Genesis 22 (BOGWICC)
1 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!”Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” 2 Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.” 3 Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. 4 Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. 5 Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.” 6 Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, 7 Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?”Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.”Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?” 8 Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo. 9 Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. 10 Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. 11 Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!”Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” 12 Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” 13 Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.” 15 Mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba kachiwiri 16 ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu, 17 ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, 18 ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.” 19 Kenaka Abrahamu anabwerera kumene anasiya antchito ake kuja nanyamukira nawo pamodzi kupita ku Beeriseba. Ndipo Abrahamu anakhala ku Beeriseba. 20 Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. 21 Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. 22 Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” 23 Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa. 24 Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.
In Other Versions
Genesis 22 in the ANGEFD
Genesis 22 in the ANTPNG2D
Genesis 22 in the AS21
Genesis 22 in the BAGH
Genesis 22 in the BBPNG
Genesis 22 in the BBT1E
Genesis 22 in the BDS
Genesis 22 in the BEV
Genesis 22 in the BHAD
Genesis 22 in the BIB
Genesis 22 in the BLPT
Genesis 22 in the BNT
Genesis 22 in the BNTABOOT
Genesis 22 in the BNTLV
Genesis 22 in the BOATCB
Genesis 22 in the BOATCB2
Genesis 22 in the BOBCV
Genesis 22 in the BOCNT
Genesis 22 in the BOECS
Genesis 22 in the BOHCB
Genesis 22 in the BOHCV
Genesis 22 in the BOHLNT
Genesis 22 in the BOHNTLTAL
Genesis 22 in the BOICB
Genesis 22 in the BOILNTAP
Genesis 22 in the BOITCV
Genesis 22 in the BOKCV
Genesis 22 in the BOKCV2
Genesis 22 in the BOKHWOG
Genesis 22 in the BOKSSV
Genesis 22 in the BOLCB
Genesis 22 in the BOLCB2
Genesis 22 in the BOMCV
Genesis 22 in the BONAV
Genesis 22 in the BONCB
Genesis 22 in the BONLT
Genesis 22 in the BONUT2
Genesis 22 in the BOPLNT
Genesis 22 in the BOSCB
Genesis 22 in the BOSNC
Genesis 22 in the BOTLNT
Genesis 22 in the BOVCB
Genesis 22 in the BOYCB
Genesis 22 in the BPBB
Genesis 22 in the BPH
Genesis 22 in the BSB
Genesis 22 in the CCB
Genesis 22 in the CUV
Genesis 22 in the CUVS
Genesis 22 in the DBT
Genesis 22 in the DGDNT
Genesis 22 in the DHNT
Genesis 22 in the DNT
Genesis 22 in the ELBE
Genesis 22 in the EMTV
Genesis 22 in the ESV
Genesis 22 in the FBV
Genesis 22 in the FEB
Genesis 22 in the GGMNT
Genesis 22 in the GNT
Genesis 22 in the HARY
Genesis 22 in the HNT
Genesis 22 in the IRVA
Genesis 22 in the IRVB
Genesis 22 in the IRVG
Genesis 22 in the IRVH
Genesis 22 in the IRVK
Genesis 22 in the IRVM
Genesis 22 in the IRVM2
Genesis 22 in the IRVO
Genesis 22 in the IRVP
Genesis 22 in the IRVT
Genesis 22 in the IRVT2
Genesis 22 in the IRVU
Genesis 22 in the ISVN
Genesis 22 in the JSNT
Genesis 22 in the KAPI
Genesis 22 in the KBT1ETNIK
Genesis 22 in the KBV
Genesis 22 in the KJV
Genesis 22 in the KNFD
Genesis 22 in the LBA
Genesis 22 in the LBLA
Genesis 22 in the LNT
Genesis 22 in the LSV
Genesis 22 in the MAAL
Genesis 22 in the MBV
Genesis 22 in the MBV2
Genesis 22 in the MHNT
Genesis 22 in the MKNFD
Genesis 22 in the MNG
Genesis 22 in the MNT
Genesis 22 in the MNT2
Genesis 22 in the MRS1T
Genesis 22 in the NAA
Genesis 22 in the NASB
Genesis 22 in the NBLA
Genesis 22 in the NBS
Genesis 22 in the NBVTP
Genesis 22 in the NET2
Genesis 22 in the NIV11
Genesis 22 in the NNT
Genesis 22 in the NNT2
Genesis 22 in the NNT3
Genesis 22 in the PDDPT
Genesis 22 in the PFNT
Genesis 22 in the RMNT
Genesis 22 in the SBIAS
Genesis 22 in the SBIBS
Genesis 22 in the SBIBS2
Genesis 22 in the SBICS
Genesis 22 in the SBIDS
Genesis 22 in the SBIGS
Genesis 22 in the SBIHS
Genesis 22 in the SBIIS
Genesis 22 in the SBIIS2
Genesis 22 in the SBIIS3
Genesis 22 in the SBIKS
Genesis 22 in the SBIKS2
Genesis 22 in the SBIMS
Genesis 22 in the SBIOS
Genesis 22 in the SBIPS
Genesis 22 in the SBISS
Genesis 22 in the SBITS
Genesis 22 in the SBITS2
Genesis 22 in the SBITS3
Genesis 22 in the SBITS4
Genesis 22 in the SBIUS
Genesis 22 in the SBIVS
Genesis 22 in the SBT
Genesis 22 in the SBT1E
Genesis 22 in the SCHL
Genesis 22 in the SNT
Genesis 22 in the SUSU
Genesis 22 in the SUSU2
Genesis 22 in the SYNO
Genesis 22 in the TBIAOTANT
Genesis 22 in the TBT1E
Genesis 22 in the TBT1E2
Genesis 22 in the TFTIP
Genesis 22 in the TFTU
Genesis 22 in the TGNTATF3T
Genesis 22 in the THAI
Genesis 22 in the TNFD
Genesis 22 in the TNT
Genesis 22 in the TNTIK
Genesis 22 in the TNTIL
Genesis 22 in the TNTIN
Genesis 22 in the TNTIP
Genesis 22 in the TNTIZ
Genesis 22 in the TOMA
Genesis 22 in the TTENT
Genesis 22 in the UBG
Genesis 22 in the UGV
Genesis 22 in the UGV2
Genesis 22 in the UGV3
Genesis 22 in the VBL
Genesis 22 in the VDCC
Genesis 22 in the YALU
Genesis 22 in the YAPE
Genesis 22 in the YBVTP
Genesis 22 in the ZBP