Ezekiel 8 (BOGWICC)
1 Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira. 2 Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira. 3 Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu. 4 Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja. 5 Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija. 6 Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.” 7 Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo. 8 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo. 9 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.” 10 Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza. 11 Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka. 12 Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ 13 Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’ ” 14 Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi. 15 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.” 16 Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa. 17 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! 18 Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”
In Other Versions
Ezekiel 8 in the ANGEFD
Ezekiel 8 in the ANTPNG2D
Ezekiel 8 in the AS21
Ezekiel 8 in the BAGH
Ezekiel 8 in the BBPNG
Ezekiel 8 in the BBT1E
Ezekiel 8 in the BDS
Ezekiel 8 in the BEV
Ezekiel 8 in the BHAD
Ezekiel 8 in the BIB
Ezekiel 8 in the BLPT
Ezekiel 8 in the BNT
Ezekiel 8 in the BNTABOOT
Ezekiel 8 in the BNTLV
Ezekiel 8 in the BOATCB
Ezekiel 8 in the BOATCB2
Ezekiel 8 in the BOBCV
Ezekiel 8 in the BOCNT
Ezekiel 8 in the BOECS
Ezekiel 8 in the BOHCB
Ezekiel 8 in the BOHCV
Ezekiel 8 in the BOHLNT
Ezekiel 8 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 8 in the BOICB
Ezekiel 8 in the BOILNTAP
Ezekiel 8 in the BOITCV
Ezekiel 8 in the BOKCV
Ezekiel 8 in the BOKCV2
Ezekiel 8 in the BOKHWOG
Ezekiel 8 in the BOKSSV
Ezekiel 8 in the BOLCB
Ezekiel 8 in the BOLCB2
Ezekiel 8 in the BOMCV
Ezekiel 8 in the BONAV
Ezekiel 8 in the BONCB
Ezekiel 8 in the BONLT
Ezekiel 8 in the BONUT2
Ezekiel 8 in the BOPLNT
Ezekiel 8 in the BOSCB
Ezekiel 8 in the BOSNC
Ezekiel 8 in the BOTLNT
Ezekiel 8 in the BOVCB
Ezekiel 8 in the BOYCB
Ezekiel 8 in the BPBB
Ezekiel 8 in the BPH
Ezekiel 8 in the BSB
Ezekiel 8 in the CCB
Ezekiel 8 in the CUV
Ezekiel 8 in the CUVS
Ezekiel 8 in the DBT
Ezekiel 8 in the DGDNT
Ezekiel 8 in the DHNT
Ezekiel 8 in the DNT
Ezekiel 8 in the ELBE
Ezekiel 8 in the EMTV
Ezekiel 8 in the ESV
Ezekiel 8 in the FBV
Ezekiel 8 in the FEB
Ezekiel 8 in the GGMNT
Ezekiel 8 in the GNT
Ezekiel 8 in the HARY
Ezekiel 8 in the HNT
Ezekiel 8 in the IRVA
Ezekiel 8 in the IRVB
Ezekiel 8 in the IRVG
Ezekiel 8 in the IRVH
Ezekiel 8 in the IRVK
Ezekiel 8 in the IRVM
Ezekiel 8 in the IRVM2
Ezekiel 8 in the IRVO
Ezekiel 8 in the IRVP
Ezekiel 8 in the IRVT
Ezekiel 8 in the IRVT2
Ezekiel 8 in the IRVU
Ezekiel 8 in the ISVN
Ezekiel 8 in the JSNT
Ezekiel 8 in the KAPI
Ezekiel 8 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 8 in the KBV
Ezekiel 8 in the KJV
Ezekiel 8 in the KNFD
Ezekiel 8 in the LBA
Ezekiel 8 in the LBLA
Ezekiel 8 in the LNT
Ezekiel 8 in the LSV
Ezekiel 8 in the MAAL
Ezekiel 8 in the MBV
Ezekiel 8 in the MBV2
Ezekiel 8 in the MHNT
Ezekiel 8 in the MKNFD
Ezekiel 8 in the MNG
Ezekiel 8 in the MNT
Ezekiel 8 in the MNT2
Ezekiel 8 in the MRS1T
Ezekiel 8 in the NAA
Ezekiel 8 in the NASB
Ezekiel 8 in the NBLA
Ezekiel 8 in the NBS
Ezekiel 8 in the NBVTP
Ezekiel 8 in the NET2
Ezekiel 8 in the NIV11
Ezekiel 8 in the NNT
Ezekiel 8 in the NNT2
Ezekiel 8 in the NNT3
Ezekiel 8 in the PDDPT
Ezekiel 8 in the PFNT
Ezekiel 8 in the RMNT
Ezekiel 8 in the SBIAS
Ezekiel 8 in the SBIBS
Ezekiel 8 in the SBIBS2
Ezekiel 8 in the SBICS
Ezekiel 8 in the SBIDS
Ezekiel 8 in the SBIGS
Ezekiel 8 in the SBIHS
Ezekiel 8 in the SBIIS
Ezekiel 8 in the SBIIS2
Ezekiel 8 in the SBIIS3
Ezekiel 8 in the SBIKS
Ezekiel 8 in the SBIKS2
Ezekiel 8 in the SBIMS
Ezekiel 8 in the SBIOS
Ezekiel 8 in the SBIPS
Ezekiel 8 in the SBISS
Ezekiel 8 in the SBITS
Ezekiel 8 in the SBITS2
Ezekiel 8 in the SBITS3
Ezekiel 8 in the SBITS4
Ezekiel 8 in the SBIUS
Ezekiel 8 in the SBIVS
Ezekiel 8 in the SBT
Ezekiel 8 in the SBT1E
Ezekiel 8 in the SCHL
Ezekiel 8 in the SNT
Ezekiel 8 in the SUSU
Ezekiel 8 in the SUSU2
Ezekiel 8 in the SYNO
Ezekiel 8 in the TBIAOTANT
Ezekiel 8 in the TBT1E
Ezekiel 8 in the TBT1E2
Ezekiel 8 in the TFTIP
Ezekiel 8 in the TFTU
Ezekiel 8 in the TGNTATF3T
Ezekiel 8 in the THAI
Ezekiel 8 in the TNFD
Ezekiel 8 in the TNT
Ezekiel 8 in the TNTIK
Ezekiel 8 in the TNTIL
Ezekiel 8 in the TNTIN
Ezekiel 8 in the TNTIP
Ezekiel 8 in the TNTIZ
Ezekiel 8 in the TOMA
Ezekiel 8 in the TTENT
Ezekiel 8 in the UBG
Ezekiel 8 in the UGV
Ezekiel 8 in the UGV2
Ezekiel 8 in the UGV3
Ezekiel 8 in the VBL
Ezekiel 8 in the VDCC
Ezekiel 8 in the YALU
Ezekiel 8 in the YAPE
Ezekiel 8 in the YBVTP
Ezekiel 8 in the ZBP