Genesis 28 (BOGWICC)
1 Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani. 2 Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. 3 Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu. 4 Mulunguyo akudalitse iwe monga mmene anamudalitsira Abrahamu kuti zidzukulu zako zidzalandira dziko limene ukukhalamo ngati mlendo kuti lidzakhale lawo. Ili ndi dziko limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu.” 5 Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau. 6 Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.” 7 Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu. 8 Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani; 9 anapita kwa Ismaeli mwana wa Abrahamu nakwatira Mahalati mwana wa Ismaeli, mlongo wake wa Nebayoti. Anatero kuwonjezera akazi amene anali nawo kale. 10 Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani. 11 Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona. 12 Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo. 13 Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo. 14 Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. 15 Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.” 16 Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.” 17 Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.” 18 Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake 19 Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi. 20 Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; 21 ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga, 22 ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”
In Other Versions
Genesis 28 in the ANGEFD
Genesis 28 in the ANTPNG2D
Genesis 28 in the AS21
Genesis 28 in the BAGH
Genesis 28 in the BBPNG
Genesis 28 in the BBT1E
Genesis 28 in the BDS
Genesis 28 in the BEV
Genesis 28 in the BHAD
Genesis 28 in the BIB
Genesis 28 in the BLPT
Genesis 28 in the BNT
Genesis 28 in the BNTABOOT
Genesis 28 in the BNTLV
Genesis 28 in the BOATCB
Genesis 28 in the BOATCB2
Genesis 28 in the BOBCV
Genesis 28 in the BOCNT
Genesis 28 in the BOECS
Genesis 28 in the BOHCB
Genesis 28 in the BOHCV
Genesis 28 in the BOHLNT
Genesis 28 in the BOHNTLTAL
Genesis 28 in the BOICB
Genesis 28 in the BOILNTAP
Genesis 28 in the BOITCV
Genesis 28 in the BOKCV
Genesis 28 in the BOKCV2
Genesis 28 in the BOKHWOG
Genesis 28 in the BOKSSV
Genesis 28 in the BOLCB
Genesis 28 in the BOLCB2
Genesis 28 in the BOMCV
Genesis 28 in the BONAV
Genesis 28 in the BONCB
Genesis 28 in the BONLT
Genesis 28 in the BONUT2
Genesis 28 in the BOPLNT
Genesis 28 in the BOSCB
Genesis 28 in the BOSNC
Genesis 28 in the BOTLNT
Genesis 28 in the BOVCB
Genesis 28 in the BOYCB
Genesis 28 in the BPBB
Genesis 28 in the BPH
Genesis 28 in the BSB
Genesis 28 in the CCB
Genesis 28 in the CUV
Genesis 28 in the CUVS
Genesis 28 in the DBT
Genesis 28 in the DGDNT
Genesis 28 in the DHNT
Genesis 28 in the DNT
Genesis 28 in the ELBE
Genesis 28 in the EMTV
Genesis 28 in the ESV
Genesis 28 in the FBV
Genesis 28 in the FEB
Genesis 28 in the GGMNT
Genesis 28 in the GNT
Genesis 28 in the HARY
Genesis 28 in the HNT
Genesis 28 in the IRVA
Genesis 28 in the IRVB
Genesis 28 in the IRVG
Genesis 28 in the IRVH
Genesis 28 in the IRVK
Genesis 28 in the IRVM
Genesis 28 in the IRVM2
Genesis 28 in the IRVO
Genesis 28 in the IRVP
Genesis 28 in the IRVT
Genesis 28 in the IRVT2
Genesis 28 in the IRVU
Genesis 28 in the ISVN
Genesis 28 in the JSNT
Genesis 28 in the KAPI
Genesis 28 in the KBT1ETNIK
Genesis 28 in the KBV
Genesis 28 in the KJV
Genesis 28 in the KNFD
Genesis 28 in the LBA
Genesis 28 in the LBLA
Genesis 28 in the LNT
Genesis 28 in the LSV
Genesis 28 in the MAAL
Genesis 28 in the MBV
Genesis 28 in the MBV2
Genesis 28 in the MHNT
Genesis 28 in the MKNFD
Genesis 28 in the MNG
Genesis 28 in the MNT
Genesis 28 in the MNT2
Genesis 28 in the MRS1T
Genesis 28 in the NAA
Genesis 28 in the NASB
Genesis 28 in the NBLA
Genesis 28 in the NBS
Genesis 28 in the NBVTP
Genesis 28 in the NET2
Genesis 28 in the NIV11
Genesis 28 in the NNT
Genesis 28 in the NNT2
Genesis 28 in the NNT3
Genesis 28 in the PDDPT
Genesis 28 in the PFNT
Genesis 28 in the RMNT
Genesis 28 in the SBIAS
Genesis 28 in the SBIBS
Genesis 28 in the SBIBS2
Genesis 28 in the SBICS
Genesis 28 in the SBIDS
Genesis 28 in the SBIGS
Genesis 28 in the SBIHS
Genesis 28 in the SBIIS
Genesis 28 in the SBIIS2
Genesis 28 in the SBIIS3
Genesis 28 in the SBIKS
Genesis 28 in the SBIKS2
Genesis 28 in the SBIMS
Genesis 28 in the SBIOS
Genesis 28 in the SBIPS
Genesis 28 in the SBISS
Genesis 28 in the SBITS
Genesis 28 in the SBITS2
Genesis 28 in the SBITS3
Genesis 28 in the SBITS4
Genesis 28 in the SBIUS
Genesis 28 in the SBIVS
Genesis 28 in the SBT
Genesis 28 in the SBT1E
Genesis 28 in the SCHL
Genesis 28 in the SNT
Genesis 28 in the SUSU
Genesis 28 in the SUSU2
Genesis 28 in the SYNO
Genesis 28 in the TBIAOTANT
Genesis 28 in the TBT1E
Genesis 28 in the TBT1E2
Genesis 28 in the TFTIP
Genesis 28 in the TFTU
Genesis 28 in the TGNTATF3T
Genesis 28 in the THAI
Genesis 28 in the TNFD
Genesis 28 in the TNT
Genesis 28 in the TNTIK
Genesis 28 in the TNTIL
Genesis 28 in the TNTIN
Genesis 28 in the TNTIP
Genesis 28 in the TNTIZ
Genesis 28 in the TOMA
Genesis 28 in the TTENT
Genesis 28 in the UBG
Genesis 28 in the UGV
Genesis 28 in the UGV2
Genesis 28 in the UGV3
Genesis 28 in the VBL
Genesis 28 in the VDCC
Genesis 28 in the YALU
Genesis 28 in the YAPE
Genesis 28 in the YBVTP
Genesis 28 in the ZBP