 37 in the TBT1E2

Ezekiel 37 in the TFTIP

Ezekiel 37 in the TFTU

Ezekiel 37 in the TGNTATF3T

Ezekiel 37 in the THAI

Ezekiel 37 in the TNFD

Ezekiel 37 in the TNT

Ezekiel 37 in the TNTIK

Ezekiel 37 in the TNTIL

Ezekiel 37 in the TNTIN

Ezekiel 37 in the TNTIP

Ezekiel 37 in the TNTIZ

Ezekiel 37 in the TOMA

Ezekiel 37 in the TTENT

Ezekiel 37 in the UBG

Ezekiel 37 in the UGV

Ezekiel 37 in the UGV2

Ezekiel 37 in the UGV3

Ezekiel 37 in the VBL

Ezekiel 37 in the VDCC

Ezekiel 37 in the YALU

Ezekiel 37 in the YAPE

Ezekiel 37 in the YBVTP

Ezekiel 37 in the ZBP