Genesis 6 (BOGWICC)
1 Anthu atayamba kuchuluka pa dziko lapansi ndi kubereka ana aakazi, 2 ana aamuna a Mulungu anaona kuti ana aakazi a anthuwo anali okongola. Ndipo anakwatira aliyense amene anamusankha. 3 Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” 4 Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu. 5 Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha, 6 Yehova anamva chisoni kuti analenga munthu ndi kumuyika pa dziko lapansi, ndipo anawawidwa mtima. 7 Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.” 8 Koma Yehova anamukomera mtima Nowa. 9 Mbiri ya Nowa inali yotere: Nowa anali munthu wolungama ndi wopanda tchimo pakati pa anthu a mʼbado wake. Ndipo anayenda ndi Mulungu. 10 Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. 11 Chiwawa chinadzaza pa dziko lapansi kotero kuti dziko linakhala lowonongeka pamaso pa Mulungu. 12 Mulungu atayangʼana, anaona kuti dziko layipadi chifukwa cha makhalidwe oyipa a anthu onse pa dziko lapansi. 13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, “Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko. 14 Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. 15 Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. 16 Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba. 17 Ndidzagwetsa mvula ya chigumula pa dziko lapansi kuti ndiwononge zamoyo zonse za pansi pa thambo ndipo chilichonse cha pa dziko lapansi chidzafa. 18 Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho. 19 Iwe udzalowa mʼchombocho ndi zolengedwa zamoyo zonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike ndi moyo pamodzi ndi iwe. 20 Udzatenga ziwiriziwiri za mitundu yonse ya mbalame, mitundu yonse ya nyama, ndi mitundu yonse ya zokwawa kuti zikhale ndi moyo. 21 Udzatengenso chakudya cha mtundu uliwonse ndi kuchisunga kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.” 22 Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira.
In Other Versions
Genesis 6 in the ANGEFD
Genesis 6 in the ANTPNG2D
Genesis 6 in the AS21
Genesis 6 in the BAGH
Genesis 6 in the BBPNG
Genesis 6 in the BBT1E
Genesis 6 in the BDS
Genesis 6 in the BEV
Genesis 6 in the BHAD
Genesis 6 in the BIB
Genesis 6 in the BLPT
Genesis 6 in the BNT
Genesis 6 in the BNTABOOT
Genesis 6 in the BNTLV
Genesis 6 in the BOATCB
Genesis 6 in the BOATCB2
Genesis 6 in the BOBCV
Genesis 6 in the BOCNT
Genesis 6 in the BOECS
Genesis 6 in the BOHCB
Genesis 6 in the BOHCV
Genesis 6 in the BOHLNT
Genesis 6 in the BOHNTLTAL
Genesis 6 in the BOICB
Genesis 6 in the BOILNTAP
Genesis 6 in the BOITCV
Genesis 6 in the BOKCV
Genesis 6 in the BOKCV2
Genesis 6 in the BOKHWOG
Genesis 6 in the BOKSSV
Genesis 6 in the BOLCB
Genesis 6 in the BOLCB2
Genesis 6 in the BOMCV
Genesis 6 in the BONAV
Genesis 6 in the BONCB
Genesis 6 in the BONLT
Genesis 6 in the BONUT2
Genesis 6 in the BOPLNT
Genesis 6 in the BOSCB
Genesis 6 in the BOSNC
Genesis 6 in the BOTLNT
Genesis 6 in the BOVCB
Genesis 6 in the BOYCB
Genesis 6 in the BPBB
Genesis 6 in the BPH
Genesis 6 in the BSB
Genesis 6 in the CCB
Genesis 6 in the CUV
Genesis 6 in the CUVS
Genesis 6 in the DBT
Genesis 6 in the DGDNT
Genesis 6 in the DHNT
Genesis 6 in the DNT
Genesis 6 in the ELBE
Genesis 6 in the EMTV
Genesis 6 in the ESV
Genesis 6 in the FBV
Genesis 6 in the FEB
Genesis 6 in the GGMNT
Genesis 6 in the GNT
Genesis 6 in the HARY
Genesis 6 in the HNT
Genesis 6 in the IRVA
Genesis 6 in the IRVB
Genesis 6 in the IRVG
Genesis 6 in the IRVH
Genesis 6 in the IRVK
Genesis 6 in the IRVM
Genesis 6 in the IRVM2
Genesis 6 in the IRVO
Genesis 6 in the IRVP
Genesis 6 in the IRVT
Genesis 6 in the IRVT2
Genesis 6 in the IRVU
Genesis 6 in the ISVN
Genesis 6 in the JSNT
Genesis 6 in the KAPI
Genesis 6 in the KBT1ETNIK
Genesis 6 in the KBV
Genesis 6 in the KJV
Genesis 6 in the KNFD
Genesis 6 in the LBA
Genesis 6 in the LBLA
Genesis 6 in the LNT
Genesis 6 in the LSV
Genesis 6 in the MAAL
Genesis 6 in the MBV
Genesis 6 in the MBV2
Genesis 6 in the MHNT
Genesis 6 in the MKNFD
Genesis 6 in the MNG
Genesis 6 in the MNT
Genesis 6 in the MNT2
Genesis 6 in the MRS1T
Genesis 6 in the NAA
Genesis 6 in the NASB
Genesis 6 in the NBLA
Genesis 6 in the NBS
Genesis 6 in the NBVTP
Genesis 6 in the NET2
Genesis 6 in the NIV11
Genesis 6 in the NNT
Genesis 6 in the NNT2
Genesis 6 in the NNT3
Genesis 6 in the PDDPT
Genesis 6 in the PFNT
Genesis 6 in the RMNT
Genesis 6 in the SBIAS
Genesis 6 in the SBIBS
Genesis 6 in the SBIBS2
Genesis 6 in the SBICS
Genesis 6 in the SBIDS
Genesis 6 in the SBIGS
Genesis 6 in the SBIHS
Genesis 6 in the SBIIS
Genesis 6 in the SBIIS2
Genesis 6 in the SBIIS3
Genesis 6 in the SBIKS
Genesis 6 in the SBIKS2
Genesis 6 in the SBIMS
Genesis 6 in the SBIOS
Genesis 6 in the SBIPS
Genesis 6 in the SBISS
Genesis 6 in the SBITS
Genesis 6 in the SBITS2
Genesis 6 in the SBITS3
Genesis 6 in the SBITS4
Genesis 6 in the SBIUS
Genesis 6 in the SBIVS
Genesis 6 in the SBT
Genesis 6 in the SBT1E
Genesis 6 in the SCHL
Genesis 6 in the SNT
Genesis 6 in the SUSU
Genesis 6 in the SUSU2
Genesis 6 in the SYNO
Genesis 6 in the TBIAOTANT
Genesis 6 in the TBT1E
Genesis 6 in the TBT1E2
Genesis 6 in the TFTIP
Genesis 6 in the TFTU
Genesis 6 in the TGNTATF3T
Genesis 6 in the THAI
Genesis 6 in the TNFD
Genesis 6 in the TNT
Genesis 6 in the TNTIK
Genesis 6 in the TNTIL
Genesis 6 in the TNTIN
Genesis 6 in the TNTIP
Genesis 6 in the TNTIZ
Genesis 6 in the TOMA
Genesis 6 in the TTENT
Genesis 6 in the UBG
Genesis 6 in the UGV
Genesis 6 in the UGV2
Genesis 6 in the UGV3
Genesis 6 in the VBL
Genesis 6 in the VDCC
Genesis 6 in the YALU
Genesis 6 in the YAPE
Genesis 6 in the YBVTP
Genesis 6 in the ZBP