Ezekiel 45 (BOGWICC)

1 “ ‘Mukamadzagawa dziko kuti fuko lililonse lilandire cholowa chake, mudzapatuleko chigawo chimodzi kuti chikhale cha Yehova. Mulitali mwake mudzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita khumi. Malo onsewo adzakhale opatulika. 2 Mʼkati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25. 3 Mʼchigawo chopatulikacho muyeze malo a makilomita 12 ndi theka mulitali mwake, makilomita asanu mulifupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika kwambiri. 4 Malo opatulika amenewa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Yehova kuti amutumikire. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zawo ndi malo omangapo Nyumba ya Mulungu. 5 Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi malo a makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake ndi makilomita asanu mulifupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhale midzi yawo. 6 “ ‘Moyandikana ndi malo opatulika, padzakhale malo a makilomita awiri ndi theka mulifupi mwake ndi makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake; kuti akhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhala a Aisraeli onse. 7 “ ‘Mfumu idzakhale ndi malo okhudzana ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda. Malowo ayandikane ndi zigawozo chakummawa ndi chakumadzulo. Malowo atalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israeli kuyambira ku malire akummawa mpaka ku malire akumadzulo. 8 Malowa adzakhala chigawo cha mfumu mu Israeli. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzidzalola Aisraeli kuti akhale ndi zigawo zawozawo. 9 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 10 Miyeso yanu yoyezera zinthu monga efa ndi bati zizikhala zokhulupirika. 11 Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iwiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo. 12 Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi awiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli 60. 13 “ ‘Zopereka zomwe mudzidzapereka ndi izi: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi ndiponso gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa barele wa homeri. 14 Gawo loyenera la mafuta, loyezedwa ndi bati, ndiponso chigawo mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi afanana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi. 15 Muperekenso nkhosa imodzi pa gulu lankhosa 200 za pa msipu wabwino wa mu Israeli. Izi zidzagwiritsidwa ntchito monga nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano ndi nsembe zopepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16 Anthu onse a mʼdzikomo azidzapereka zimenezi kwa mfumu ya Israeli. 17 Udzakhala udindo wa mfumu kupereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, ndi nsembe za zakumwa pa nthawi ya zikondwerero, chikondwerero cha mwezi watsopano ndi cha masabata, nthawi yonse ya zikondwerero zoyikika za Aisraeli. Mfumuyo idzapereka nsembe zopepesera machimo, nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe zopepesera machimo a Aisraeli. 18 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba muzitenga mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika. 19 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo ndipo awapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinayi za pamwamba pa guwa lansembe ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo la mʼkati. 20 Muzichita chimodzimodzi pa tsiku la chisanu ndi chiwiri la mwezi, kuchitira aliyense amene wachimwa mosafuna kapena mosadziwa. Motero Nyumba ya Mulungu idzakhala yoyera. 21 “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi awiri. Pa masiku amenewo muzidzadya buledi wopanda yisiti. 22 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ngʼombe yayimuna monga nsembe yopepesera machimo ake ndi machimo a anthu onse a mʼdziko. 23 Pa masiku asanu ndi awiri a chikondwererocho, mfumu ipereke kwa Yehova nsembe zopsereza izi: ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, zonsezi zopanda chilema. Pa masikuwa mfumu iziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo. 24 Pamodzi ndi ngʼombe iliyonse yayimuna ndi nkhosa iliyonse yayimuna, mfumu ipereke chopereka cha chakudya chokwanira efa imodzi ndiponso mafuta okwanira hini imodzi pa efa iliyonse. 25 “ ‘Pa nthawi ya chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri, chimene chimayamba pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mfumuyo iziperekanso nsembe za mtundu womwewo: nsembe zopepesera machimo, nsembe zopsereza, nsembe za chakudya ndi za mafuta.’ ”

In Other Versions

Ezekiel 45 in the ANGEFD

Ezekiel 45 in the ANTPNG2D

Ezekiel 45 in the AS21

Ezekiel 45 in the BAGH

Ezekiel 45 in the BBPNG

Ezekiel 45 in the BBT1E

Ezekiel 45 in the BDS

Ezekiel 45 in the BEV

Ezekiel 45 in the BHAD

Ezekiel 45 in the BIB

Ezekiel 45 in the BLPT

Ezekiel 45 in the BNT

Ezekiel 45 in the BNTABOOT

Ezekiel 45 in the BNTLV

Ezekiel 45 in the BOATCB

Ezekiel 45 in the BOATCB2

Ezekiel 45 in the BOBCV

Ezekiel 45 in the BOCNT

Ezekiel 45 in the BOECS

Ezekiel 45 in the BOHCB

Ezekiel 45 in the BOHCV

Ezekiel 45 in the BOHLNT

Ezekiel 45 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 45 in the BOICB

Ezekiel 45 in the BOILNTAP

Ezekiel 45 in the BOITCV

Ezekiel 45 in the BOKCV

Ezekiel 45 in the BOKCV2

Ezekiel 45 in the BOKHWOG

Ezekiel 45 in the BOKSSV

Ezekiel 45 in the BOLCB

Ezekiel 45 in the BOLCB2

Ezekiel 45 in the BOMCV

Ezekiel 45 in the BONAV

Ezekiel 45 in the BONCB

Ezekiel 45 in the BONLT

Ezekiel 45 in the BONUT2

Ezekiel 45 in the BOPLNT

Ezekiel 45 in the BOSCB

Ezekiel 45 in the BOSNC

Ezekiel 45 in the BOTLNT

Ezekiel 45 in the BOVCB

Ezekiel 45 in the BOYCB

Ezekiel 45 in the BPBB

Ezekiel 45 in the BPH

Ezekiel 45 in the BSB

Ezekiel 45 in the CCB

Ezekiel 45 in the CUV

Ezekiel 45 in the CUVS

Ezekiel 45 in the DBT

Ezekiel 45 in the DGDNT

Ezekiel 45 in the DHNT

Ezekiel 45 in the DNT

Ezekiel 45 in the ELBE

Ezekiel 45 in the EMTV

Ezekiel 45 in the ESV

Ezekiel 45 in the FBV

Ezekiel 45 in the FEB

Ezekiel 45 in the GGMNT

Ezekiel 45 in the GNT

Ezekiel 45 in the HARY

Ezekiel 45 in the HNT

Ezekiel 45 in the IRVA

Ezekiel 45 in the IRVB

Ezekiel 45 in the IRVG

Ezekiel 45 in the IRVH

Ezekiel 45 in the IRVK

Ezekiel 45 in the IRVM

Ezekiel 45 in the IRVM2

Ezekiel 45 in the IRVO

Ezekiel 45 in the IRVP

Ezekiel 45 in the IRVT

Ezekiel 45 in the IRVT2

Ezekiel 45 in the IRVU

Ezekiel 45 in the ISVN

Ezekiel 45 in the JSNT

Ezekiel 45 in the KAPI

Ezekiel 45 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 45 in the KBV

Ezekiel 45 in the KJV

Ezekiel 45 in the KNFD

Ezekiel 45 in the LBA

Ezekiel 45 in the LBLA

Ezekiel 45 in the LNT

Ezekiel 45 in the LSV

Ezekiel 45 in the MAAL

Ezekiel 45 in the MBV

Ezekiel 45 in the MBV2

Ezekiel 45 in the MHNT

Ezekiel 45 in the MKNFD

Ezekiel 45 in the MNG

Ezekiel 45 in the MNT

Ezekiel 45 in the MNT2

Ezekiel 45 in the MRS1T

Ezekiel 45 in the NAA

Ezekiel 45 in the NASB

Ezekiel 45 in the NBLA

Ezekiel 45 in the NBS

Ezekiel 45 in the NBVTP

Ezekiel 45 in the NET2

Ezekiel 45 in the NIV11

Ezekiel 45 in the NNT

Ezekiel 45 in the NNT2

Ezekiel 45 in the NNT3

Ezekiel 45 in the PDDPT

Ezekiel 45 in the PFNT

Ezekiel 45 in the RMNT

Ezekiel 45 in the SBIAS

Ezekiel 45 in the SBIBS

Ezekiel 45 in the SBIBS2

Ezekiel 45 in the SBICS

Ezekiel 45 in the SBIDS

Ezekiel 45 in the SBIGS

Ezekiel 45 in the SBIHS

Ezekiel 45 in the SBIIS

Ezekiel 45 in the SBIIS2

Ezekiel 45 in the SBIIS3

Ezekiel 45 in the SBIKS

Ezekiel 45 in the SBIKS2

Ezekiel 45 in the SBIMS

Ezekiel 45 in the SBIOS

Ezekiel 45 in the SBIPS

Ezekiel 45 in the SBISS

Ezekiel 45 in the SBITS

Ezekiel 45 in the SBITS2

Ezekiel 45 in the SBITS3

Ezekiel 45 in the SBITS4

Ezekiel 45 in the SBIUS

Ezekiel 45 in the SBIVS

Ezekiel 45 in the SBT

Ezekiel 45 in the SBT1E

Ezekiel 45 in the SCHL

Ezekiel 45 in the SNT

Ezekiel 45 in the SUSU

Ezekiel 45 in the SUSU2

Ezekiel 45 in the SYNO

Ezekiel 45 in the TBIAOTANT

Ezekiel 45 in the TBT1E

Ezekiel 45 in the TBT1E2

Ezekiel 45 in the TFTIP

Ezekiel 45 in the TFTU

Ezekiel 45 in the TGNTATF3T

Ezekiel 45 in the THAI

Ezekiel 45 in the TNFD

Ezekiel 45 in the TNT

Ezekiel 45 in the TNTIK

Ezekiel 45 in the TNTIL

Ezekiel 45 in the TNTIN

Ezekiel 45 in the TNTIP

Ezekiel 45 in the TNTIZ

Ezekiel 45 in the TOMA

Ezekiel 45 in the TTENT

Ezekiel 45 in the UBG

Ezekiel 45 in the UGV

Ezekiel 45 in the UGV2

Ezekiel 45 in the UGV3

Ezekiel 45 in the VBL

Ezekiel 45 in the VDCC

Ezekiel 45 in the YALU

Ezekiel 45 in the YAPE

Ezekiel 45 in the YBVTP

Ezekiel 45 in the ZBP