Genesis 2 (BOGWICC)

1 Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo. 2 Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. 3 Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira. 4 Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba, 5 zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka, 6 koma kasupe ankatuluka mʼnthaka ndi kuthirira pa dziko lonse. 7 Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. 8 Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. 9 Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa. 10 Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi. 11 Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. 12 (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). 13 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. 14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. 15 Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira. 16 Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu; 17 koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.” 18 Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.” 19 Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. 20 Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse.Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. 21 Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. 22 Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye. 23 Munthu uja anati,“Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa angandi mnofu wochokera ku mnofu wanga;adzatchedwa ‘mkazi,’popeza wachokera mwa mwamuna.” 24 Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi. 25 Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.

In Other Versions

Genesis 2 in the ANGEFD

Genesis 2 in the ANTPNG2D

Genesis 2 in the AS21

Genesis 2 in the BAGH

Genesis 2 in the BBPNG

Genesis 2 in the BBT1E

Genesis 2 in the BDS

Genesis 2 in the BEV

Genesis 2 in the BHAD

Genesis 2 in the BIB

Genesis 2 in the BLPT

Genesis 2 in the BNT

Genesis 2 in the BNTABOOT

Genesis 2 in the BNTLV

Genesis 2 in the BOATCB

Genesis 2 in the BOATCB2

Genesis 2 in the BOBCV

Genesis 2 in the BOCNT

Genesis 2 in the BOECS

Genesis 2 in the BOHCB

Genesis 2 in the BOHCV

Genesis 2 in the BOHLNT

Genesis 2 in the BOHNTLTAL

Genesis 2 in the BOICB

Genesis 2 in the BOILNTAP

Genesis 2 in the BOITCV

Genesis 2 in the BOKCV

Genesis 2 in the BOKCV2

Genesis 2 in the BOKHWOG

Genesis 2 in the BOKSSV

Genesis 2 in the BOLCB

Genesis 2 in the BOLCB2

Genesis 2 in the BOMCV

Genesis 2 in the BONAV

Genesis 2 in the BONCB

Genesis 2 in the BONLT

Genesis 2 in the BONUT2

Genesis 2 in the BOPLNT

Genesis 2 in the BOSCB

Genesis 2 in the BOSNC

Genesis 2 in the BOTLNT

Genesis 2 in the BOVCB

Genesis 2 in the BOYCB

Genesis 2 in the BPBB

Genesis 2 in the BPH

Genesis 2 in the BSB

Genesis 2 in the CCB

Genesis 2 in the CUV

Genesis 2 in the CUVS

Genesis 2 in the DBT

Genesis 2 in the DGDNT

Genesis 2 in the DHNT

Genesis 2 in the DNT

Genesis 2 in the ELBE

Genesis 2 in the EMTV

Genesis 2 in the ESV

Genesis 2 in the FBV

Genesis 2 in the FEB

Genesis 2 in the GGMNT

Genesis 2 in the GNT

Genesis 2 in the HARY

Genesis 2 in the HNT

Genesis 2 in the IRVA

Genesis 2 in the IRVB

Genesis 2 in the IRVG

Genesis 2 in the IRVH

Genesis 2 in the IRVK

Genesis 2 in the IRVM

Genesis 2 in the IRVM2

Genesis 2 in the IRVO

Genesis 2 in the IRVP

Genesis 2 in the IRVT

Genesis 2 in the IRVT2

Genesis 2 in the IRVU

Genesis 2 in the ISVN

Genesis 2 in the JSNT

Genesis 2 in the KAPI

Genesis 2 in the KBT1ETNIK

Genesis 2 in the KBV

Genesis 2 in the KJV

Genesis 2 in the KNFD

Genesis 2 in the LBA

Genesis 2 in the LBLA

Genesis 2 in the LNT

Genesis 2 in the LSV

Genesis 2 in the MAAL

Genesis 2 in the MBV

Genesis 2 in the MBV2

Genesis 2 in the MHNT

Genesis 2 in the MKNFD

Genesis 2 in the MNG

Genesis 2 in the MNT

Genesis 2 in the MNT2

Genesis 2 in the MRS1T

Genesis 2 in the NAA

Genesis 2 in the NASB

Genesis 2 in the NBLA

Genesis 2 in the NBS

Genesis 2 in the NBVTP

Genesis 2 in the NET2

Genesis 2 in the NIV11

Genesis 2 in the NNT

Genesis 2 in the NNT2

Genesis 2 in the NNT3

Genesis 2 in the PDDPT

Genesis 2 in the PFNT

Genesis 2 in the RMNT

Genesis 2 in the SBIAS

Genesis 2 in the SBIBS

Genesis 2 in the SBIBS2

Genesis 2 in the SBICS

Genesis 2 in the SBIDS

Genesis 2 in the SBIGS

Genesis 2 in the SBIHS

Genesis 2 in the SBIIS

Genesis 2 in the SBIIS2

Genesis 2 in the SBIIS3

Genesis 2 in the SBIKS

Genesis 2 in the SBIKS2

Genesis 2 in the SBIMS

Genesis 2 in the SBIOS

Genesis 2 in the SBIPS

Genesis 2 in the SBISS

Genesis 2 in the SBITS

Genesis 2 in the SBITS2

Genesis 2 in the SBITS3

Genesis 2 in the SBITS4

Genesis 2 in the SBIUS

Genesis 2 in the SBIVS

Genesis 2 in the SBT

Genesis 2 in the SBT1E

Genesis 2 in the SCHL

Genesis 2 in the SNT

Genesis 2 in the SUSU

Genesis 2 in the SUSU2

Genesis 2 in the SYNO

Genesis 2 in the TBIAOTANT

Genesis 2 in the TBT1E

Genesis 2 in the TBT1E2

Genesis 2 in the TFTIP

Genesis 2 in the TFTU

Genesis 2 in the TGNTATF3T

Genesis 2 in the THAI

Genesis 2 in the TNFD

Genesis 2 in the TNT

Genesis 2 in the TNTIK

Genesis 2 in the TNTIL

Genesis 2 in the TNTIN

Genesis 2 in the TNTIP

Genesis 2 in the TNTIZ

Genesis 2 in the TOMA

Genesis 2 in the TTENT

Genesis 2 in the UBG

Genesis 2 in the UGV

Genesis 2 in the UGV2

Genesis 2 in the UGV3

Genesis 2 in the VBL

Genesis 2 in the VDCC

Genesis 2 in the YALU

Genesis 2 in the YAPE

Genesis 2 in the YBVTP

Genesis 2 in the ZBP