Ezekiel 39 (BOGWICC)

1 “Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala. 2 Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli. 3 Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja. 4 Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo. 5 Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 6 Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ 7 “Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli. 8 Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija. 9 “Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 10 Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova. 11 “Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. 12 “Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko. 13 Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 14 “Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo. 15 Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. 16 (Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko. 17 “Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi. 18 Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani. 19 Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera. 20 Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova. 21 “Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. 22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 23 Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. 24 Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga. 25 “Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. 26 Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. 27 Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. 28 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. 29 Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

In Other Versions

Ezekiel 39 in the ANGEFD

Ezekiel 39 in the ANTPNG2D

Ezekiel 39 in the AS21

Ezekiel 39 in the BAGH

Ezekiel 39 in the BBPNG

Ezekiel 39 in the BBT1E

Ezekiel 39 in the BDS

Ezekiel 39 in the BEV

Ezekiel 39 in the BHAD

Ezekiel 39 in the BIB

Ezekiel 39 in the BLPT

Ezekiel 39 in the BNT

Ezekiel 39 in the BNTABOOT

Ezekiel 39 in the BNTLV

Ezekiel 39 in the BOATCB

Ezekiel 39 in the BOATCB2

Ezekiel 39 in the BOBCV

Ezekiel 39 in the BOCNT

Ezekiel 39 in the BOECS

Ezekiel 39 in the BOHCB

Ezekiel 39 in the BOHCV

Ezekiel 39 in the BOHLNT

Ezekiel 39 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 39 in the BOICB

Ezekiel 39 in the BOILNTAP

Ezekiel 39 in the BOITCV

Ezekiel 39 in the BOKCV

Ezekiel 39 in the BOKCV2

Ezekiel 39 in the BOKHWOG

Ezekiel 39 in the BOKSSV

Ezekiel 39 in the BOLCB

Ezekiel 39 in the BOLCB2

Ezekiel 39 in the BOMCV

Ezekiel 39 in the BONAV

Ezekiel 39 in the BONCB

Ezekiel 39 in the BONLT

Ezekiel 39 in the BONUT2

Ezekiel 39 in the BOPLNT

Ezekiel 39 in the BOSCB

Ezekiel 39 in the BOSNC

Ezekiel 39 in the BOTLNT

Ezekiel 39 in the BOVCB

Ezekiel 39 in the BOYCB

Ezekiel 39 in the BPBB

Ezekiel 39 in the BPH

Ezekiel 39 in the BSB

Ezekiel 39 in the CCB

Ezekiel 39 in the CUV

Ezekiel 39 in the CUVS

Ezekiel 39 in the DBT

Ezekiel 39 in the DGDNT

Ezekiel 39 in the DHNT

Ezekiel 39 in the DNT

Ezekiel 39 in the ELBE

Ezekiel 39 in the EMTV

Ezekiel 39 in the ESV

Ezekiel 39 in the FBV

Ezekiel 39 in the FEB

Ezekiel 39 in the GGMNT

Ezekiel 39 in the GNT

Ezekiel 39 in the HARY

Ezekiel 39 in the HNT

Ezekiel 39 in the IRVA

Ezekiel 39 in the IRVB

Ezekiel 39 in the IRVG

Ezekiel 39 in the IRVH

Ezekiel 39 in the IRVK

Ezekiel 39 in the IRVM

Ezekiel 39 in the IRVM2

Ezekiel 39 in the IRVO

Ezekiel 39 in the IRVP

Ezekiel 39 in the IRVT

Ezekiel 39 in the IRVT2

Ezekiel 39 in the IRVU

Ezekiel 39 in the ISVN

Ezekiel 39 in the JSNT

Ezekiel 39 in the KAPI

Ezekiel 39 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 39 in the KBV

Ezekiel 39 in the KJV

Ezekiel 39 in the KNFD

Ezekiel 39 in the LBA

Ezekiel 39 in the LBLA

Ezekiel 39 in the LNT

Ezekiel 39 in the LSV

Ezekiel 39 in the MAAL

Ezekiel 39 in the MBV

Ezekiel 39 in the MBV2

Ezekiel 39 in the MHNT

Ezekiel 39 in the MKNFD

Ezekiel 39 in the MNG

Ezekiel 39 in the MNT

Ezekiel 39 in the MNT2

Ezekiel 39 in the MRS1T

Ezekiel 39 in the NAA

Ezekiel 39 in the NASB

Ezekiel 39 in the NBLA

Ezekiel 39 in the NBS

Ezekiel 39 in the NBVTP

Ezekiel 39 in the NET2

Ezekiel 39 in the NIV11

Ezekiel 39 in the NNT

Ezekiel 39 in the NNT2

Ezekiel 39 in the NNT3

Ezekiel 39 in the PDDPT

Ezekiel 39 in the PFNT

Ezekiel 39 in the RMNT

Ezekiel 39 in the SBIAS

Ezekiel 39 in the SBIBS

Ezekiel 39 in the SBIBS2

Ezekiel 39 in the SBICS

Ezekiel 39 in the SBIDS

Ezekiel 39 in the SBIGS

Ezekiel 39 in the SBIHS

Ezekiel 39 in the SBIIS

Ezekiel 39 in the SBIIS2

Ezekiel 39 in the SBIIS3

Ezekiel 39 in the SBIKS

Ezekiel 39 in the SBIKS2

Ezekiel 39 in the SBIMS

Ezekiel 39 in the SBIOS

Ezekiel 39 in the SBIPS

Ezekiel 39 in the SBISS

Ezekiel 39 in the SBITS

Ezekiel 39 in the SBITS2

Ezekiel 39 in the SBITS3

Ezekiel 39 in the SBITS4

Ezekiel 39 in the SBIUS

Ezekiel 39 in the SBIVS

Ezekiel 39 in the SBT

Ezekiel 39 in the SBT1E

Ezekiel 39 in the SCHL

Ezekiel 39 in the SNT

Ezekiel 39 in the SUSU

Ezekiel 39 in the SUSU2

Ezekiel 39 in the SYNO

Ezekiel 39 in the TBIAOTANT

Ezekiel 39 in the TBT1E

Ezekiel 39 in the TBT1E2

Ezekiel 39 in the TFTIP

Ezekiel 39 in the TFTU

Ezekiel 39 in the TGNTATF3T

Ezekiel 39 in the THAI

Ezekiel 39 in the TNFD

Ezekiel 39 in the TNT

Ezekiel 39 in the TNTIK

Ezekiel 39 in the TNTIL

Ezekiel 39 in the TNTIN

Ezekiel 39 in the TNTIP

Ezekiel 39 in the TNTIZ

Ezekiel 39 in the TOMA

Ezekiel 39 in the TTENT

Ezekiel 39 in the UBG

Ezekiel 39 in the UGV

Ezekiel 39 in the UGV2

Ezekiel 39 in the UGV3

Ezekiel 39 in the VBL

Ezekiel 39 in the VDCC

Ezekiel 39 in the YALU

Ezekiel 39 in the YAPE

Ezekiel 39 in the YBVTP

Ezekiel 39 in the ZBP