Genesis 35 (BOGWICC)

1 Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.” 2 Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu. 3 Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” 4 Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu. 5 Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo. 6 Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani. 7 Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake. 8 Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro). 9 Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa. 10 Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli. 11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu. 12 Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.” 13 Kenaka Mulungu anamusiya Yakobo. 14 Yakobo anayika mwala wachikumbutso pa malo pamene Mulungu anayankhula naye paja. Iye anathirapo nsembe yachakumwa ndi yamafuta. 15 Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli. 16 Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka. 17 Akanali chivutikire choncho, mzamba anamulimbikitsa nati, “Usaope pakuti ubala mwana wina wamwamuna.” 18 Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini. 19 Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu). 20 Pa manda ake, Yakobo anayimika mwala wachikumbutso wa pa manda ndipo ulipobe mpaka lero. 21 Israeli (Yakobo) anasunthanso nakamanga tenti yake kupitirira nsanja ya Ederi. 22 Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri: 23 Ana a Leya ndi awa:Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo,Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni. 24 Ana a Rakele ndi awa:Yosefe ndi Benjamini. 25 Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa:Dani ndi Nafutali. 26 Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa:Gadi ndi Aseri.Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu. 27 Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale. 28 Isake anakhala ndi moyo zaka 180. 29 Anamwalira ali wokalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ndipo ana ake Esau ndi Yakobo anamuyika mʼmanda.

In Other Versions

Genesis 35 in the ANGEFD

Genesis 35 in the ANTPNG2D

Genesis 35 in the AS21

Genesis 35 in the BAGH

Genesis 35 in the BBPNG

Genesis 35 in the BBT1E

Genesis 35 in the BDS

Genesis 35 in the BEV

Genesis 35 in the BHAD

Genesis 35 in the BIB

Genesis 35 in the BLPT

Genesis 35 in the BNT

Genesis 35 in the BNTABOOT

Genesis 35 in the BNTLV

Genesis 35 in the BOATCB

Genesis 35 in the BOATCB2

Genesis 35 in the BOBCV

Genesis 35 in the BOCNT

Genesis 35 in the BOECS

Genesis 35 in the BOHCB

Genesis 35 in the BOHCV

Genesis 35 in the BOHLNT

Genesis 35 in the BOHNTLTAL

Genesis 35 in the BOICB

Genesis 35 in the BOILNTAP

Genesis 35 in the BOITCV

Genesis 35 in the BOKCV

Genesis 35 in the BOKCV2

Genesis 35 in the BOKHWOG

Genesis 35 in the BOKSSV

Genesis 35 in the BOLCB

Genesis 35 in the BOLCB2

Genesis 35 in the BOMCV

Genesis 35 in the BONAV

Genesis 35 in the BONCB

Genesis 35 in the BONLT

Genesis 35 in the BONUT2

Genesis 35 in the BOPLNT

Genesis 35 in the BOSCB

Genesis 35 in the BOSNC

Genesis 35 in the BOTLNT

Genesis 35 in the BOVCB

Genesis 35 in the BOYCB

Genesis 35 in the BPBB

Genesis 35 in the BPH

Genesis 35 in the BSB

Genesis 35 in the CCB

Genesis 35 in the CUV

Genesis 35 in the CUVS

Genesis 35 in the DBT

Genesis 35 in the DGDNT

Genesis 35 in the DHNT

Genesis 35 in the DNT

Genesis 35 in the ELBE

Genesis 35 in the EMTV

Genesis 35 in the ESV

Genesis 35 in the FBV

Genesis 35 in the FEB

Genesis 35 in the GGMNT

Genesis 35 in the GNT

Genesis 35 in the HARY

Genesis 35 in the HNT

Genesis 35 in the IRVA

Genesis 35 in the IRVB

Genesis 35 in the IRVG

Genesis 35 in the IRVH

Genesis 35 in the IRVK

Genesis 35 in the IRVM

Genesis 35 in the IRVM2

Genesis 35 in the IRVO

Genesis 35 in the IRVP

Genesis 35 in the IRVT

Genesis 35 in the IRVT2

Genesis 35 in the IRVU

Genesis 35 in the ISVN

Genesis 35 in the JSNT

Genesis 35 in the KAPI

Genesis 35 in the KBT1ETNIK

Genesis 35 in the KBV

Genesis 35 in the KJV

Genesis 35 in the KNFD

Genesis 35 in the LBA

Genesis 35 in the LBLA

Genesis 35 in the LNT

Genesis 35 in the LSV

Genesis 35 in the MAAL

Genesis 35 in the MBV

Genesis 35 in the MBV2

Genesis 35 in the MHNT

Genesis 35 in the MKNFD

Genesis 35 in the MNG

Genesis 35 in the MNT

Genesis 35 in the MNT2

Genesis 35 in the MRS1T

Genesis 35 in the NAA

Genesis 35 in the NASB

Genesis 35 in the NBLA

Genesis 35 in the NBS

Genesis 35 in the NBVTP

Genesis 35 in the NET2

Genesis 35 in the NIV11

Genesis 35 in the NNT

Genesis 35 in the NNT2

Genesis 35 in the NNT3

Genesis 35 in the PDDPT

Genesis 35 in the PFNT

Genesis 35 in the RMNT

Genesis 35 in the SBIAS

Genesis 35 in the SBIBS

Genesis 35 in the SBIBS2

Genesis 35 in the SBICS

Genesis 35 in the SBIDS

Genesis 35 in the SBIGS

Genesis 35 in the SBIHS

Genesis 35 in the SBIIS

Genesis 35 in the SBIIS2

Genesis 35 in the SBIIS3

Genesis 35 in the SBIKS

Genesis 35 in the SBIKS2

Genesis 35 in the SBIMS

Genesis 35 in the SBIOS

Genesis 35 in the SBIPS

Genesis 35 in the SBISS

Genesis 35 in the SBITS

Genesis 35 in the SBITS2

Genesis 35 in the SBITS3

Genesis 35 in the SBITS4

Genesis 35 in the SBIUS

Genesis 35 in the SBIVS

Genesis 35 in the SBT

Genesis 35 in the SBT1E

Genesis 35 in the SCHL

Genesis 35 in the SNT

Genesis 35 in the SUSU

Genesis 35 in the SUSU2

Genesis 35 in the SYNO

Genesis 35 in the TBIAOTANT

Genesis 35 in the TBT1E

Genesis 35 in the TBT1E2

Genesis 35 in the TFTIP

Genesis 35 in the TFTU

Genesis 35 in the TGNTATF3T

Genesis 35 in the THAI

Genesis 35 in the TNFD

Genesis 35 in the TNT

Genesis 35 in the TNTIK

Genesis 35 in the TNTIL

Genesis 35 in the TNTIN

Genesis 35 in the TNTIP

Genesis 35 in the TNTIZ

Genesis 35 in the TOMA

Genesis 35 in the TTENT

Genesis 35 in the UBG

Genesis 35 in the UGV

Genesis 35 in the UGV2

Genesis 35 in the UGV3

Genesis 35 in the VBL

Genesis 35 in the VDCC

Genesis 35 in the YALU

Genesis 35 in the YAPE

Genesis 35 in the YBVTP

Genesis 35 in the ZBP